Add parallel Print Page Options

Yehu Adzozedwa Ufumu wa ku Israeli

Mneneri Elisa anayitanitsa mmodzi mwa ana a aneneri, namuwuza kuti, “Manga lamba mʼchiwuno mwako, tenga botolo la mafuta mʼdzanja lako ndipo upite ku Ramoti Giliyadi. Ukakafika kumeneko, ukafunefune Yehu mwana wa Yehosafati, mwana wa Nimisi. Ukapite kwa iye, ukamuchotse pakati pa anzake ndi kukamulowetsa mʼchipinda chamʼkati. Ndipo ukatenge botololi ndi kuthira mafuta pa mutu wake ndipo ukanene kuti, ‘Yehova akuti, Ine ndikudzoza iwe kukhala mfumu ya Israeli.’ Kenaka ukatsekule chitseko ndi kuthawa ndipo usakachedwe!”

Choncho mneneri wachinyamatayo anapita ku Ramoti Giliyadi. Atafika ku Giliyadiko anapeza atsogoleri a ankhondo ali pa msonkhano. Iye anati, “Mtsogoleri, ine ndili ndi uthenga wanu.”

Ndipo Yehu anafunsa kuti, “Uthengawo ndi wa yani pakati pathu?”

Mneneriyo anayankha kuti, “Ndi wa inuyo, mtsogoleri.”

Yehu anayimirira nakalowa mʼnyumba. Pamenepo mneneriyo anakhuthulira mafuta pamutu pa Yehu ndipo ananena kuti, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ine ndikukudzoza kukhala mfumu ya Israeli, anthu a Yehova. Uyenera kuwononga nyumba ya mbuye wako Ahabu ndipo ndidzabwezera imfa ya atumiki anga, aneneri ndiponso imfa ya atumiki ena onse a Yehova amene anaphedwa ndi Yezebeli. Banja lonse la Ahabu lidzatheratu. Ndidzachotsa munthu aliyense wamwamuna wa banja la Ahabu kaya ndi kapolo kapena mfulu. Ndidzachititsa kuti banja la Ahabu lifanane ndi banja la Yeroboamu mwana wa Nebati ndiponso ngati banja la Baasa mwana wa Ahiya. 10 Kunena za Yezebeli, agalu adzamudya ku dera la Yezireeli ndipo palibe amene adzamuyike mʼmanda.’ ” Kenaka mneneriyo anatsekula chitseko nʼkuthawa.

11 Yehu atatuluka kupita kumene kunali atsogoleri anzake, mmodzi mwa iwo anamufunsa kuti, “Kodi zonse zili bwino? Kodi munthu wamisala uja anabwera kudzatani kwa iwe?”

Yehu anayankha kuti, “Iwe ukumudziwa munthu uja ndiponso ukudziwa zomwe amayankhula.”

12 Atsogoleri aja anati, “Ukunama! Tiwuze.”

Yehu anati, “Zimene wandiwuza ndi izi: ‘Yehova akuti: Ine ndakudzoza iwe kukhala mfumu ya Israeli.’ ”

13 Atsogoleri aja mofulumira anatenga zofunda zawo naziyala pansi pa makwerero kuti Yehu akhalepo. Kenaka analiza lipenga, nafuwula kuti, “Yehu ndiye mfumu!”

Yehu Apha Yoramu ndi Ahaziya

14 Choncho Yehu mwana wa Yehosafati, mwana wa Nimisi, anachitira chiwembu Yoramu. (Nthawi imeneyi nʼkuti Yoramu ndi Aisraeli onse akuteteza Ramoti Giliyadi kwa Hazaeli mfumu ya ku Aramu, 15 koma nʼkuti Yoramu atabwerera ku Yezireeli kuti akachire mabala amene Aaramu anamuvulaza pa nkhondo ndi Hazaeli mfumu ya ku Aramu.) Yehu anati, “Ngati mukugwirizana nazo zimenezi, wina aliyense asatuluke mu mzinda muno kupita kukafotokoza nkhaniyi ku Yezireeli.” 16 Pamenepo Yehu anakwera galeta lake, napita ku Yezireeli, chifukwa Yoramu anali akupumula kumeneko ndipo Ahaziya, mfumu ya ku Yuda, nʼkuti ali komweko kudzamuona.

