Add parallel Print Page Options

Mayi wa ku Sunemu Atenganso Munda wake

Ndipo Elisa anawuza mayi amene anamuukitsira mwana wake kuti, “Choka kuno pamodzi ndi banja lako ndipo ukakhale kulikonse ukufuna, chifukwa Yehova akubweretsa njala ya zaka zisanu ndi ziwiri mʼdziko muno.” Mayiyo ananyamuka nachita zimene munthu wa Mulungu ananena. Iye pamodzi ndi banja lake anachoka nakakhala ku dziko la Afilisti zaka zisanu ndi ziwiri.

Zitatha zaka zisanu ndi ziwirizo anabwera kuchokera ku dziko la Afilisti ndipo anapita kwa mfumu kukafunsa za nyumba yake ndi munda wake. Ndipo mfumu inkayankhula ndi Gehazi, mtumiki wa munthu wa Mulungu kuti, “Tandiwuza zinthu zikuluzikulu zimene Elisa wachita.” Pamene Gehazi ankayiwuza mfumuyo momwe Elisa anaukitsira anthu akufa, mayi amene mwana wake Elisa anamuukitsa kwa akufayo analowa kudzafunsa mfumu za nyumba yake ndi munda wake.

Gehazi anati, “Mbuye wanga mfumu, mayi wake ndi uyu ndipo mwana wakeyo ndi uyu amene Elisa anamuukitsa kwa akufa.” Mfumu inafunsa mayiyo za nkhaniyi ndipo iye anayifotokozera mfumuyo.

Ndipo mfumu inasankha munthu woti ayendetse nkhani yake ndipo inati, “Mubwezereni zonse zimene zinali zake, kuphatikizapo phindu lonse lochokera mʼmunda wake, kuyambira tsiku limene anachoka mpaka tsopano lino.”

Hazaeli Apha Beni-Hadadi

Elisa anapita ku Damasiko, ndipo Beni-Hadadi mfumu ya ku Aramu ankadwala. Mfumuyo itawuzidwa kuti, “Munthu wa Mulungu wabwera kuno kuchokera kutali,” inawuza Hazaeli kuti, “Tenga mphatso ndipo pita ukakumane ndi munthu wa Mulungu. Ukandifunsire kwa Yehova kudzera mwa iye kuti, ‘Kodi ndidzachira matenda angawa?’ ”

Choncho Hazaeli anapita kukakumana ndi Elisa, atasenzetsa ngamira 40 mphatso za zinthu zosiyanasiyana zabwino kwambiri za ku Damasiko. Iye analowa mʼnyumba ya Elisa ndi kuyima pamaso pake, ndipo anati, “Mwana wanu Beni-Hadadi wandituma kuti ndidzakufunseni kuti, ‘Kodi ndidzachira matenda angawa?’ ”

10 Elisa anayankha kuti, “Pita ndipo ukamuwuze kuti, ‘Udzachira ndithu,’ koma Yehova wandionetsa kuti adzafabe.” 11 Elisa anamuyangʼana kwambiri Hazaeli mpaka anachita manyazi. Pamenepo munthu wa Mulungu anayamba kulira.

12 Hazaeli anafunsa kuti, “Mbuye wanga mukulira chifukwa chiyani?”

Elisa anayankha kuti, “Chifukwa ndikudziwa choyipa chimene udzachitira Aisraeli. Udzatentha mizinda yawo ya chitetezo, udzapha anyamata awo ndi lupanga, udzaphwanyitsa pansi makanda awo ndiponso udzatumbula mimba za akazi awo oyembekezera.”

13 Ndipo Hazaeli anati, “Kodi kapolo wanune, amene ndine wonyozeka ngati galu, ndingathe bwanji kuchita chinthu chachikulu chotere?”

Elisa anayankha kuti, “Yehova wandionetsa kuti iwe udzakhala mfumu ya ku Aramu.”

