Add parallel Print Page Options

Malamulo Khumi

Mose anayitanitsa Aisraeli onse nati:

Tamverani inu Aisraeli, malangizo ndi malamulo amene ndikuwuzeni lero. Muwaphunzire ndi kuonetsetsa kuti mukuwatsata. Yehova Mulungu wathu anachita pangano ndi ife ku Horebu. Yehova sanachite pangano ndi makolo athu koma ndi ife, tonse amene tili moyo lero. Yehova anayankhula nanu maso ndi maso kuchokera mʼmoto pa phiri paja. (Pa nthawi imeneyo ine ndinayimirira pakati pa Yehova ndi inu kuti ndikuwuzeni mawu a Yehova, chifukwa inu munkachita mantha ndi moto ndipo simunakwere ku phiri). Ndipo Iye anati:

“Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakutulutsa ku Igupto, mʼdziko la ukapolo.

“Usakhale ndi milungu ina koma Ine ndekha.

“Usadzipangire chofanizira chinthu chilichonse chakumwamba kapena cha pa dziko lapansi kapena cha mʼmadzi a pansi pa dziko. Usazigwadire kapena kuzipembedza, pakuti Ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wansanje, wolanga ana chifukwa cha tchimo la makolo awo mpaka mʼbado wachitatu ndi wachinayi wa iwo amene amadana nane, 10 koma ndimaonetsa chikondi chosasinthika ku mibado miyandamiyanda ya anthu amene amandikonda ndi kusunga malamulo anga.

11 “Usagwiritse ntchito molakwika dzina la Yehova Mulungu wako, pakuti Yehova adzamutenga kukhala wochimwa aliyense amene akugwiritsa ntchito dzina lakelo molakwika.

12 “Uzisunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika monga momwe Yehova Mulungu wako anakulamulira. 13 Uzigwira ntchito zako zonse masiku asanu ndi limodzi, 14 koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndi Sabata, tsiku loperekedwa kwa Yehova Mulungu wako. Tsiku limeneli musagwire ntchito iliyonse, inuyo kapena mwana wanu wamwamuna kapena mwana wanu wamkazi kapena wantchito wanu wamwamuna kapena mdzakazi wanu kapena ngʼombe yanu kapena bulu wanu kapena ziweto zanu kapena mlendo amene akukhala mʼmudzi mwanu, motero ndiye kuti wantchito wanu wamwamuna ndi wantchito wanu wamkazi adzapumula monga inuyo. 15 Kumbukira kuti unali kapolo ku Igupto ndipo Yehova Mulungu wako anakutulutsa kumeneko ndi dzanja lamphamvu ndi lotambasuka. Choncho Yehova Mulungu wako akukulamula kuti uzisunga tsiku la Sabata.

16 “Lemekeza abambo ako ndi amayi ako monga Yehova Mulungu wako wakulamulira iwe kuti ukhale ndi moyo wautali ndi kuti zikuyendere bwino mʼdziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.

17 “Usaphe.

18 “Usachite chigololo.

19 “Usabe.

20 “Usapereke umboni womunamizira mnzako.

21 “Usasirire mkazi wa mnzako. Usasirire nyumba ya mnzako kapena munda wake, wantchito wake wamwamuna kapena mdzakazi wake, ngʼombe yake kapena bulu wake, kapena chilichonse cha mnzako.”

22 Awa ndi malamulo amene Yehova anayankhula ndi mawu okweza kwa gulu lanu lonse pa phiri paja mʼmoto, mtambo ndi mdima woopsa, sanawonjezerepo kanthu. Ndipo anawalemba pa mapale awiri amiyala ndi kundipatsa.

23 Mutamva mawu kuchokera mu mdimawo, phiri lili moto lawilawi, atsogoleri onse a mafuko anu ndi akuluakulu anu anabwera kwa ine. 24 Ndipo munati, “Yehova Mulungu wathu wationetsa ulemerero ndi ukulu wake, ndipo tamva mawu ake kuchokera mʼmoto. Lero taona kuti munthu akhoza kukhala ndi moyo ngakhale Mulungu atayankhula naye. 25 Koma tsopano tife chifukwa chiyani? Moto waukuluwu utinyeketsa, ndipo tifa tikapitirirabe kumva mawu a Yehova Mulungu wathu. 26 Pakuti ndi munthu uti wolengedwa amene anamvapo mawu a Mulungu wamoyo akuyankhula kuchokera mʼmoto, monga tachitiramu, nakhala ndi moyo? 27 Pita pafupi kuti ukamvetsere zonse zimene Yehova Mulungu wathu akunena. Kenaka udzatiwuze chilichonse chimene Yehova Mulungu wathu akunena ndipo tidzamvera ndi kuchita.”

28 Yehova anakumvani pamene munkayankhula kwa ine ndipo Yehova anati kwa ine, “Ndamva zimene anthuwa anena kwa iwe. Chilichonse chimene anena ndi chabwino. 29 Zikanakhala bwino akanakhala ndi mtima wondiopa ndi kusunga malamulo anga nthawi zonse kuti zinthu ziziwayendera bwino, iwowo pamodzi ndi ana awo kwamuyaya.