17 Mlonda amene ankayimirira pa nsanja yolondera mzinda wa Yezireeli ataona gulu lankhondo la Yehu likuyandikira, anafuwula kuti, “Ndikuona gulu lankhondo likubwera.”

Yoramu analamula kuti, “Peza munthu wokwera kavalo, mutume kuti akakumane nawo ndi kuwafunsa kuti, ‘Kodi mukubwera mwamtendere?’ ”

18 Choncho munthu wokwera kavalo anapita kukakumana ndi Yehu ndipo anati, “Mfumu ikufunsa kuti, ‘Kodi mukubwera mwamtendere?’ ”

Yehu anayankha kuti, “Kodi iwe nkhani ya mtendere yakukhudza bwanji? Tiye, zinditsata pambuyo panga.”

Mlonda uja anakafotokoza kwa mfumu kuti, “Wamthenga uja wakafika kwa anthuwo koma sakubwerera.”

19 Choncho mfumu inatumanso munthu wina wachiwiri wokwera kavalo. Atafika kwa anthuwo iye anati, “Mfumu ikufunsa kuti, ‘Kodi mukubwera mwamtendere?’ ”

Yehu anayankha kuti, “Kodi iwe nkhani ya mtendere yakukhudza bwanji? Tiye, zinditsata pambuyo panga.”

20 Mlonda uja anakanenanso kuti, “Wamthenga uja wakafika kwa anthuwo koma sakubwereranso. Kuyendako kukukhala ngati kwa Yehu mwana wa Nimisi, iye amayenda ngati munthu wamisala.”

21 Yoramu analamula kuti, “Konzani galeta langa.” Ndipo atakonza galeta lake, Yoramu mfumu ya Israeli ndi Ahaziya mfumu ya ku Yuda anakwera nʼkutuluka mu mzindamo, aliyense atakwera galeta lake, kukakumana ndi Yehu. Iwo anakumana ndi Yehu pa munda umene unali wa Naboti, wa ku Yezireeli. 22 Yoramu ataona Yehu anafunsa kuti, “Yehu, kodi wabwera mwamtendere?”

Yehu anayankha kuti, “Pangakhale bwanji mtendere pamene zopembedza mafano zonse zilipo ndiponso ufiti wa amayi ako Yezebeli uli ponseponse?”

23 Yoramu anatembenuka, nathawa akufuwula kwa Ahaziya kuti, “Ahaziya, anthuwa atiwukira!”

24 Pamenepo Yehu anakoka uta wake ndipo analasa Yoramu kumsana pakati pa mapewa. Muviwo unakalasa mtima wake ndipo anagwa pansi mʼgaleta lakelo. 25 Yehu anawuza Bidikara, mtsogoleri wa galeta lake kuti, “Munyamule ndipo ukamuponye mʼmunda umene unali wa Naboti wa ku Yezireeli, chifukwa kumbukira mmene iwe ndi ine tinkayenda pambuyo pa Ahabu abambo ake, kuti Yehova ananeneratu za iye kuti, 26 ‘Zoonadi dzulo ndinaona magazi a Naboti ndi magazi a ana ake, akutero Yehova, ndipo Ine ndidzakubwezera ndithu choyipa chimenechi pa munda womwe uno, akutero Yehova.’ Tsono munyamule ndipo ukamuponye mʼmundamo, potsatira zimene Yehova ananena.”

27 Ahaziya mfumu ya ku Yuda ataona zimene zinachitika, anathawira ku Beti Hagani. Yehu anamuthamangitsa, uku akufuwula kuti, “Mupheninso!” Iwo anamuvulaza ali mʼgaleta lakelo pa njira yopita ku Guri pafupi ndi Ibuleamu, koma iye anathawira ku Megido ndipo anakafera kumeneko. 28 Antchito ake anamunyamulira mʼgaleta kupita naye ku Yerusalemu ndipo anamuyika mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu mzinda wa Davide. 29 (Mʼchaka cha khumi ndi chimodzi cha ufumu wa Yoramu mwana wa Ahabu, Ahaziya anakhala mfumu ya ku Yuda).