14 Choncho Hazaeli anasiyana ndi Elisa ndi kubwerera kwa mbuye wake. Beni-Hadadi atafunsa kuti, “Elisa wakuwuza chiyani?” Hazaeli anayankha kuti, “Elisa wandiwuza kuti inu mudzachira ndithu.” 15 Koma mmawa mwake Hazaeli anatenga nsalu yokhuthala ndi kuyiviyika mʼmadzi ndipo anaphimba nayo nkhope ya mfumu, kotero mfumuyo inafa. Hazaeli analowa ufumu mʼmalo mwake.

Yehoramu Mfumu ya ku Yuda

16 Chaka chachisanu cha ufumu wa Yoramu mwana wa Ahabu mfumu ya ku Israeli, Yehosafati ali mfumu ya ku Yuda, Yehoramu mwana wake anakhala mfumu ya Ayuda. 17 Yehoramu analowa ufumu ali ndi zaka 32, ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka zisanu ndi zitatu. 18 Iye anatsatira khalidwe la mafumu a ku Israeli, monga mmene linachitira banja la Ahabu, popeza iye anakwatira mwana wa Ahabu. Yehoramu anachita zoyipa pamaso pa Yehova. 19 Komabe, chifukwa cha mtumiki wake Davide, Yehova sanafune kuwononga Yuda popeza Yehova analonjeza Davide kuti adzamupatsa nyale pamodzi ndi zidzukulu zake mpaka muyaya.

20 Pa nthawi ya Yehoramu, Edomu anawukira ulamuliro wa Yuda ndipo anadzisankhira mfumu. 21 Choncho Yehoramu anapita ku Zairi pamodzi ndi magaleta ake onse. Ndipo iye anakantha Aedomu amene anamuzungulira pamodzi ndi oyendetsa magaleta ake usiku. Koma ankhondo ake anathawa napita ku misasa yawo. 22 Mpaka lero lino Edomu ndi wowukira Yuda. Nthawi yomweyo mzinda wa Libina unawukiranso.

23 Ndipo ntchito zina za Yehoramu ndi zonse zomwe anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? 24 Choncho Yehoramu anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide. Ndipo Ahaziya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.

Ahaziya Mfumu ya ku Yuda

25 Mʼchaka cha khumi ndi chiwiri cha Yoramu mwana wa Ahabu mfumu ya Israeli, Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda anayamba kulamulira. 26 Ahaziya anali ndi zaka 22 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu chaka chimodzi. Amayi ake anali Ataliya, chidzukulu cha Omiri mfumu ya Israeli. 27 Iye anatsatira makhalidwe a banja la Ahabu ndipo anachita zoyipa pamaso pa Yehova, monga linachitira banja la Ahabu, pakuti anali mkamwini wa banja la Ahabu.

28 Ahaziya anapita pamodzi ndi Yoramu mwana wa Ahabu kukachita nkhondo ndi Hazaeli mfumu ya Aramu ku Ramoti Giliyadi. Aaramu anavulaza Yoramu. 29 Choncho mfumu Yoramu inabwerera ku Yezireeli kuti ikachire mabala ake amene Aaramu anamuvulaza ku Rama pa nkhondo yake ndi Hazaeli mfumu ya Aramu.

Tsono Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya ku Yuda anapita ku Yezireeli kuti akamuone Yoramu mwana wa Ahabu, popeza nʼkuti akudwala.

The Shunammite’s Land Restored

Now Elisha had said to the woman(A) whose son he had restored to life, “Go away with your family and stay for a while wherever you can, because the Lord has decreed a famine(B) in the land that will last seven years.”(C) The woman proceeded to do as the man of God said. She and her family went away and stayed in the land of the Philistines seven years.

At the end of the seven years she came back from the land of the Philistines and went to appeal to the king for her house and land. The king was talking to Gehazi, the servant of the man of God, and had said, “Tell me about all the great things Elisha has done.” Just as Gehazi was telling the king how Elisha had restored(D) the dead to life, the woman whose son Elisha had brought back to life came to appeal to the king for her house and land.

Gehazi said, “This is the woman, my lord the king, and this is her son whom Elisha restored to life.” The king asked the woman about it, and she told him.

Then he assigned an official to her case and said to him, “Give back everything that belonged to her, including all the income from her land from the day she left the country until now.”

