Add parallel Print Page Options

14 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Uza Aisraeli abwerere ndi kukagona pafupi ndi Pihahiroti, pakati pa Migidoli ndi nyanja. Inu mumange zithando mʼmbali mwa nyanja moyangʼanana ndi Baala-Zefoni. Farao adzaganiza kuti ‘Aisraeli asokonezeka nʼkumangozungulirazungulira mu dzikomo, chipululu chitawazinga.’ Ndidzawumitsa mtima wa Farao ndipo adzathamangira Aisraeliwo. Choncho ndikadzagonjetsa Farao ndi gulu lake lonse la nkhondo, Ine ndidzalemekezedwa.” Choncho Aisraeli aja anachita zimenezi.

Farao, mfumu ya Igupto atamva kuti anthu aja athawa, iye pamodzi ndi nduna zake anasintha maganizo awo pa Israeli ndipo anati, “Ife tachita chiyani? Tawalola Aisraeli kuti apite ndi kuleka kutitumikira?” Choncho anakonzetsa galeta lake ndipo ananyamuka pamodzi ndi ankhondo ake. Iye anatenga magaleta 600 abwino kwambiri pamodzi ndi magaleta ena a dziko la Igupto. Anatenganso akuluakulu onse ankhondo. Yehova anawumitsa mtima wa Farao mfumu ya dziko la Igupto, kotero iye anawathamangira Aisraeli amene ankachoka mʼdzikomo mosavutika. Aigupto aja (kutanthauza akavalo ndi magaleta onse a Farao, okwera akavalowo pamodzi ndi gulu lonse la nkhondo) analondola Aisraeli aja ndipo anakawapeza pamalo pamene anamanga zithando paja, mʼmbali mwa nyanja, pafupi ndi Pihahiroti, moyangʼanana ndi Baala-Zefoni.

10 Tsono Farao anayandikira. Ndipo Aisraeli ataona kuti Aigupto akuwatsatira, anachita mantha aakulu ndipo anafuwula kwa Yehova. 11 Iwo anafunsa Mose kuti, “Kodi nʼchifukwa chakuti kunalibe manda ku dziko la Igupto kuti iwe utibweretse muno mʼchipululu kuti tidzafe? Chimene watichitachi nʼchiyani, kutitulutsa mʼdziko la Igupto? 12 Kodi sindizo zimene tinakuwuza mʼdziko la Igupto? Ife tinati, ‘Tileke titumikire Aigupto?’ Zikanatikomera kutumikira Aigupto kulekana ndi kufa mʼchipululu muno.”

13 Mose anayankha anthu kuti, “Musachite mantha. Imani, ndipo muone chipulumutso chimene Yehova akuchitireni lero. Aigupto amene mukuwaona lerowa simudzawaonanso. 14 Yehova adzakumenyerani nkhondo. Inu mungokhala chete.”

15 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Chifukwa chiyani ukufuwulira kwa ine? Uwuze Aisraeli aziyenda. 16 Nyamula ndodo yako ndi kutambasula dzanja lako kuloza ku nyanja, kugawa madzi kuti Aisraeli awoloke powuma. 17 Ine ndidzawumitsa mitima ya Aigupto kotero kuti adzatsatirabe Aisraeli. Ndipo ine ndikadzagonjetsa Farao ndi asilikali ake onse ankhondo, okwera magaleta ndi akavalo, ndidzapeza ulemerero. 18 Aigupto adzadziwa kuti Ine ndine Yehova akadzaona mmene ndipambanire Farao ndi magaleta ndi owayendetsa ake.”

19 Ndipo mngelo wa Mulungu amene amayenda patsogolo pa gulu lankhondo la Israeli anachoka ndi kupita kumbuyo kwawo. Chipilala cha mtambo chinasunthanso kuchoka kutsogolo ndi kupita kumbuyo kwawo. 20 Choncho mtambowo unakhala pakati pa asilikali ankhondo a dziko la Igupto ndi a dziko la Israeli. Choncho panali mdima motero kuti magulu awiri ankhondowa sanathe kuyandikizana usiku wonse.

21 Kenaka Mose anatambalitsa dzanja lake pa nyanja, ndipo Yehova pogwiritsa ntchito mphepo yamphamvu ya kummawa imene inawomba usiku wonse anabweza madzi ndi kuwumitsa nyanja ija. Choncho nyanja ija inagawanika. 22 Ndipo Aisraeli anawoloka pakati pa nyanja powuma, madzi atasanduka khoma kumanja ndi kumanzere kwawo.

23 Aigupto onse, Farao, ndi onse okwera pa magaleta ndi akavalo anawalondola ndipo analowa mʼmadzi. 24 Kutatsala pangʼono kucha, Yehova ali mu chipilala chamoto ndi chamtambo, anayangʼana asilikali ankhondo a Igupto ndipo anabweretsa chisokonezo pakati pawo. 25 Yehova anamanga matayala a magaleta kotero kuti ankavutika kuyenda. Ndipo Aigupto anati, “Tiyeni tiwathawe Aisraeli! Yehova akuwamenyera nkhondo kulimbana nafe.”

26 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Tambasula dzanja lako pa nyanja kuti madzi amize Aigupto ndi magaleta awo ndi okwera pa akavalo.” 27 Mose anatambasula dzanja lake pa nyanja, ndipo mmene kumacha nyanja inabwerera mʼmalo mwake. Aigupto pothawa anakumana nayo, ndipo Yehova anawakokera mʼnyanja momwemo. 28 Madzi anabwerera ndi kumiza magaleta ndi okwera akavalo, asilikali ankhondo onse amene anatsatira Aisraeli mʼnyanja, palibe ndi mmodzi yemwe amene anapulumuka.

