Add parallel Print Page Options

32 Mverani, inu mayiko a mmwamba ndipo ine ndidzayankhula;
    imva, iwe dziko lapansi, mawu a pakamwa panga.
Chiphunzitso changa chigwe ngati mvula
    ndipo mawu anga atsike ngati mame,
ngati mvumbi pa udzu watsopano,
    ngati mvula yochuluka pa zomera zanthete.

Ndidzalalikira dzina la Yehova.
    Aa, tamandani ukulu wa Mulungu wathu!
Iye ndi Thanthwe, ntchito zake ndi zangwiro,
    njira zake zonse ndi zolungama.
Mulungu wokhulupirika amene salakwitsa,
    Iye ndiye wolungama ndi wosalakwa.

Koma iwo achita mosakhulupirika pamaso pake,
    iwo si ana akenso,
    koma iwo ndi mʼbado wachinyengo ndi wokhotakhota.
Kodi mukumubwezera Yehova chotere,
    inu anthu opusa ndi opanda nzeru?
Kodi Iye si Atate anu, Mlengi wanu,
    amene anakupangani ndi kukuwumbani?

Kumbukirani masiku amakedzana;
    ganizirani za mibado yakalekale.
Funsa abambo ako ndipo adzakuwuza,
    akuluakulu ako, ndipo adzakufotokozera.
Pamene Wammwambamwamba anapereka mayiko kwa anthu a mitundu ina kukhala cholowa chawo,
    pamene analekanitsa anthu onse,
anayikira malire anthu onse
    molingana ndi chiwerengero cha ana a Israeli.
Pakuti gawo la Yehova ndi anthu ake,
    Yakobo ndiye cholowa chake.

10 Anamupeza mʼchipululu,
    ku malo owuma ndi kopanda kanthu.
Anamuteteza ndi kumusamalira;
    anamutchinjiriza ngati mwanadiso wake,
11 ngati chiwombankhanga chimene chimasasula chisa chake
    nʼkumazungulira pamwamba pa ana ake,
chimene chimatambalalitsa mapiko ake kuti chigwire anawo
    ndi kuwanyamula pa mapiko ake otambalalawo.
12 Yehova yekha ndiye anamutsogolera;
    popanda thandizo la mulungu wachilendo.

13 Anamuyendetsa pamwamba pa mapiri a mʼdziko
    ndi kumudyetsa zipatso za mʼminda.
Anamudyetsa uchi wofula pa thanthwe,
    ndiponso mafuta ochokera mʼnthaka ya miyala,
14 pamodzi ndi chambiko ndi mkaka wochokera ku ngʼombe ndi nkhosa,
    ndiponso ana ankhosa onenepa ndi mbuzi,
pamodzinso ndi nkhosa zazimuna zabwino za ku Basani
    ndiponso tirigu wabwino kwambiri.
Munamwa vinyo wa thovu lofiira.

15 Yesuruni ananenepa ndi kuyamba kuwukira;
    atakhuta, ananenepa ndi kukula thupi.
Anasiya Mulungu amene anamulenga
    ndipo anakana Thanthwe ndi Mpulumutsi wake.
16 Anamuchititsa nsanje ndi milungu yawo yachilendo
    ndiponso anamukwiyitsa ndi mafano awo onyansa.
17 Anapereka nsembe kwa ziwanda zimene si Mulungu,
    milungu imene sankayidziwa nʼkale lomwe,
    milungu yongobwera kumene,
    milungu imene makolo anu sankayiopa.
18 Inu munasiya Thanthwe limene linakulerani;
    munayiwala Mulungu amene anakubalani.

19 Yehova anaona zimenezi ndipo anawakana
    chifukwa ana ake aamuna ndi aakazi anamukwiyitsa.
20 Iye anati, “Ndidzawabisira nkhope yanga,
    ndi kuona kuti mathero awo adzakhala otani;
pakuti ndi mʼbado wopotoka,
    ana amene ndi osakhulupirika.
21 Anandichititsa kukhala wansanje pamene ankapembedza chimene si mulungu
    ndi kundikwiyitsa chifukwa cha mafano awo achabechabe.
Ine ndidzawachititsa kuti achite nsanje ndi mtundu wina wopandapake;
    ndidzawakwiyitsa ndi mtundu wina wachabechabe.
22 Pakuti mkwiyo wanga wayaka ngati moto,
    umene umayaka mpaka ku dziko la anthu akufa.
Motowo udzanyeketsa dziko lapansi ndi zokolola zake
    ndipo udzapsereza maziko a mapiri.

