Add parallel Print Page Options

Mboni Zotsutsa Israeli

Inu Aisraeli, imvani mawu awa amene Yehova wayankhula kutsutsana nanu, kutsutsana ndi banja lonse limene analitulutsa mu Igupto:

“Inu nokha ndi amene ndinakusankhani
    pakati pa mabanja onse a dziko lapansi;
nʼchifukwa chake ndidzakulangani
    chifukwa cha machimo anu onse.”

Kodi anthu awiri nʼkuyendera limodzi
    asanapangane?
Kodi mkango umabangula mʼnkhalango
    usanagwire nyama?
Kodi msona wamkango umalira mʼphanga mwake
    pamene sunagwire kanthu?
Kodi mbalame nʼkutera pa msampha
    pamene palibe nyambo yake?
Kodi msampha umafwamphuka
    usanakole kanthu?
Kodi pamene lipenga la nkhondo lalira mu mzinda,
    anthu sanjenjemera?
Pamene tsoka lafika mu mzinda,
    kodi si Yehova amene wachititsa zimenezo?

Zoonadi Ambuye Yehova sachita kanthu
    asanawulule zimene akufuna kuchita
    kwa atumiki ake, aneneri.

Mkango wabangula,
    ndani amene sachita mantha?
Ambuye Yehova wayankhula,
    ndani amene sanganenere?

Lengezani zimenezi ku nyumba zaufumu za ku Asidodi
    ndiponso ku nyumba zaufumu za ku Igupto:
“Sonkhanani ku mapiri a ku Samariya;
    onani chisokonezo pakati pake
    ndiponso kuponderezana pakati pa anthu ake.”

10 “Iwo sadziwa kuchita zolungama,
    ndipo amadzaza malo awo otetezedwa ndi zinthu zolanda ku nkhondo ndi zakuba,” akutero Yehova.

11 Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akunena izi:

“Mdani adzalizungulira dzikoli;
    iye adzagwetsa malinga ako,
    ndi kufunkha nyumba zako zaufumu.”

12 Yehova akuti,

“Monga mʼbusa amalanditsa mʼkamwa mwa mkango
    miyendo iwiri yokha kapena msonga yokha ya khutu,
    moteronso ndimo mmene adzapulumukire Aisraeli
amene amakhala mu Samariya
    pa msonga za mabedi awo,
    ndi ku Damasiko pa akakhutagona awo.”

13 “Imvani izi ndipo mupereke umboni wotsutsa nyumba ya Yakobo,” akutero Ambuye, Yehova Mulungu Wamphamvuzonse.

14 “Pa tsiku limene ndidzalange Israeli chifukwa cha machimo ake,
    ndidzagumula maguwa ansembe a ku Beteli;
nyanga za guwa zidzathyoka
    ndipo zidzagwa pansi.
15 Ndidzagwetsa nyumba ya pa nthawi yozizira
    pamodzi ndi nyumba ya pa nthawi yotentha;
nyumba zokongoletsedwa ndi minyanga ya njovu zidzawonongedwa
    ndipo nyumba zikuluzikulu zidzaphwasulidwa,”
            akutero Yehova.