Add parallel Print Page Options

Madalitso Akabwerera kwa Yehova

30 Madalitso ndi matemberero awa onse amene ndawayika pamaso panu akadzafika pa inu, inu nʼkukumbukira kulikonse kumene Yehova Mulungu wanu wakubalalitsirani pakati pa mitundu ya anthu, ndipo inu pamodzi ndi ana anu nʼkudzatembenukira kwa Yehova Mulungu wanu ndi kumumvera ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse molingana ndi chilichonse chimene ndakulamulani lero lino, pamenepo Yehova Mulungu wanu adzakukhalitsani monga kale ndi kukuchitirani chifundo, ndipo adzakusonkhanitsani kukuchotsani ku mitundu ina ya anthu kumene anakubalalitsirani. Ngakhale atakupirikitsirani ku malekezero a dziko lapansi, adzakusonkhanitsani kuchokera kumeneko ndi kukubweretsaninso. Adzakubweretsani ku dziko limene linali la makolo anu, ndipo lidzakhala lanu. Iye adzakulemeretsani ndi kukuchulukitsani kupambana makolo anu. Yehova Mulungu wanu adzasintha mitima yanu pamodzi ndi mitima ya zidzukulu zanu, kotero kuti mudzamukonda ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, ndipo mudzakhala ndi moyo. Yehova Mulungu wanu adzayika matemberero awa onse pa adani anu amene amadana nanu ndi kukuzunzani. Inu mudzamveranso Yehova ndi kutsatira malamulo ake onse amene ndikukupatsani lero lino. Pamenepo Yehova Mulungu wanu adzakulemeretsani pa zochita zanu zonse ndipo adzakupatsani ana ambiri, zoweta zambiri, ndiponso mudzakhala ndi zokolola zambiri za mʼdziko lanu. Yehova adzakondwera nanunso ndi kukulemeretsani monga momwe anakondwera ndi makolo anu, 10 ngati mudzamvera Yehova Mulungu wanu ndi kusunga malamulo ake ndi mawu ake amene alembedwa Mʼbuku ili la Malamulo ndi kutembenukira kwa Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.

Moyo kapena Imfa

11 Tsopano zimene ndikukulamulirani leroli sizovuta kapena zapatali. 12 Sizili kumwamba, kuti muzichita kufunsa kuti, “Kodi ndani amene akwere kumwamba kuti akazitenge ndi kudzatilalikira kuti timvere?” 13 Komanso sizili pa tsidya la nyanja, kuti muzichita kufunsa kuti, “Kodi ndani amene adzawoloke nyanja kuti akatenge ndi kudzatilalikira kuti timvere?” 14 Ayi, mawu ali pafupi ndi inu; ali mʼkamwa mwanu ndi mu mtima mwanu kuti muwamvere.

15 Taonani, lero ine ndayika pamaso panu moyo ndi zokoma, imfa ndi chiwonongeko. 16 Pakuti lero ndikukulamulani kuti mukonde Yehova Mulungu wanu, kuti muyende mʼnjira zake, ndi kusunga malamulo ake, malangizo ake. Mukatero mudzakhala ndi moyo ndi kuchulukana, ndipo Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani mʼdziko limene mukulowa kukakhalamo.

17 Koma ngati mtima wanu udzatembenuka, inu nʼkukhala osandimvera, ndipo ngati mudzatengeka ndi kupita kukagwadira milungu ina ndi kuyipembedza, 18 lero ndikulengeza kwa inu kuti mudzawonongeka ndithu. Simudzakhala nthawi yayitali mʼdziko limene mukulowamo pamene mukuwoloka Yorodani kuti mulitenge.

19 Lero kumwamba ndi dziko lapansi zikhale mboni zodzakutsutsani pakuti ndayika pamaso panu moyo ndi imfa, madalitso ndi matemberero. Tsopano sankhani moyo kuti inu ndi ana anu mukhale ndi moyo. 20 Ndi kuti mukonde Yehova Mulungu wanu, kumvera mawu ake, ndi kukhulupirika kwa Iye. Pakuti Yehova ndiye moyo wanu, ndipo mudzakhala zaka zambiri mʼdziko limene analumbira kulipereka kwa makolo anu, Abrahamu, Isake ndi Yakobo.