Kuphedwa kwa Yezebeli

30 Kenaka Yehu anapita ku Yezireeli. Yezebeli atamva zimene zinachitika, anapaka zodzikometsera mʼmaso, naluka tsitsi lake, namasuzumira pa zenera. 31 Pamene Yehu ankalowa pa chipata iye anafunsa kuti, “Kodi wabwera mwamtendere, iwe Zimuri, munthu wopha mbuye wako?”

32 Yehu anakweza maso nayangʼana pa zenera, ndipo anafuwula kuti, “Kodi ndani ali mbali yanga? Ndani?” Anthu ofulidwa awiri kapena atatu anayangʼana Yehu pansipo. 33 Yehu anawawuza kuti, “Muponyeni pansi!” Motero anamuponya pansi ndipo magazi ake ena anafalikira pa khoma ndi pa akavalo pamene ankamupondaponda.

34 Yehu analowa mʼnyumba yaufumu ndipo anadya ndi kumwa. Kenaka iye anati, “Kamutoleni mkazi wotembereredwayo, ndipo kamuyikeni mʼmanda, popeza ndi mwana wa mfumu.” 35 Koma atapita kuti akamuyike mʼmanda, sanapeze kanthu kupatula chibade cha mutu wokha, mapazi ake ndi manja ake. 36 Choncho iwo anabwerera kwa Yehu ndi kukamufotokozera kuti, “Mawu amene Yehova anayankhula kudzera mwa mtumiki wake Eliya wa ku Tisibe ndi awa: Pa munda wa ku Yezireeli agalu adzadya mtembo wa Yezebeli. 37 Mtembo wa Yezebeli udzakhala ngati zinyalala pa munda wa ku Yezireeli, kotero kuti palibe amene adzathe kunena kuti, ‘Uyu ndi Yezebeli.’ ”

Jehu Anointed King of Israel

The prophet Elisha summoned a man from the company(A) of the prophets and said to him, “Tuck your cloak into your belt,(B) take this flask of olive oil(C) with you and go to Ramoth Gilead.(D) When you get there, look for Jehu son of Jehoshaphat, the son of Nimshi. Go to him, get him away from his companions and take him into an inner room. Then take the flask and pour the oil(E) on his head and declare, ‘This is what the Lord says: I anoint you king over Israel.’ Then open the door and run; don’t delay!”

So the young prophet went to Ramoth Gilead. When he arrived, he found the army officers sitting together. “I have a message for you, commander,” he said.

“For which of us?” asked Jehu.

“For you, commander,” he replied.

Jehu got up and went into the house. Then the prophet poured the oil(F) on Jehu’s head and declared, “This is what the Lord, the God of Israel, says: ‘I anoint you king over the Lord’s people Israel. You are to destroy the house of Ahab your master, and I will avenge(G) the blood of my servants(H) the prophets and the blood of all the Lord’s servants shed by Jezebel.(I) The whole house(J) of Ahab will perish. I will cut off from Ahab every last male(K) in Israel—slave or free.[a] I will make the house of Ahab like the house of Jeroboam(L) son of Nebat and like the house of Baasha(M) son of Ahijah. 10 As for Jezebel, dogs(N) will devour her on the plot of ground at Jezreel, and no one will bury her.’” Then he opened the door and ran.

11 When Jehu went out to his fellow officers, one of them asked him, “Is everything all right? Why did this maniac(O) come to you?”

“You know the man and the sort of things he says,” Jehu replied.

12 “That’s not true!” they said. “Tell us.”

Jehu said, “Here is what he told me: ‘This is what the Lord says: I anoint you king over Israel.’”

13 They quickly took their cloaks and spread(P) them under him on the bare steps. Then they blew the trumpet(Q) and shouted, “Jehu is king!”

Jehu Kills Joram and Ahaziah(R)

14 So Jehu son of Jehoshaphat, the son of Nimshi, conspired against Joram. (Now Joram and all Israel had been defending Ramoth Gilead(S) against Hazael king of Aram, 15 but King Joram[b] had returned to Jezreel to recover(T) from the wounds the Arameans had inflicted on him in the battle with Hazael king of Aram.) Jehu said, “If you desire to make me king, don’t let anyone slip out of the city to go and tell the news in Jezreel.” 16 Then he got into his chariot and rode to Jezreel, because Joram was resting there and Ahaziah(U) king of Judah had gone down to see him.

