Add parallel Print Page Options

Samueli Adzudzula Sauli

13 Sauli analowa ufumu ali ndi zaka makumi atatu, ndipo analamulira Israeli kwa zaka 42.

Nthawi ina Sauli anasankha Aisraeli 3,000. Mwa iwowa, 2,000 anali ndi Sauliyo ku Mikimasi ndi ku dziko la mapiri ku Beteli, ndipo 1,000 anali ndi Yonatani ku Gibeya ku Benjamini. Anthu ena onse otsala anawabweza kwawo.

Yonatani anakantha mkulu wa ankhondo wa Afilisti ku Geba, ndipo Afilisti anamva kuti Aheberi awukira. Tsono Sauli anawuza amithenga kuti alize lipenga mʼdziko lonse la Israeli. Choncho Aisraeli onse anamva kuti Sauli wakantha mkulu wa ankhondo Wachifilisiti ndi kuti Afilisti anayipidwa nawo Aisraeli. Ndiye anthu anayitanidwa kuti abwere kwa Sauli ku Giligala.

Tsono Afilisti anasonkhana kuti amenyane ndi Aisraeli. Iwo anali ndi magaleta 3,000, okwera pa akavalo 2,000 ndiponso asilikali kuchuluka kwake ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja. Iwo anapita ndi kukamanga misasa yawo ku Mikimasi, kummawa kwa Beti-Aveni. Pamene Aisraeli anaona kuti anali pamavuto akulu, poti anali atapanikizidwa kwambiri, anabisala mʼmapanga, mʼmaenje, mʼmatanthwe, mʼmakwalala ndi mʼzitsime. Ahebri ena anawoloka Yorodani mpaka kukafika ku dziko la Gadi ndi ku Giliyadi.

Koma Sauli anakhalabe ku Giligala ndipo ankhondo onse amene anali naye anali njenjenje ndi mantha. Saulo anadikirira masiku asanu ndi awiri, monga mwa nthawi imene ananena Samueli. Koma Samueli sanabwere ku Giligala, ndipo anthu anayamba kumuthawa Sauli uja. Kotero iye anati, “Bwera nayoni nsembe yopsereza ndi nsembe ya chiyanjano.” Ndipo Sauli anapereka nsembe yopsereza. 10 Atangomaliza kupereka nsembe, anangoona Samueli watulukira ndipo Sauli anapita kukamulonjera.

11 Samueli anafunsa kuti, “Nʼchiyani chimene wachita?”

Sauli anayankha kuti, “Nditaona kuti anthu ayamba kundithawa, ndi kuti inu simunabwere pa nthawi munanena ija, ndiponso kuti Afilisti akusonkhana ku Mikimasi, 12 ndinati, ‘Tsopano Afilisti abwera kudzandithira nkhondo ku Giligala kuno, chonsecho sindinapemphe Yehova kuti andikomere mtima.’ Motero ndinakakamizika kupereka nsembe yopsereza.”

13 Samueli anati, “Mwachita zopusa. Simunatsate zimene Yehova Mulungu wanu anakulamulani kuti muchite. Mukanazitsata, Yehova akanawukhazikitsa ufumu wanu mu Israeli mpaka kalekale. 14 Koma tsopano ufumu wanu sudzakhalitsa. Yehova wapeza munthu wapamtima pake ndipo wamusankha kukhala mtsogoleri wa anthu ake chifukwa inu simunasunge malamulo a Yehova.”

15 Kenaka Samueli anachoka ku Giligala ndi kupita ku Gibeyati ku dziko la Benjamini. Saulo anawerenga anthu amene anali naye ndipo analipo 600.

Sauli Akonzekera Nkhondo

16 Sauli ndi mwana wake Yonatani pamodzi ndi asilikali amene anali naye aja amakhala ku Geba ku dziko la Benjamini. Koma Afilisti anamanga misasa yawo ku Mikimasi. 17 Ankhondo a Afilisti anatuluka mʼmisasa yawo mʼmagulu atatu. Gulu lina linapita ku Ofiri ku dziko la Suwala. 18 Gulu lina linalunjika ku Beti-Horoni, ndipo gulu lachitatu linalunjika ku malire oyangʼanana ndi chigwa cha Zeboimu cha ku chipululu.

19 Nthawi imeneyo nʼkuti mulibe osula zitsulo mʼdziko lonse la Israeli, pakuti Afilisti anati, “Tisawalole Aheberi kudzipangira okha malupanga kapena mikondo!” 20 Kotero Aisraeli onse amapita kwa Afilisti kukanoletsa mapulawo, makasu, nkhwangwa ndi zikwakwa zawo. 21 Mtengo wonolera mapulawo ndi makasu unali zigawo ziwiri za sekeli, mtengo wonolera zisonga ndi nkhwangwa unali gawo limodzi la Sekeli.

