Masalimo 121
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.
121 Ndikweza maso anga ku mapiri;
kodi thandizo langa limachokera kuti?
2 Thandizo langa limachokera kwa Yehova,
wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.
3 Sadzalola kuti phazi lako literereke;
Iye amene amakusunga sadzawodzera.
4 Taonani, Iye amene amasunga Israeli
sadzawodzera kapena kugona.
5 Yehova ndiye amene amakusunga;
Yehova ndiye mthunzi wako ku dzanja lako lamanja.
6 Dzuwa silidzakupweteka nthawi ya masana,
kapena mwezi nthawi ya usiku.
7 Yehova adzakuteteza ku zoyipa zonse;
adzasunga moyo wako.
8 Yehova adzayangʼanira kutuluka kwako ndi kulowa kwako;
kuyambira tsopano mpaka muyaya.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.