17 When the lookout(V) standing on the tower in Jezreel saw Jehu’s troops approaching, he called out, “I see some troops coming.”

“Get a horseman,” Joram ordered. “Send him to meet them and ask, ‘Do you come in peace?(W)’”

18 The horseman rode off to meet Jehu and said, “This is what the king says: ‘Do you come in peace?’”

“What do you have to do with peace?” Jehu replied. “Fall in behind me.”

The lookout reported, “The messenger has reached them, but he isn’t coming back.”

19 So the king sent out a second horseman. When he came to them he said, “This is what the king says: ‘Do you come in peace?’”

Jehu replied, “What do you have to do with peace? Fall in behind me.”

20 The lookout reported, “He has reached them, but he isn’t coming back either. The driving is like(X) that of Jehu son of Nimshi—he drives like a maniac.”

21 “Hitch up my chariot,” Joram ordered. And when it was hitched up, Joram king of Israel and Ahaziah king of Judah rode out, each in his own chariot, to meet Jehu. They met him at the plot of ground that had belonged to Naboth(Y) the Jezreelite. 22 When Joram saw Jehu he asked, “Have you come in peace, Jehu?”

“How can there be peace,” Jehu replied, “as long as all the idolatry and witchcraft of your mother Jezebel(Z) abound?”

23 Joram turned about and fled, calling out to Ahaziah, “Treachery,(AA) Ahaziah!”

24 Then Jehu drew his bow(AB) and shot Joram between the shoulders. The arrow pierced his heart and he slumped down in his chariot. 25 Jehu said to Bidkar, his chariot officer, “Pick him up and throw him on the field that belonged to Naboth the Jezreelite. Remember how you and I were riding together in chariots behind Ahab his father when the Lord spoke this prophecy(AC) against him: 26 ‘Yesterday I saw the blood of Naboth(AD) and the blood of his sons, declares the Lord, and I will surely make you pay for it on this plot of ground, declares the Lord.’[c] Now then, pick him up and throw him on that plot, in accordance with the word of the Lord.”(AE)

27 When Ahaziah king of Judah saw what had happened, he fled up the road to Beth Haggan.[d] Jehu chased him, shouting, “Kill him too!” They wounded him in his chariot on the way up to Gur near Ibleam,(AF) but he escaped to Megiddo(AG) and died there. 28 His servants took him by chariot(AH) to Jerusalem and buried him with his ancestors in his tomb in the City of David. 29 (In the eleventh(AI) year of Joram son of Ahab, Ahaziah had become king of Judah.)

Jezebel Killed

30 Then Jehu went to Jezreel. When Jezebel heard about it, she put on eye makeup,(AJ) arranged her hair and looked out of a window. 31 As Jehu entered the gate, she asked, “Have you come in peace, you Zimri,(AK) you murderer of your master?”[e]

32 He looked up at the window and called out, “Who is on my side? Who?” Two or three eunuchs looked down at him. 33 “Throw her down!” Jehu said. So they threw her down, and some of her blood spattered the wall and the horses as they trampled her underfoot.(AL)

34 Jehu went in and ate and drank. “Take care of that cursed woman,” he said, “and bury her, for she was a king’s daughter.”(AM) 35 But when they went out to bury her, they found nothing except her skull, her feet and her hands. 36 They went back and told Jehu, who said, “This is the word of the Lord that he spoke through his servant Elijah the Tishbite: On the plot of ground at Jezreel dogs(AN) will devour Jezebel’s flesh.[f](AO) 37 Jezebel’s body will be like dung(AP) on the ground in the plot at Jezreel, so that no one will be able to say, ‘This is Jezebel.’”

Footnotes

  1. 2 Kings 9:8 Or Israel—every ruler or leader
  2. 2 Kings 9:15 Hebrew Jehoram, a variant of Joram; also in verses 17 and 21-24
  3. 2 Kings 9:26 See 1 Kings 21:19.
  4. 2 Kings 9:27 Or fled by way of the garden house
  5. 2 Kings 9:31 Or “Was there peace for Zimri, who murdered his master?”
  6. 2 Kings 9:36 See 1 Kings 21:23.