Add parallel Print Page Options

Bokosi la Chipangano Alibweretsa ku Yerusalemu

15 Davide atadzimangira nyumba zina mu Mzinda wa Davide, iye anakonza malo a Bokosi la Mulungu ndipo analimangira tenti. Pamenepo Davide anati, “Palibe wina ati anyamule Bokosi la Mulungu koma Alevi chifukwa Yehova anawasankha kuti azinyamula Bokosi la Yehova ndi kumatumikira pamaso pake nthawi zonse.”

Davide anasonkhanitsa Aisraeli onse mu Yerusalemu kuti abweretse Bokosi la Yehova ku malo amene analikonzera. Iye anayitanitsa pamodzi zidzukulu za Aaroni ndi Alevi:

kuchokera ku banja la Kohati,

mtsogoleri Urieli ndi abale ake 120.

Kuchokera ku banja la Merari,

mtsogoleri Asaya ndi abale ake 220;

kuchokera ku banja la Geresomu,

mtsogoleri Yoweli ndi abale ake 130;

kuchokera ku banja la Elizafani,

mtsogoleri Semaya ndi abale ake 200;

kuchokera ku banja la Hebroni,

mtsogoleri Elieli ndi abale ake 80;

10 kuchokera ku banja la Uzieli,

mtsogoleri Aminadabu ndi abale ake 112.

11 Kenaka Davide anayitanitsa ansembe Zadoki ndi Abiatara, ndi Alevi awa, Urieli, Asaya, Yoweli, Semaya, Elieli ndi Aminadabu. 12 Iye anawawuza kuti, “Inu ndinu atsogoleri a mabanja a Alevi ndipo inu ndi abale anu Alevi mudziyeretse nokha ndi kubweretsa Bokosi la Yehova Mulungu wa Israeli ku malo amene ine ndalikonzera. 13 Popeza kuti inu Alevi simunalinyamule poyamba paja, Yehova Mulungu wathu anatikantha. Sitinafunse momwe tikanachitira monga mmene Iyeyo anafotokozera.” 14 Kotero ansembe ndi Alevi anadziyeretsa ndi cholinga chakuti akatenge Bokosi la Yehova Mulungu wa Israeli. 15 Ndipo Alevi ananyamula Bokosi la Mulungu pa mapewa awo pa mitengo yake yonyamulira monga momwe Mose analamulira molingana ndi mawu a Yehova.

16 Davide anawuza atsogoleri a Alevi kuti asankhe abale awo kuti akhale oyimba nyimbo zachisangalalo, zoyimba ndi zida: azeze, apangwe ndi ziwaya za malipenga.

17 Kotero Alevi anasankha Hemani mwana wa Yoweli; ndipo mwa abale ake anasankha Asafu mwana wa Berekiya; ndipo mwa ana a Merari, abale awo, anasankha Etani mwana wa Kusaya; 18 ndipo pamodzi ndi iwowa abale awo otsatana nawo: Zekariya, Yaazieli, Semiramoti, Yehieli, Uni, Eliabu, Benaya, Maaseya, Matitiya, Elifelehu, Mikineya, Obedi-Edomu ndi Yeiyeli, alonda a pa chipata.

19 Anthu oyimba aja Hemani, Asafu ndi Etani ndiwo ankayimba ziwaya za malipenga zamkuwa; 20 Zekariya, Azieli, Semiramoti, Yehieli, Uni, Eliabu, Maaseya ndi Benaya ankayimba azeze a liwu lokwera; 21 ndipo Matitiya, Elifelehu, Mikineya, Obedi-Edomu, Yeiyeli ndi Azaziya ankayimba apangwe a liwu lotsika. 22 Kenaniya, mtsogoleri wa Alevi anali woyangʼanira mayimbidwe; uwu ndiye unali udindo wake pakuti anali waluso pa zimenezi.

23 Berekiya ndi Elikana anali olondera pa khomo la bokosilo. 24 Ansembe awa; Sebaniya, Yehosafati, Netaneli, Amasai, Zekariya, Benaya ndi Eliezara ndiwo ankayimba malipenga patsogolo pa Bokosi la Mulungu. Obedi-Edomu ndi Yehiya analinso alonda a pa khomo la bokosilo.

25 Choncho Davide pamodzi ndi akuluakulu a Israeli ndiponso asilikali olamulira magulu a anthu 1,000, anapita kukatenga Bokosi la Chipangano la Yehova ku nyumba ya Obedi-Edomu akukondwera. 26 Popeza Mulungu anathandiza Alevi amene ananyamula Bokosi la Chipangano la Yehova, anapereka nsembe ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri ndiponso nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri. 27 Ndipo Davide anali atavala mkanjo wa nsalu yofewa yosalala, monga anavalira Alevi onse amene ananyamula bokosi pamodzi anthu oyimba, ndiponso Kenaniya, amene anali woyangʼanira magulu oyimba. Davide anavalanso efodi ya nsalu yofewa yosalala. 28 Kotero Aisraeli onse anabweretsa Bokosi la Chipangano la Yehova ndi mfuwu, ndiponso akuyimba zitoliro zanyanga zankhosa zazimuna, malipenga ndi maseche ndiponso akuyimba azeze ndi apangwe.

29 Bokosi la Chipangano la Yehova likulowa mu Mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Sauli ankaona ali pa zenera. Ndipo ataona Mfumu Davide ikuvina ndi kukondwera, iye ananyoza Davideyo mu mtima mwake.