Add parallel Print Page Options

Amaziya Mfumu ya Yuda

14 Mʼchaka chachiwiri cha Yehowasi mwana wa Yowahazi mfumu ya Israeli, Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda anayamba kulamulira. Iye anali ndi zaka 25 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 29. Amayi ake anali Yehoyadini wa ku Yerusalemu. Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova, koma osafanana ndi zomwe anachita Davide kholo lake. Iye anatsatira zochita zonse za Yowasi abambo ake. Komabe sanachotse malo opembedzerapo mafano. Anthu anapitiriza kupereka nsembe ndi kufukiza lubani kumeneko.

Atakhazikika mu ufumu wake, Amaziya anapha atumiki ake amene anapha abambo ake, mfumu ija. Komatu iye sanaphe ana a anthu amene anapha abambo ake potsatira zomwe zinalembedwa mʼbuku la Malamulo a Mose. Mʼmenemo Yehova analamula kuti, “Makolo asaphedwe chifukwa cha ana awo, ndipo ana asaphedwe chifukwa cha makolo awo, koma aliyense ayenera kufa chifukwa cha zolakwa zake.”

Iye ndiye amene anapha Aedomu 10,000 mʼchigwa cha Mchere nalanda mzinda wa Sela pa nkhondo ndipo anawutcha Yokiteeli, dzina lake ndi lomwelo mpaka lero lino.

Tsono Amaziya anatuma amithenga kwa Yehowasi mwana wa Yehowahazi, mwana wa Yehu mfumu ya Israeli ndi kumuopseza kuti, “Bwera tidzaonane maso ndi maso.”

Koma Yehowasi mfumu ya Israeli anabweza mawu kwa Amaziya mfumu ya Yuda kuti, “Mtengo wa minga wa ku Lebanoni unatumiza uthenga kwa mkungudza wa ku Lebanoni. ‘Patse mwana wako wamkazi kuti ndimukwatire.’ Kenaka chirombo cha ku Lebanoni chinabwera ndi kupondaponda mtengo wa mingawo. 10 Inde iwe wagonjetsa Edomu ndipo tsopano wayamba kudzikuza. Dzitamandire chifukwa cha kupambana kwako, koma khala kwanu konko! Nʼchifukwa chiyani ukuyamba dala mavuto amene adzakuwononga pamodzi ndi Yuda?”

11 Koma Amaziya sanamvere zimenezi. Choncho Yehowasi mfumu ya Israeli anakamuthira nkhondo. Yehowasi ndi Amaziya anakumana maso ndi maso ku Beti-Semesi mʼdziko la Yuda. 12 Israeli anagonjetsa Yuda ndipo munthu aliyense anathawira kwawo. 13 Yehowasi mfumu ya Israeli anagwira Amaziya mfumu ya Yuda, mwana wa Yowasi, mwana wa Ahaziya ku Beti-Semesi. Ndipo anapita ku Yerusalemu nakagwetsa khoma la Yerusalemu kuyambira ku Chipata cha Efereimu mpaka ku Chipata Chapangodya, gawo lotalika mamita 180. 14 Iye anatenga golide ndi siliva yense pamodzi ndi ziwiya zonse zimene zinali mʼNyumba ya Yehova ndi zimene zinali mosungira chuma cha nyumba ya mfumu. Iye anagwiranso anthu nabwerera ku Samariya.

15 Ntchito zina za Yehowasi ndi zonse zimene anachita, kuwonjezera za nkhondo yake ndi Amaziya mfumu ya Yuda, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli? 16 Yehowasi anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda mu Samariya pamodzi ndi mafumu a Israeli. Ndipo mwana wake Yeroboamu analowa ufumu mʼmalo mwake.

17 Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda anakhala zaka khumi ndi zisanu atamwalira Yehowasi mwana wa Yehowahazi mfumu ya Israeli. 18 Ntchito zina za Amaziya, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda?

19 Anthu anapangana zomuchita chiwembu mu Yerusalemu ndipo Amaziya anathawira ku Lakisi, koma anatumiza anthu ku Lakisiko nakamuphera komweko. 20 Anabwera naye ku pa kavalo ku Yerusalemu ndi kumuyika mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide.

21 Ndipo anthu onse a ku Yuda anatenga Azariya, amene anali ndi zaka 16 namulonga ufumu mʼmalo mwa abambo ake Amaziya. 22 Azariya anamanga mzinda wa Elati ndi kuwubwezeretsa ku Yuda, Amaziya atamwalira.

Mfumu Yeroboamu Wachiwiri wa ku Israeli

23 Mʼchaka cha khumi ndi chisanu cha Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda, Yeroboamu mwana wa Yehowasi mfumu ya Israeli analowa ufumu ku Samariya ndipo analamulira za 41. 24 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova ndipo sanasiye machimo a Yeroboamu mwana wa Nebati, amene anachimwitsa nawo Israeli. 25 Iye ndi amene anabwezeretsanso malire a Israeli kuyambira ku Lebo Hamati mpaka ku Nyanja ya Araba, molingana ndi zimene ananena Yehova Mulungu wa Israeli, kudzera mwa mtumiki wake Yona mwana wa Amitai, mneneri wochokera ku Gati-Heferi.

26 Pakuti Yehova anaona masautso a Israeli amene anali owawa kwambiri, panalibe kapolo kapena mfulu ngakhale wina aliyense amene akanathandiza Israeli. 27 Pakuti Yehova anali asananene zofafaniza ufumu wa Israeli pa dziko lapansi, Iye anawapulumutsa kudzera mʼdzanja la Yeroboamu mwana wa Yowasi.

28 Ntchito zina za Yeroboamu ndi zonse zimene anachita, za kupambana kwake pa nkhondo, za mmene anagonjetsera Damasiko ndi Hamati, imene inali mizinda ya Yuda, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli? 29 Yeroboamu anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi mafumu a Israeli. Ndipo Zekariya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.