Add parallel Print Page Options

Yoswa Alowa Mʼmalo mwa Mose

31 Tsono Mose anapita ndi kukayankhula mawu awa kwa Aisraeli onse: “Tsopano ndili ndi zaka 120, ndipo sindingathenso kukutsogolerani. Yehova wandiwuza kuti, ‘Iwe sudzawoloka Yorodani.’ Mwini wake Yehova Mulungu wanu ndiye amene adzakutsogolerani powoloka. Iye adzawononga mitundu ina yonse, ndipo inu mudzatenga dziko lawo. Yoswa adzakutsogoleraninso powoloka, monga momwe ananenera Yehova. Ndipo Yehova adzawawononga iwo monga momwe anawonongera Sihoni ndi Ogi, mafumu Aamori, amene Iye anawawononga pamodzi ndi dziko lawo. Ambuye adzawapereka kwa inu, ndipo inu mukawachitire zonse zimene ndakulamulani. Khalani amphamvu ndi olimba mtima. Musachite nawo mantha kapena kunjenjemera pamaso pawo, chifukwa Yehova Mulungu wanu apita nanu. Sadzakusiyani kapena kukutayani.”

Pamenepo Yehova anayitana Yoswa pamaso pa Aisraeli onse ndipo anamuwuza kuti, “Khala wamphamvu ndi wolimba mtima, pakuti iwe udzatsogolera anthu awa ku dziko limene Yehova analumbira kulipereka kwa makolo awo, ndipo iwe ukaligawe pakati pawo kuti likakhale cholowa chawo. Yehova mwini ndiye akukutsogolerani ndipo adzakhala nanu. Sadzakusiyani kapena kukutayani. Usachite mantha ndiponso usataye mtima.”

Kuwerenga Malamulo

Choncho Mose analemba malamulo awa nawapereka kwa ansembe, ana Alevi, amene amanyamula Bokosi la Chipangano la Yehova, ndiponso kwa akuluakulu onse a Aisraeli. 10 Kenaka Mose anawalamula kuti, “Pamapeto pa zaka zisanu ndi ziwiri zilizonse, chaka cha kukhululukidwa ngongole, pa nthawi ya Chikondwerero cha Misasa, 11 pamene Aisraeli onse abwera kudzaonekera pamaso pa Yehova Mulungu wanu pamalo pamene Iye adzasankhe, mudzawerenge malamulo onsewa iwo akumva. 12 Mudzasonkhanitse anthu onse pamodzi, amuna, akazi ndi ana pamodzi ndi alendo amene akukhala mʼmizinda yanu, kuti adzawamve ndi kuphunzira kuopa Yehova Mulungu wanu ndi kutsatira mosamala mawu onse a mʼmalamulowa. 13 Ana awo amene sadziwa malamulo awa, ayenera kuwamva ndi kuphunzira kuopa Yehova Mulungu wanu nthawi zonse pamene mukukhala mʼdziko limene mukuwoloka Yorodani kukalitenga.”

Aneneratu za Kuwukira kwa Aisraeli

14 Yehova anawuza Mose kuti, “Nthawi ya kufa kwako yafika. Itana Yoswa ndipo mubwere ku tenti ya msonkhano, kumene Ine ndidzamulangiza.” Choncho Mose ndi Yoswa anabwera ku tenti ya msonkhano.

15 Pamenepo Yehova anaonekera ku tenti mʼchipilala cha mtambo, ndipo mtambowo unayima pamwamba pa khomo lolowera mu tenti. 16 Ndipo Yehova anawuza Mose kuti, “Iwe ukupita kukapuma kumene kuli makolo ako, ndipo ukangomwalira, anthu awa adzayamba kupembedza milungu yachilendo ya mʼdziko limene akukalowamo. Adzanditaya ndi kuphwanya pangano lomwe ndinachita nawo. 17 Tsiku limenelo Ine ndidzawakwiyira ndi kuwataya. Ndidzawabisira nkhope yanga, ndipo adzawonongedwa. Masautso ambiri ndi zovuta zambiri zidzawagwera, ndipo tsiku limenelo adzafunsa kuti, ‘Kodi masautso awa sanagwere ife chifukwa Yehova Mulungu wathu sali nafe?’ 18 Ndipo Ine ndidzabisa ndithu nkhope yanga pa tsiku limenelo chifukwa cha zoyipa zimene anachita potembenukira kwa milungu ina.