22 Motero tsiku la nkhondolo panalibe lupanga kapena mkondo mʼdzanja la aliyense amene anatsatira Saulo ndi Yonatani. Koma Saulo ndi Yonatani, iwo okha ndiwo anali ndi zida.

Yonatani Athira Nkhondo Afilisti

23 Tsono gulu lina lankhondo la Chifilisti linapita kukalonda mpata wa Mikimasi.

Samuel Rebukes Saul

13 Saul was thirty[a] years old when he became king, and he reigned over Israel forty-[b] two years.

Saul chose three thousand men from Israel; two thousand(A) were with him at Mikmash(B) and in the hill country of Bethel, and a thousand were with Jonathan at Gibeah(C) in Benjamin. The rest of the men he sent back to their homes.

Jonathan attacked the Philistine outpost(D) at Geba,(E) and the Philistines heard about it. Then Saul had the trumpet(F) blown throughout the land and said, “Let the Hebrews hear!” So all Israel heard the news: “Saul has attacked the Philistine outpost, and now Israel has become obnoxious(G) to the Philistines.” And the people were summoned to join Saul at Gilgal.

The Philistines assembled(H) to fight Israel, with three thousand[c] chariots, six thousand charioteers, and soldiers as numerous as the sand(I) on the seashore. They went up and camped at Mikmash,(J) east of Beth Aven.(K) When the Israelites saw that their situation was critical and that their army was hard pressed, they hid(L) in caves and thickets, among the rocks, and in pits and cisterns.(M) Some Hebrews even crossed the Jordan to the land of Gad(N) and Gilead.

Saul remained at Gilgal, and all the troops with him were quaking(O) with fear. He waited seven(P) days, the time set by Samuel; but Samuel did not come to Gilgal, and Saul’s men began to scatter. So he said, “Bring me the burnt offering and the fellowship offerings.” And Saul offered(Q) up the burnt offering. 10 Just as he finished making the offering, Samuel(R) arrived, and Saul went out to greet(S) him.

11 “What have you done?” asked Samuel.

Saul replied, “When I saw that the men were scattering, and that you did not come at the set time, and that the Philistines were assembling at Mikmash,(T) 12 I thought, ‘Now the Philistines will come down against me at Gilgal,(U) and I have not sought the Lord’s favor.(V)’ So I felt compelled to offer the burnt offering.”

13 “You have done a foolish thing,(W)” Samuel said. “You have not kept(X) the command the Lord your God gave you; if you had, he would have established your kingdom over Israel for all time.(Y) 14 But now your kingdom(Z) will not endure; the Lord has sought out a man after his own heart(AA) and appointed(AB) him ruler(AC) of his people, because you have not kept(AD) the Lord’s command.”

15 Then Samuel left Gilgal[d] and went up to Gibeah(AE) in Benjamin, and Saul counted the men who were with him. They numbered about six hundred.(AF)

Israel Without Weapons

16 Saul and his son Jonathan and the men with them were staying in Gibeah[e](AG) in Benjamin, while the Philistines camped at Mikmash. 17 Raiding(AH) parties went out from the Philistine camp in three detachments. One turned toward Ophrah(AI) in the vicinity of Shual, 18 another toward Beth Horon,(AJ) and the third toward the borderland overlooking the Valley of Zeboyim(AK) facing the wilderness.

19 Not a blacksmith(AL) could be found in the whole land of Israel, because the Philistines had said, “Otherwise the Hebrews will make swords or spears!(AM) 20 So all Israel went down to the Philistines to have their plow points, mattocks, axes and sickles[f] sharpened. 21 The price was two-thirds of a shekel[g] for sharpening plow points and mattocks, and a third of a shekel[h] for sharpening forks and axes and for repointing goads.

22 So on the day of the battle not a soldier with Saul and Jonathan(AN) had a sword or spear(AO) in his hand; only Saul and his son Jonathan had them.

Jonathan Attacks the Philistines

23 Now a detachment of Philistines had gone out to the pass(AP) at Mikmash.(AQ)

Footnotes

  1. 1 Samuel 13:1 A few late manuscripts of the Septuagint; Hebrew does not have thirty.
  2. 1 Samuel 13:1 Probable reading of the original Hebrew text (see Acts 13:21); Masoretic Text does not have forty-.
  3. 1 Samuel 13:5 Some Septuagint manuscripts and Syriac; Hebrew thirty thousand
  4. 1 Samuel 13:15 Hebrew; Septuagint Gilgal and went his way; the rest of the people went after Saul to meet the army, and they went out of Gilgal
  5. 1 Samuel 13:16 Two Hebrew manuscripts; most Hebrew manuscripts Geba, a variant of Gibeah
  6. 1 Samuel 13:20 Septuagint; Hebrew plow points
  7. 1 Samuel 13:21 That is, about 1/4 ounce or about 8 grams
  8. 1 Samuel 13:21 That is, about 1/8 ounce or about 4 grams