Add parallel Print Page Options

Moyo Watsopano

Popeza kuti Khristu anamva zowawa mʼthupi lake, mukhale nawonso mtima omwewo, chifukwa iye amene wamva zowawa mʼthupi lake walekana nawo uchimo. Chifukwa cha ichi, iwo sakhalanso moyo wawo akuchita zofuna za matupi awo, koma amachita chifuniro cha Mulungu. Pakuti mwataya kale nthawi yambiri mʼmbuyomu pochita zimene anthu osapembedza amachita, moyo wokhumba zonyansa, zilakolako zoyipa kuledzera, zochitika zoyipa za pa phwando, mapokoso ndi kupembedza mafano onyansa. Anthu osapembedza amadabwa pamene simuthamangira nawo kuchita zoyipitsitsazi, nʼchifukwa chake amakuchitani chipongwe. Koma adzafotokoza okha mlandu wawo kwa Mulungu amene wakonzeka kuweruza amoyo ndi akufa. Pa chifukwa chimenechi, Uthenga Wabwino unalalikidwa ngakhale kwa iwo amene tsopano ndi akufa, kuti adzaweruzidwe monga anthu ku thupi, koma adzakhale ndi moyo monga mwa Mulungu mu mzimu.

Chimaliziro cha zinthu zonse chili pafupi. Choncho khalani maso ndi odziletsa kuti muthe kupemphera. Koposa zonse muzikondana wina ndi mnzake kwambiri, chifukwa chikondi chimaphimba machimo ambiri. Muzisamalirana wina ndi mnzake osamanyinyirika. 10 Aliyense agwiritse ntchito mokhulupirika mphatso iliyonse imene anayilandira potumikira ena ngati adindo ogwiritsa bwino ntchito mphatso za Mulungu za mitundumitundu. 11 Ngati wina ayankhula, ayankhuledi mawu enieni a Mulungu. Ngati wina atumikira, atumikire ndi mphamvu imene Mulungu amapereka, kuti pa zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu. Kwa Iye kukhale ulemerero ndi mphamvu mpaka muyaya, Ameni.

Kumva Zowawa Chifukwa cha Chikhristu

12 Abale okondedwa musadabwe ndi mayesero owawa amene mukukumana nawo ngati kuti china chake chachilendo chakuchitikirani. 13 Koma kondwerani popeza mukumva zowawa pamodzi ndi Khristu, kuti mudzakondwere kwakukulu pamene ulemerero wake udzaonekera. 14 Ngati akuchitani chipongwe chifukwa cha dzina la Khristu, ndinu odala, ndiye kuti Mzimu waulemerero wa Mulungu uli pa inu. 15 Ngati mumva zowawa, zisakhale chifukwa cha kupha munthu, kapena kuba, kapena kuchita choyipa, kapena kulowerera za anthu ena, 16 koma ngati mumva zowawa chifukwa ndinu Mkhristu, musachite manyazi, koma muyamike Mulungu chifukwa cha dzinalo. 17 Pakuti nthawi yafika kuti chiweruzo chiyambe mʼnyumba ya Mulungu, ndipo ngati chiyamba ndi ife nanga podzafika kwa osamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu, chidzakhala chotani? 18 Monga Malemba akuti,

“Ngati kuli kovuta kuti olungama apulumuke,
    nanga munthu wochimwa, wosasamala za Mulungu adzatani?”

19 Nʼchifukwa chake, iwo amene akumva zowawa monga mwa chifuniro cha Mulungu, adzipereke okha mʼmanja mwa Mlengi wawo wokhulupirika ndi kumapitiriza kuchita zabwino.

Living for God

Therefore, since Christ suffered in his body,(A) arm yourselves also with the same attitude, because whoever suffers in the body is done with sin.(B) As a result, they do not live the rest of their earthly lives for evil human desires,(C) but rather for the will of God. For you have spent enough time in the past(D) doing what pagans choose to do—living in debauchery, lust, drunkenness, orgies, carousing and detestable idolatry.(E) They are surprised that you do not join them in their reckless, wild living, and they heap abuse on you.(F) But they will have to give account to him who is ready to judge the living and the dead.(G) For this is the reason the gospel was preached even to those who are now dead,(H) so that they might be judged according to human standards in regard to the body, but live according to God in regard to the spirit.

The end of all things is near.(I) Therefore be alert and of sober mind(J) so that you may pray. Above all, love each other deeply,(K) because love covers over a multitude of sins.(L) Offer hospitality(M) to one another without grumbling.(N) 10 Each of you should use whatever gift you have received to serve others,(O) as faithful(P) stewards of God’s grace in its various forms. 11 If anyone speaks, they should do so as one who speaks the very words of God.(Q) If anyone serves, they should do so with the strength God provides,(R) so that in all things God may be praised(S) through Jesus Christ. To him be the glory and the power for ever and ever. Amen.(T)

Suffering for Being a Christian

12 Dear friends, do not be surprised at the fiery ordeal that has come on you(U) to test you, as though something strange were happening to you. 13 But rejoice(V) inasmuch as you participate in the sufferings of Christ,(W) so that you may be overjoyed when his glory is revealed.(X) 14 If you are insulted because of the name of Christ,(Y) you are blessed,(Z) for the Spirit of glory and of God rests on you. 15 If you suffer, it should not be as a murderer or thief or any other kind of criminal, or even as a meddler. 16 However, if you suffer as a Christian, do not be ashamed, but praise God that you bear that name.(AA) 17 For it is time for judgment to begin with God’s household;(AB) and if it begins with us, what will the outcome be for those who do not obey the gospel of God?(AC) 18 And,

“If it is hard for the righteous to be saved,
    what will become of the ungodly and the sinner?”[a](AD)

19 So then, those who suffer according to God’s will(AE) should commit themselves to their faithful Creator and continue to do good.

Footnotes

  1. 1 Peter 4:18 Prov. 11:31 (see Septuagint)