23 “Ndidzawawunjikira masautso
    ndipo mivi yanga yonse idzathera pa iwo.
24 Ndidzawatumizira njala yoopsa,
    malungo woopsa ndi nthenda zofa nazo;
ndidzawatumizira zirombo zakuthengo zowavuta,
    ululu wa njoka ya mʼphiri imene imakwawa pa fumbi.
25 Mʼmisewu lupanga lidzawasandutsa kukhala wopanda ana;
    mantha adzalamulira nyumba zawo.
Anyamata ndi atsikana adzafa,
    ngakhalenso makanda ndi okalamba.
26 Ine ndinanena kuti ndidzawamwaza
    ndi kuwafafaniza kuti anthu asawakumbukirenso,
27 koma sindinafune kuti adani anga adzandinyoze,
    mwina adani anga sadzandimvetsetsa
ndipo adzanena kuti, ‘Tagonjetsa anthuwa ndife;
    Yehova sanachite zonsezi.’ ”

28 Iwo ndi mtundu wopanda maganizo,
    iwo alibe nzeru nʼpangʼono pomwe.
29 Ngati iwo akanakhala anzeru akanamvetsetsa izi
    ndi kuzindikira kuti mathero awo adzakhala otani!
30 Kodi munthu mmodzi akanathamangitsa bwanji anthu 1,000
    kapena anthu awiri kuthamangitsa anthu 10,000, kuti awagonjetse,
Thanthwe lawo likanapanda kuwagulitsa,
    Yehova akanapanda kuwataya?
31 Pakuti thanthwe lawo silofanana ndi Thanthwe lathu,
    ngakhale adani athu amavomereza zimenezi.
32 Mpesa wawo umachokera ku mpesa wa ku Sodomu
    ndiponso ku minda ya ku Gomora.
Mphesa zawo zili ndi ululu wakupha
    ndipo maphava ake ndi owawa.
33 Vinyo wawo ndi wa ululu wa njoka,
    ululu woopsa wa mphiri.

34 “Kodi zimenezi sindinazisunge
    ndi kuzitsekera mʼkatikati mwa chuma changa?
35 Kubwezera chilango nʼkwanga; ndidzawalanga ndine.
    Pa nthawi yake phazi lawo lidzaterera;
tsiku lawo la masautso layandikira
    ndipo chiwonongeko chawo chikubwera pa iwo mofulumira.”

36 Yehova adzaweruza anthu ake
    ndipo adzachitira atumiki ake chifundo
pamene adzaona kuti mphamvu zawo zatha
    ndipo kuti palibe amene watsala, kapolo kapena mfulu.
37 Iye adzanena kuti, “Nanga ili kuti milungu yawo,
    thanthwe limene ankabisalamo,
38 milungu imene inkadya mafuta a nsembe zawo
    ndi kumwa vinyo wa chopereka chawo cha chakumwa?”
Iwuzeni ibwere kuti idzakuthandizeni!
    Ibwere kuti idzakutetezenitu!

39 “Onani tsopano kuti Ine ndine Iyeyo!
    Palibe mulungu wina koma Ine ndekha.
Ine ndimapha ndiponso kupereka moyo,
    ndavulaza ndipo ndidzachiritsa,
    ndipo palibe angathe kupulumutsa munthu mʼmanja mwanga.
40 Ndikweza dzanja langa kumwamba ndi kulumbira kuti,
    ‘Pali Ine wamoyo wamuyaya,
41 pamene ndidzanola lupanga langa lonyezimira
    ndipo dzanja liligwira pakubweretsa chiweruzo,
ndidzabwezera chilango adani anga
    ndi kulanga onse odana nane.
42 Mivi yanga idzakhuta magazi awo
    pamene lupanga langa lidzawononga mnofu:
magazi a anthu ophedwa ndi ogwidwa ukapolo,
    mitu ya atsogoleri a adani.’ ”

43 Kondwerani, inu mitundu yonse ya anthu pamodzi ndi anthu ake,
    pakuti Iye adzabwezera chilango anthu amene anapha atumiki ake;
adzabwezera chilango adani ake
    ndipo adzakhululukira dziko lake ndi la anthu ake.

44 Mose anabwera ndi Yoswa mwana wa Nuni ndipo anayankhula mawu onsewa mʼnyimbo anthu akumva. 45 Mose atatsiriza kunena mawu onsewa pamtima kwa Aisraeli, 46 iye anawawuza kuti, “Muwasunge bwino mu mtima mwanu, mawu onse amene lero lino ndikukuwuzani kuti mudzawuze ana anu, kuti adzamvere mosamalitsa mawu onse a malamulo amenewa. 47 Mawuwa sikuti ndi mawu achabe kwa inu. Mawuwa ndi moyo wanu. Mukawamvera mudzakhala ndi moyo wautali mʼdziko limene mukukalitenga kukhala lanu mukawoloka Yorodani.”