Hazael Murders Ben-Hadad

Elisha went to Damascus,(E) and Ben-Hadad(F) king of Aram was ill. When the king was told, “The man of God has come all the way up here,” he said to Hazael,(G) “Take a gift(H) with you and go to meet the man of God. Consult(I) the Lord through him; ask him, ‘Will I recover from this illness?’”

Hazael went to meet Elisha, taking with him as a gift forty camel-loads of all the finest wares of Damascus. He went in and stood before him, and said, “Your son Ben-Hadad king of Aram has sent me to ask, ‘Will I recover from this illness?’”

10 Elisha answered, “Go and say to him, ‘You will certainly recover.’(J) Nevertheless,[a] the Lord has revealed to me that he will in fact die.” 11 He stared at him with a fixed gaze until Hazael was embarrassed.(K) Then the man of God began to weep.(L)

12 “Why is my lord weeping?” asked Hazael.

“Because I know the harm(M) you will do to the Israelites,” he answered. “You will set fire to their fortified places, kill their young men with the sword, dash(N) their little children(O) to the ground, and rip open(P) their pregnant women.”

13 Hazael said, “How could your servant, a mere dog,(Q) accomplish such a feat?”

“The Lord has shown me that you will become king(R) of Aram,” answered Elisha.

14 Then Hazael left Elisha and returned to his master. When Ben-Hadad asked, “What did Elisha say to you?” Hazael replied, “He told me that you would certainly recover.” 15 But the next day he took a thick cloth, soaked it in water and spread it over the king’s face, so that he died.(S) Then Hazael succeeded him as king.

Jehoram King of Judah(T)

16 In the fifth year of Joram(U) son of Ahab king of Israel, when Jehoshaphat was king of Judah, Jehoram(V) son of Jehoshaphat began his reign as king of Judah. 17 He was thirty-two years old when he became king, and he reigned in Jerusalem eight years. 18 He followed the ways of the kings of Israel, as the house of Ahab had done, for he married a daughter(W) of Ahab. He did evil in the eyes of the Lord. 19 Nevertheless, for the sake of his servant David, the Lord was not willing to destroy(X) Judah. He had promised to maintain a lamp(Y) for David and his descendants forever.

20 In the time of Jehoram, Edom rebelled against Judah and set up its own king.(Z) 21 So Jehoram[b] went to Zair with all his chariots. The Edomites surrounded him and his chariot commanders, but he rose up and broke through by night; his army, however, fled back home. 22 To this day Edom has been in rebellion(AA) against Judah. Libnah(AB) revolted at the same time.

23 As for the other events of Jehoram’s reign, and all he did, are they not written in the book of the annals of the kings of Judah? 24 Jehoram rested with his ancestors and was buried with them in the City of David. And Ahaziah his son succeeded him as king.

Ahaziah King of Judah(AC)

25 In the twelfth(AD) year of Joram son of Ahab king of Israel, Ahaziah son of Jehoram king of Judah began to reign. 26 Ahaziah was twenty-two years old when he became king, and he reigned in Jerusalem one year. His mother’s name was Athaliah,(AE) a granddaughter of Omri(AF) king of Israel. 27 He followed the ways of the house of Ahab(AG) and did evil(AH) in the eyes of the Lord, as the house of Ahab had done, for he was related by marriage to Ahab’s family.

28 Ahaziah went with Joram son of Ahab to war against Hazael king of Aram at Ramoth Gilead.(AI) The Arameans wounded Joram; 29 so King Joram returned to Jezreel(AJ) to recover from the wounds the Arameans had inflicted on him at Ramoth[c] in his battle with Hazael(AK) king of Aram.

Then Ahaziah(AL) son of Jehoram king of Judah went down to Jezreel to see Joram son of Ahab, because he had been wounded.

Footnotes

  1. 2 Kings 8:10 The Hebrew may also be read Go and say, ‘You will certainly not recover,’ for.
  2. 2 Kings 8:21 Hebrew Joram, a variant of Jehoram; also in verses 23 and 24
  3. 2 Kings 8:29 Hebrew Ramah, a variant of Ramoth