Add parallel Print Page Options

Zaka Zotsiriza za Asa

16 Mʼchaka cha 36 cha ufumu wa Asa, Baasa mfumu ya Israeli inapita kukathira nkhondo dziko la Yuda. Anamangira mpanda mzinda wa Rama kuletsa aliyense kutuluka kapena kulowa mʼdziko la Asa mfumu ya Yuda.

Ndipo Asa anatenga siliva ndi golide ku malo osungirako a mʼNyumba ya Mulungu ndi ku nyumba yake yaufumu ndi kuzitumiza kwa Beni-Hadadi mfumu ya Aramu imene inkakhala mu Damasiko. Iye anati, “Pakhale pangano pakati pa inu ndi ine, monga zinalili pakati pa abambo anu ndi abambo anga. Taonani, ine ndikutumiza kwa inu siliva ndi golide. Tsopano thetsani mgwirizano wanu ndi Baasa mfumu ya Israeli kuti achoke kwa ine.”

Beni-Hadadi anagwirizana ndi mfumu Asa ndipo anatumiza olamulira nkhondo ake kukathira nkhondo mizinda ya Israeli. Iwo anagonjetsa Iyoni, Dani, Abeli-Maimu ndi mizinda yonse yosungira chuma ya Nafutali. Baasa atamva izi, anasiya kumanga Rama ndipo anayimitsa ntchito yakeyo. Ndipo mfumu Asa anabwera ndi Ayuda onse, ndipo anachotsa miyala ndi matabwa ku Rama amene Baasa amagwiritsa ntchito. Ndi zimenezi Asa ankamangira Geba ndi Mizipa.

Nthawi imeneyi mlosi Hanani anabwera kwa Asa mfumu ya Yuda ndipo anati kwa iye, “Chifukwa chakuti munadalira mfumu ya Aramu osati Yehova Mulungu wanu, gulu la ankhondo la mfumu ya ku Aramu lapulumuka mʼmanja mwanu. Kodi Akusi ndi Alibiya sanali gulu lankhondo lamphamvu lokhala ndi magaleta ochuluka ndi okwera magaleta ake? Koma pamene inu munadalira Yehova, Iye anawapereka mʼdzanja lanu. Pakuti Yehova amayangʼana uku ndi uku pa dziko lonse lapansi kuti alimbikitse iwo amene mitima yawo ayipereka kwathunthu kwa Iye. Inu mwachita chinthu chopusa ndipo kuyambira lero mudzakhala pa nkhondo.”

10 Asa anamupsera mtima mlosi uja chifukwa cha izi mwakuti anakwiya kwambiri namuyika mʼndende. Pa nthawi yomweyonso Asa anazunza mwankhanza anthu ena.

11 Ntchito zina za mfumu Asa, kuyambira pachiyambi mpaka kumapeto zalembedwa mʼbuku la mafumu a Yuda ndi Israeli. 12 Mʼchaka cha 39 cha ufumu wake, Asa anayamba kudwala nthenda ya mapazi. Ngakhale nthendayo inali yaululu kwambiri, komabe iye sanafunefune Yehova, koma anafuna thandizo kwa asingʼanga. 13 Ndipo mʼchaka cha 41 cha ufumu wake, Asa anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake. 14 Iye anayikidwa mʼmanda amene anadzisemera yekha mu Mzinda wa Davide. Anagoneka mtembo wake pa chithatha chimene anayikapo zonunkhira zamitundumitundu, ndipo anasonkha chimoto chachikulu pomuchitira ulemu.

Asa’s Last Years(A)(B)

16 In the thirty-sixth year of Asa’s reign Baasha(C) king of Israel went up against Judah and fortified Ramah to prevent anyone from leaving or entering the territory of Asa king of Judah.

Asa then took the silver and gold out of the treasuries of the Lord’s temple and of his own palace and sent it to Ben-Hadad king of Aram, who was ruling in Damascus.(D) “Let there be a treaty(E) between me and you,” he said, “as there was between my father and your father. See, I am sending you silver and gold. Now break your treaty with Baasha king of Israel so he will withdraw from me.”

Ben-Hadad agreed with King Asa and sent the commanders of his forces against the towns of Israel. They conquered Ijon, Dan, Abel Maim[a] and all the store cities of Naphtali.(F) When Baasha heard this, he stopped building Ramah and abandoned his work. Then King Asa brought all the men of Judah, and they carried away from Ramah the stones and timber Baasha had been using. With them he built up Geba and Mizpah.(G)

At that time Hanani(H) the seer came to Asa king of Judah and said to him: “Because you relied(I) on the king of Aram and not on the Lord your God, the army of the king of Aram has escaped from your hand. Were not the Cushites[b](J) and Libyans a mighty army with great numbers(K) of chariots and horsemen[c]? Yet when you relied on the Lord, he delivered(L) them into your hand. For the eyes(M) of the Lord range throughout the earth to strengthen those whose hearts are fully committed to him. You have done a foolish(N) thing, and from now on you will be at war.(O)

10 Asa was angry with the seer because of this; he was so enraged that he put him in prison.(P) At the same time Asa brutally oppressed some of the people.

11 The events of Asa’s reign, from beginning to end, are written in the book of the kings of Judah and Israel. 12 In the thirty-ninth year of his reign Asa was afflicted(Q) with a disease in his feet. Though his disease was severe, even in his illness he did not seek(R) help from the Lord,(S) but only from the physicians. 13 Then in the forty-first year of his reign Asa died and rested with his ancestors. 14 They buried him in the tomb that he had cut out for himself(T) in the City of David. They laid him on a bier covered with spices and various blended perfumes,(U) and they made a huge fire(V) in his honor.

Footnotes

  1. 2 Chronicles 16:4 Also known as Abel Beth Maakah
  2. 2 Chronicles 16:8 That is, people from the upper Nile region
  3. 2 Chronicles 16:8 Or charioteers