Mose Adzafera pa Phiri la Nebo

48 Tsiku lomwelo Yehova anawuza Mose kuti, 49 “Pita ku mapiri a ku Abarimu ukakwere pa Phiri la Nebo ku Mowabu, moyangʼanana ndi Yeriko, ndipo ukaone dziko la Kanaani, dziko limene ndikulipereka kwa Aisraeli kukhala lawo. 50 Iwe udzafera pa phiri limenelo ndipo udzapita kumene makolo ako anapita, monga mʼbale wako Aaroni anafera pa phiri la Hori ndipo anakakhala ndi anthu a mtundu wake. 51 Chifukwa chake nʼchakuti inu nonse awiri simunakhulupirike kwa Ine pamaso pa Aisraeli pa madzi a Meriba ku Kadesi mʼchipululu cha Zini chifukwa simunandilemekeze kokwanira pakati pa Aisraeli. 52 Choncho udzalionera kutali dziko limene ndikupereka kwa Aisraeli. Sudzalowa mʼdziko limene ndi kulipereka kwa Aisraeli.”

32 Listen,(A) you heavens,(B) and I will speak;
    hear, you earth, the words of my mouth.(C)
Let my teaching fall like rain(D)
    and my words descend like dew,(E)
like showers(F) on new grass,
    like abundant rain on tender plants.

I will proclaim(G) the name of the Lord.(H)
    Oh, praise the greatness(I) of our God!
He is the Rock,(J) his works are perfect,(K)
    and all his ways are just.
A faithful God(L) who does no wrong,
    upright(M) and just is he.(N)

They are corrupt and not his children;
    to their shame they are a warped and crooked generation.(O)
Is this the way you repay(P) the Lord,
    you foolish(Q) and unwise people?(R)
Is he not your Father,(S) your Creator,[a]
    who made you and formed you?(T)

Remember the days of old;(U)
    consider the generations long past.(V)
Ask your father and he will tell you,
    your elders, and they will explain to you.(W)
When the Most High(X) gave the nations their inheritance,
    when he divided all mankind,(Y)
he set up boundaries(Z) for the peoples
    according to the number of the sons of Israel.[b](AA)
For the Lord’s portion(AB) is his people,
    Jacob his allotted inheritance.(AC)

10 In a desert(AD) land he found him,
    in a barren and howling waste.(AE)
He shielded(AF) him and cared for him;
    he guarded him as the apple of his eye,(AG)
11 like an eagle that stirs up its nest
    and hovers over its young,(AH)
that spreads its wings to catch them
    and carries them aloft.(AI)
12 The Lord alone led(AJ) him;(AK)
    no foreign god was with him.(AL)

13 He made him ride on the heights(AM) of the land
    and fed him with the fruit of the fields.
He nourished him with honey from the rock,(AN)
    and with oil(AO) from the flinty crag,
14 with curds and milk from herd and flock
    and with fattened lambs and goats,
with choice rams of Bashan(AP)
    and the finest kernels of wheat.(AQ)
You drank the foaming blood of the grape.(AR)

15 Jeshurun[c](AS) grew fat(AT) and kicked;
    filled with food, they became heavy and sleek.
They abandoned(AU) the God who made them
    and rejected the Rock(AV) their Savior.
16 They made him jealous(AW) with their foreign gods
    and angered(AX) him with their detestable idols.
17 They sacrificed(AY) to false gods,(AZ) which are not God—
    gods they had not known,(BA)
    gods that recently appeared,(BB)
    gods your ancestors did not fear.
18 You deserted the Rock, who fathered you;
    you forgot(BC) the God who gave you birth.

19 The Lord saw this and rejected them(BD)
    because he was angered by his sons and daughters.(BE)
20 “I will hide my face(BF) from them,” he said,
    “and see what their end will be;
for they are a perverse generation,(BG)
    children who are unfaithful.(BH)
21 They made me jealous(BI) by what is no god
    and angered me with their worthless idols.(BJ)
I will make them envious by those who are not a people;
    I will make them angry by a nation that has no understanding.(BK)
22 For a fire will be kindled by my wrath,(BL)
    one that burns down to the realm of the dead below.(BM)
It will devour(BN) the earth and its harvests(BO)
    and set afire the foundations of the mountains.(BP)