30 “Pita uwawuze kuti abwerere ku matenti awo. 31 Koma iwe ukhale kuno ndi ine kuti ndikupatse malamulo, malangizo ndi ziphunzitso zimene azitsatira mʼdziko limene ndiwapatse kuti alitenge.”

32 Choncho samalirani kuchita zimene Yehova Mulungu wanu akukulamulirani inu, musapatukire kudzanja lamanja kapena lamanzere. 33 Muyende mʼnjira yonse imene Yehova Mulungu wanu wakulamulirani kuti mukhale ndi moyo ndi kupambana, ndi kuti masiku anu achuluke mʼdziko limene mudzatengelo.

The Ten Commandments(A)

Moses summoned all Israel and said:

Hear, Israel, the decrees and laws(B) I declare in your hearing today. Learn them and be sure to follow them. The Lord our God made a covenant(C) with us at Horeb.(D) It was not with our ancestors[a] that the Lord made this covenant, but with us,(E) with all of us who are alive here today.(F) The Lord spoke(G) to you face to face(H) out of the fire(I) on the mountain. (At that time I stood between(J) the Lord and you to declare to you the word of the Lord, because you were afraid(K) of the fire and did not go up the mountain.) And he said:

“I am the Lord your God, who brought you out of Egypt,(L) out of the land of slavery.(M)

“You shall have no other gods before[b] me.

“You shall not make for yourself an image in the form of anything in heaven above or on the earth beneath or in the waters below.(N) You shall not bow down to them or worship them; for I, the Lord your God, am a jealous God, punishing the children for the sin of the parents(O) to the third and fourth generation of those who hate me,(P) 10 but showing love to a thousand(Q) generations of those who love me and keep my commandments.(R)

11 “You shall not misuse the name(S) of the Lord your God, for the Lord will not hold anyone guiltless who misuses his name.(T)

12 “Observe the Sabbath day by keeping it holy,(U) as the Lord your God has commanded you. 13 Six days you shall labor and do all your work, 14 but the seventh day(V) is a sabbath to the Lord your God. On it you shall not do any work, neither you, nor your son or daughter, nor your male or female servant,(W) nor your ox, your donkey or any of your animals, nor any foreigner residing in your towns, so that your male and female servants may rest, as you do.(X) 15 Remember that you were slaves(Y) in Egypt and that the Lord your God brought you out of there with a mighty hand(Z) and an outstretched arm.(AA) Therefore the Lord your God has commanded you to observe the Sabbath day.

16 “Honor your father(AB) and your mother,(AC) as the Lord your God has commanded you, so that you may live long(AD) and that it may go well with you in the land the Lord your God is giving you.

17 “You shall not murder.(AE)

18 “You shall not commit adultery.(AF)

19 “You shall not steal.(AG)

20 “You shall not give false testimony against your neighbor.(AH)

21 “You shall not covet your neighbor’s wife. You shall not set your desire on your neighbor’s house or land, his male or female servant, his ox or donkey, or anything that belongs to your neighbor.”(AI)

22 These are the commandments the Lord proclaimed in a loud voice to your whole assembly there on the mountain from out of the fire, the cloud and the deep darkness;(AJ) and he added nothing more. Then he wrote them on two stone tablets(AK) and gave them to me.

23 When you heard the voice out of the darkness, while the mountain was ablaze with fire, all the leaders of your tribes and your elders(AL) came to me. 24 And you said, “The Lord our God has shown us(AM) his glory and his majesty,(AN) and we have heard his voice from the fire. Today we have seen that a person can live even if God speaks with them.(AO) 25 But now, why should we die? This great fire will consume us, and we will die if we hear the voice of the Lord our God any longer.(AP) 26 For what mortal has ever heard the voice of the living God speaking out of fire, as we have, and survived?(AQ) 27 Go near and listen to all that the Lord our God says.(AR) Then tell us whatever the Lord our God tells you. We will listen and obey.”(AS)

28 The Lord heard you when you spoke to me, and the Lord said to me, “I have heard what this people said to you. Everything they said was good.(AT) 29 Oh, that their hearts would be inclined to fear me(AU) and keep all my commands(AV) always, so that it might go well with them and their children forever!(AW)

30 “Go, tell them to return to their tents. 31 But you stay here(AX) with me so that I may give you all the commands, decrees and laws you are to teach them to follow in the land I am giving them to possess.”

32 So be careful to do what the Lord your God has commanded you;(AY) do not turn aside to the right or to the left.(AZ) 33 Walk in obedience to all that the Lord your God has commanded you,(BA) so that you may live and prosper and prolong your days(BB) in the land that you will possess.

Footnotes

  1. Deuteronomy 5:3 Or not only with our parents
  2. Deuteronomy 5:7 Or besides