19 “Tsopano ulembe mawu a nyimbo iyi ndipo uwaphunzitse Aisraeli, uwawuze kuti aziyimba, kuti ikhale mboni yanga yowatsutsa. 20 Pamene ndawalowetsa mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi, dziko limene ndinalonjeza mwalumbiro kwa makolo awo, ndipo pamene adzadya ndi kukhuta ndi kumasangalala, iwo adzatembenukira kwa milungu ina ndi kumayipembedza, kundikana Ine ndi kuphwanya pangano langa. 21 Ndipo pamene masautso ambiri ndi zovuta zambiri zidzawagwera, nyimbo iyi idzakhala mboni yanga yowatsutsa, chifukwa zidzukulu zawo sizidzayiwala nyimboyi. Ine ndikudziwa zimene iwo akulingalira kuchita, ngakhale kuti sindinawalowetse mʼdziko limene ndinalonjeza mwa lumbiro.” 22 Choncho Mose analemba nyimbo iyi tsiku limenelo ndi kuwaphunzitsa Aisraeli.

23 Yehova analamula Yoswa mwana wa Nuni kuti, “Khala wamphamvu ndipo limba mtima, chifukwa udzalowetsa Aisraeli mʼdziko limene ndinawalonjeza mwa lumbiro, ndipo Ine mwini ndidzakhala nawe.”

24 Mose atatha kulemba malamulowa mʼbuku, osasiyako kanthu, 25 analamula Alevi amene ananyamula Bokosi la Chipangano la Yehova kuti, 26 “Tengani Buku ili la Malamulo ndi kuliyika pambali pa Bokosi la Chipangano la Yehova Mulungu wanu. Likhale kumeneko ngati mboni yokutsutsani. 27 Pakuti Ine ndikudziwa kuwukira kwanu ndi kuwuma mtima kwanu. Ngati inu mwakhala mukuwukira Yehova ine ndili moyo ndiponso ndili nanu pamodzi, nanga mudzawukira motani ine ndikamwalira! 28 Mundisonkhanitsire atsogoleri onse a mafuko anu pamodzi ndi akuluakulu onse, kuti ndiyankhule mawu awa iwo akumva ndipo kumwamba ndi dziko lapansi zikhale mboni yowatsutsa. 29 Chifukwa ndikudziwa kuti ine ndikamwalira mudzayipa kwambiri ndi kutembenuka kuleka njira imene ndinakulamulani. Masiku amene akubwera, masautso adzakugwerani chifukwa mudzachita zoyipa pamaso pa Yehova ndi kuputa mkwiyo wake chifukwa cha zimene manja anu anapanga.”

Nyimbo ya Mose

30 Ndipo Mose ananena mawu a nyimbo iyi kuyiimba koyambira mpaka potsiriza gulu lonse la Aisraeli likumva:

Joshua to Succeed Moses

31 Then Moses went out and spoke these words to all Israel: “I am now a hundred and twenty years old(A) and I am no longer able to lead you.(B) The Lord has said to me, ‘You shall not cross the Jordan.’(C) The Lord your God himself will cross(D) over ahead of you.(E) He will destroy these nations(F) before you, and you will take possession of their land. Joshua also will cross(G) over ahead of you, as the Lord said. And the Lord will do to them what he did to Sihon and Og,(H) the kings of the Amorites, whom he destroyed along with their land. The Lord will deliver(I) them to you, and you must do to them all that I have commanded you. Be strong and courageous.(J) Do not be afraid or terrified(K) because of them, for the Lord your God goes with you;(L) he will never leave you(M) nor forsake(N) you.”