23 “I will heap calamities(BQ) on them
    and spend my arrows(BR) against them.
24 I will send wasting famine(BS) against them,
    consuming pestilence(BT) and deadly plague;(BU)
I will send against them the fangs of wild beasts,(BV)
    the venom of vipers(BW) that glide in the dust.(BX)
25 In the street the sword will make them childless;
    in their homes terror(BY) will reign.(BZ)
The young men and young women will perish,
    the infants and those with gray hair.(CA)
26 I said I would scatter(CB) them
    and erase their name from human memory,(CC)
27 but I dreaded the taunt of the enemy,
    lest the adversary misunderstand(CD)
and say, ‘Our hand has triumphed;
    the Lord has not done all this.’”(CE)

28 They are a nation without sense,
    there is no discernment(CF) in them.
29 If only they were wise and would understand this(CG)
    and discern what their end will be!(CH)
30 How could one man chase a thousand,
    or two put ten thousand to flight,(CI)
unless their Rock had sold them,(CJ)
    unless the Lord had given them up?(CK)
31 For their rock is not like our Rock,(CL)
    as even our enemies concede.(CM)
32 Their vine comes from the vine of Sodom(CN)
    and from the fields of Gomorrah.
Their grapes are filled with poison,(CO)
    and their clusters with bitterness.(CP)
33 Their wine is the venom of serpents,
    the deadly poison of cobras.(CQ)

34 “Have I not kept this in reserve
    and sealed it in my vaults?(CR)
35 It is mine to avenge;(CS) I will repay.(CT)
    In due time their foot will slip;(CU)
their day of disaster is near
    and their doom rushes upon them.(CV)

36 The Lord will vindicate his people(CW)
    and relent(CX) concerning his servants(CY)
when he sees their strength is gone
    and no one is left, slave(CZ) or free.[d]
37 He will say: “Now where are their gods,
    the rock they took refuge in,(DA)
38 the gods who ate the fat of their sacrifices
    and drank the wine of their drink offerings?(DB)
Let them rise up to help you!
    Let them give you shelter!

39 “See now that I myself am he!(DC)
    There is no god besides me.(DD)
I put to death(DE) and I bring to life,(DF)
    I have wounded and I will heal,(DG)
    and no one can deliver out of my hand.(DH)
40 I lift my hand(DI) to heaven and solemnly swear:
    As surely as I live forever,(DJ)
41 when I sharpen my flashing sword(DK)
    and my hand grasps it in judgment,
I will take vengeance(DL) on my adversaries
    and repay those who hate me.(DM)
42 I will make my arrows drunk with blood,(DN)
    while my sword devours flesh:(DO)
the blood of the slain and the captives,
    the heads of the enemy leaders.”

43 Rejoice,(DP) you nations, with his people,[e][f]
    for he will avenge the blood of his servants;(DQ)
he will take vengeance on his enemies(DR)
    and make atonement for his land and people.(DS)

44 Moses came with Joshua[g](DT) son of Nun and spoke all the words of this song in the hearing of the people. 45 When Moses finished reciting all these words to all Israel, 46 he said to them, “Take to heart all the words I have solemnly declared to you this day,(DU) so that you may command(DV) your children to obey carefully all the words of this law. 47 They are not just idle words for you—they are your life.(DW) By them you will live long(DX) in the land you are crossing the Jordan to possess.”

Moses to Die on Mount Nebo

48 On that same day the Lord told Moses,(DY) 49 “Go up into the Abarim(DZ) Range to Mount Nebo(EA) in Moab, across from Jericho,(EB) and view Canaan,(EC) the land I am giving the Israelites as their own possession. 50 There on the mountain that you have climbed you will die(ED) and be gathered to your people, just as your brother Aaron died(EE) on Mount Hor(EF) and was gathered to his people. 51 This is because both of you broke faith with me in the presence of the Israelites at the waters of Meribah Kadesh(EG) in the Desert of Zin(EH) and because you did not uphold my holiness among the Israelites.(EI) 52 Therefore, you will see the land only from a distance;(EJ) you will not enter(EK) the land I am giving to the people of Israel.”

Footnotes

  1. Deuteronomy 32:6 Or Father, who bought you
  2. Deuteronomy 32:8 Masoretic Text; Dead Sea Scrolls (see also Septuagint) sons of God
  3. Deuteronomy 32:15 Jeshurun means the upright one, that is, Israel.
  4. Deuteronomy 32:36 Or and they are without a ruler or leader
  5. Deuteronomy 32:43 Or Make his people rejoice, you nations
  6. Deuteronomy 32:43 Masoretic Text; Dead Sea Scrolls (see also Septuagint) people, / and let all the angels worship him, /
  7. Deuteronomy 32:44 Hebrew Hoshea, a variant of Joshua