29 Koma Aisraeli aja anawoloka nyanja pansi pali powuma, madzi atachita khoma kumanja ndi kumanzere kwawo. 30 Tsiku limeneli Yehova anapulumutsa Israeli mʼmanja mwa Aigupto ndipo Israeli anaona Aigupto ali lambalamba mʼmbali mwa nyanja atafa 31 Choncho Aisraeli anaona dzanja lamphamvu la Yehova limene linagonjetsa Aigupto aja, ndipo iwo anaopa Yehova ndi kumukhulupirira pamodzi ndi mtumiki wake Mose.

14 Then the Lord said to Moses, “Tell the Israelites to turn back and encamp near Pi Hahiroth, between Migdol(A) and the sea. They are to encamp by the sea, directly opposite Baal Zephon.(B) Pharaoh will think, ‘The Israelites are wandering around the land in confusion, hemmed in by the desert.’ And I will harden Pharaoh’s heart,(C) and he will pursue them.(D) But I will gain glory(E) for myself through Pharaoh and all his army, and the Egyptians will know that I am the Lord.”(F) So the Israelites did this.

When the king of Egypt was told that the people had fled,(G) Pharaoh and his officials changed their minds(H) about them and said, “What have we done? We have let the Israelites go and have lost their services!” So he had his chariot made ready and took his army with him. He took six hundred of the best chariots,(I) along with all the other chariots of Egypt, with officers over all of them. The Lord hardened the heart(J) of Pharaoh king of Egypt, so that he pursued the Israelites, who were marching out boldly.(K) The Egyptians—all Pharaoh’s horses(L) and chariots, horsemen[a] and troops(M)—pursued the Israelites and overtook(N) them as they camped by the sea near Pi Hahiroth, opposite Baal Zephon.(O)

10 As Pharaoh approached, the Israelites looked up, and there were the Egyptians, marching after them. They were terrified and cried(P) out to the Lord. 11 They said to Moses, “Was it because there were no graves in Egypt that you brought us to the desert to die?(Q) What have you done to us by bringing us out of Egypt? 12 Didn’t we say to you in Egypt, ‘Leave us alone; let us serve the Egyptians’? It would have been better for us to serve the Egyptians than to die in the desert!”(R)

13 Moses answered the people, “Do not be afraid.(S) Stand firm and you will see(T) the deliverance the Lord will bring you today. The Egyptians you see today you will never see(U) again. 14 The Lord will fight(V) for you; you need only to be still.”(W)

15 Then the Lord said to Moses, “Why are you crying out to me?(X) Tell the Israelites to move on. 16 Raise your staff(Y) and stretch out your hand over the sea to divide the water(Z) so that the Israelites can go through the sea on dry ground. 17 I will harden the hearts(AA) of the Egyptians so that they will go in after them.(AB) And I will gain glory through Pharaoh and all his army, through his chariots and his horsemen. 18 The Egyptians will know that I am the Lord(AC) when I gain glory through Pharaoh, his chariots and his horsemen.”

19 Then the angel of God,(AD) who had been traveling in front of Israel’s army, withdrew and went behind them. The pillar of cloud(AE) also moved from in front and stood behind(AF) them, 20 coming between the armies of Egypt and Israel. Throughout the night the cloud brought darkness(AG) to the one side and light to the other side; so neither went near the other all night long.

21 Then Moses stretched out his hand(AH) over the sea,(AI) and all that night the Lord drove the sea back with a strong east wind(AJ) and turned it into dry land.(AK) The waters were divided,(AL) 22 and the Israelites went through the sea(AM) on dry ground,(AN) with a wall(AO) of water on their right and on their left.

23 The Egyptians pursued them, and all Pharaoh’s horses and chariots and horsemen(AP) followed them into the sea. 24 During the last watch of the night the Lord looked down from the pillar of fire and cloud(AQ) at the Egyptian army and threw it into confusion.(AR) 25 He jammed[b] the wheels of their chariots so that they had difficulty driving. And the Egyptians said, “Let’s get away from the Israelites! The Lord is fighting(AS) for them against Egypt.”(AT)

26 Then the Lord said to Moses, “Stretch out your hand over the sea so that the waters may flow back over the Egyptians and their chariots and horsemen.” 27 Moses stretched out his hand over the sea, and at daybreak the sea went back to its place.(AU) The Egyptians were fleeing toward[c] it, and the Lord swept them into the sea.(AV) 28 The water flowed back and covered the chariots and horsemen—the entire army of Pharaoh that had followed the Israelites into the sea.(AW) Not one of them survived.(AX)

29 But the Israelites went through the sea on dry ground,(AY) with a wall(AZ) of water on their right and on their left. 30 That day the Lord saved(BA) Israel from the hands of the Egyptians, and Israel saw the Egyptians lying dead on the shore. 31 And when the Israelites saw the mighty hand(BB) of the Lord displayed against the Egyptians, the people feared(BC) the Lord and put their trust(BD) in him and in Moses his servant.

Footnotes

  1. Exodus 14:9 Or charioteers; also in verses 17, 18, 23, 26 and 28
  2. Exodus 14:25 See Samaritan Pentateuch, Septuagint and Syriac; Masoretic Text removed
  3. Exodus 14:27 Or from