Then Moses summoned Joshua and said(O) to him in the presence of all Israel, “Be strong and courageous, for you must go with this people into the land that the Lord swore to their ancestors to give them,(P) and you must divide it among them as their inheritance. The Lord himself goes before you and will be with you;(Q) he will never leave you nor forsake you.(R) Do not be afraid; do not be discouraged.”

Public Reading of the Law

So Moses wrote(S) down this law and gave it to the Levitical priests, who carried(T) the ark of the covenant of the Lord, and to all the elders of Israel. 10 Then Moses commanded them: “At the end of every seven years, in the year for canceling debts,(U) during the Festival of Tabernacles,(V) 11 when all Israel comes to appear(W) before the Lord your God at the place he will choose,(X) you shall read this law(Y) before them in their hearing. 12 Assemble the people—men, women and children, and the foreigners residing in your towns—so they can listen and learn(Z) to fear(AA) the Lord your God and follow carefully all the words of this law. 13 Their children,(AB) who do not know this law, must hear it and learn to fear the Lord your God as long as you live in the land you are crossing the Jordan to possess.”

Israel’s Rebellion Predicted

14 The Lord said to Moses, “Now the day of your death(AC) is near. Call Joshua(AD) and present yourselves at the tent of meeting, where I will commission him.(AE)” So Moses and Joshua came and presented themselves at the tent of meeting.(AF)

15 Then the Lord appeared at the tent in a pillar of cloud, and the cloud stood over the entrance to the tent.(AG) 16 And the Lord said to Moses: “You are going to rest with your ancestors,(AH) and these people will soon prostitute(AI) themselves to the foreign gods of the land they are entering. They will forsake(AJ) me and break the covenant I made with them. 17 And in that day I will become angry(AK) with them and forsake(AL) them; I will hide(AM) my face(AN) from them, and they will be destroyed. Many disasters(AO) and calamities will come on them, and in that day they will ask, ‘Have not these disasters come on us because our God is not with us?’(AP) 18 And I will certainly hide my face in that day because of all their wickedness in turning to other gods.

19 “Now write(AQ) down this song and teach it to the Israelites and have them sing it, so that it may be a witness(AR) for me against them. 20 When I have brought them into the land flowing with milk and honey, the land I promised on oath to their ancestors,(AS) and when they eat their fill and thrive, they will turn to other gods(AT) and worship them,(AU) rejecting me and breaking my covenant.(AV) 21 And when many disasters and calamities come on them,(AW) this song will testify against them, because it will not be forgotten by their descendants. I know what they are disposed to do,(AX) even before I bring them into the land I promised them on oath.” 22 So Moses wrote(AY) down this song that day and taught it to the Israelites.

23 The Lord gave this command(AZ) to Joshua son of Nun: “Be strong and courageous,(BA) for you will bring the Israelites into the land I promised them on oath, and I myself will be with you.”

24 After Moses finished writing(BB) in a book the words of this law(BC) from beginning to end, 25 he gave this command to the Levites who carried(BD) the ark of the covenant of the Lord: 26 “Take this Book of the Law and place it beside the ark of the covenant of the Lord your God. There it will remain as a witness against you.(BE) 27 For I know how rebellious(BF) and stiff-necked(BG) you are. If you have been rebellious against the Lord while I am still alive and with you, how much more will you rebel after I die! 28 Assemble before me all the elders of your tribes and all your officials, so that I can speak these words in their hearing and call the heavens and the earth to testify against them.(BH) 29 For I know that after my death you are sure to become utterly corrupt(BI) and to turn from the way I have commanded you. In days to come, disaster(BJ) will fall on you because you will do evil in the sight of the Lord and arouse his anger by what your hands have made.”

The Song of Moses

30 And Moses recited the words of this song from beginning to end in the hearing of the whole assembly of Israel: