Add parallel Print Page Options

Babuloni, Lupanga la Mulungu

21 Yehova anandiyankhula nati: “Iwe mwana wa munthu, tembenuka uyangʼane ku Yerusalemu ndipo ulalike mawu odzudzula malo ake opatulika. Unenere zodzudzula anthu a ku Yerusalemu. Uwawuze kuti, Ambuye Yehova akuti, ‘Taona, Ine ndidzalimbana nawe. Ndidzasolola lupanga langa mʼchimake ndi kuwononga anthu olungama ndi ochimwa omwe. Motero ndidzapha aliyense kuchokera kummawa mpaka kumpoto. Pamenepo anthu onse adzadziwa kuti Ine Yehova ndi amene ndasolola lupanga langa mʼchimake; sindidzalilowetsanso mʼchimakemo.’

“Tsono iwe mwana wa munthu, buwula. Buwula pamaso pawo ndi mtima wosweka ndi wachisoni chachikulu. Ndipo akadzakufunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani ukubuwula?’ Iwe udzayankhe kuti, ‘Ndikubuwula chifukwa cha nkhani imene ndamva. Zikadzachitika zimenezi, mitima yonse idzangoti fumu, manja onse adzangolefuka, mpweya wawo udzawathera, ndipo mawondo onse adzangoti zii.’ Izi zikubwera! Ndipo zidzachitika ndithu, akutero Ambuye Yehova.”

Yehova anandiyankhulanso kuti, “Iwe mwana wa munthu, unenere ndipo unene kuti, Ambuye Yehova akuti,

“Izi ndi zimene Yehova akunena:
    Lupanga, lupanga, lanoledwa ndipo lapukutidwa.
10 Lanoledwa kuti likaphe,
    lapukutidwa kuti lingʼanime ngati mphenzi!

“ ‘Kodi tingakondwere bwanji? Wanyoza ndodo, mwana wanga ndi chilichonse cha mtengo.

11 “ ‘Lupanga laperekedwa kuti lipukutidwe,
    ndi kuti linyamulidwe,
lanoledwa ndi kupukutidwa,
    kuti liperekedwe mʼmanja mwa munthu amene amapha.
12 Fuwula ndi kulira, iwe mwana wa munthu,
    pakuti zimenezi zidzagwera anthu anga;
    zidzagweranso akalonga onse a Israeli.
Adzaphedwa ndi lupanga
    pamodzi ndi anthu anga.
Chifukwa chake udzigugude pa chifuwa ndi chisoni.

13 “ ‘Ambuye Wamphamvuzonse akuti: Ndikuwayesa anthu anga, ndipo ngati satembenuka mtima, ndiye kuti zimenezi sizidzalephera kuwagwera.’

14 “Tsono mwana wa munthu, nenera
    ndipo uwombe mʼmanja.
Lupanga likanthe kawiri
    ngakhale katatu.
Limenelo ndilo lupanga lophera anthu.
    Inde ndilodi lupanga lophera anthu koopsa
    limene likuwazungulira.
15 Ndawayikira pa zipata zawo zonse
    lupanga laphuliphuli
kuti ataye mtima
    ndiponso kuti anthu ambiri agwe.
Aa! Lapangidwa lupanga kuti lizingʼanima ngati mphenzi
    ndi kuti azilisolola kuphera anthu.
16 Iwe lupanga, ipha anthu kumanja,
    kenaka kumanzere,
    kulikonse kumene msonga yako yaloza.
17 Inenso ndidzawomba mʼmanja mwanga,
    ndipo ndidzaziziritsa ukali wanga
Ine Yehova ndayankhula.”

18 Yehova anandiyankhulanso kuti, 19 “Iwe mwana wa munthu, ulembe zizindikiro za misewu iwiri imene lupanga la mfumu ya ku Babuloni lingathe kudzeramo. Misewu yonse ikhale yochokera mʼdziko limodzi. Ika chikwangwani pa mphambano yopita mu mzinda. 20 Ulembe chizindikiro pa msewu umene lupanga lidzadzere popita ku Raba wa ku Amoni, ndiponso ku Yuda ndi ku Yerusalemu, mzinda wotetezedwa. 21 Pakuti mfumu ya ku Babuloni yayima pa msewu, pa mphambano ya misewu iwiriyo. Ikuwombeza ndi mivi yake kuti idziwe njira yoyenera kudzeramo. Ikupempha nzeru kwa milungu yake ndipo ikuyangʼana chiwindi cha nyama yoperekedwa ku nsembe. 22 Mʼdzanja lake lamanja muli muvi waula wolembedwa Yerusalemu. Kumeneko mfumuyo idzayika zida zogumulira, idzalamula kupha anthu ndiponso kufuwula mfuwu wa nkhondo. Mfumuyo idzapanga zida zogumulira makoma, kuwunda mitumbira ya nkhondo ndi kumanga nsanja za nkhondo. 23 Koma kwa anthu a ku Yerusalemu zidzaoneka ngati zowombeza zabodza chifukwa cha malumbiro amene anachita kwa mfumuyo. Koma mfumuyo idzawakumbutsa za zolakwa zawo kuti atengedwe ku ukapolo.

24 “Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti, ‘Popeza mwandikumbutsa zolakwa, moti kundiwukira kwanu kwaonekera poyera ndi kuti mu zochita zanu zonse mukuonetsa machimo anu, nʼchifukwa chake mudzagwidwa ndi kutengedwa ukapolo.

25 “ ‘Tsono iwe kalonga wonyozedwa ndi woyipa wa Israeli, amene tsiku lako lafika, amene nthawi yako yolangidwa yafika penipeni, 26 Ambuye Yehova akuti: Vula nduwira, chotsa chipewa chaufumu. Zinthu sizidzakhala monga zinalili: anthu wamba adzakwezedwa ndipo okwezedwa adzatsitsidwa. 27 Chipasupasu! Chipasupasu! Ine ndidzawupasula mzindawo! Ndipo sadzawumanganso mpaka atafika amene ali woyenera kuwulandira; Ine ndidzawupereka kwa iyeyo.’

28 “Ndipo iwe mwana wa munthu, nenera kuti, ponena za Aamoni ndi zonyoza zawo, Ambuye Yehova akuti,

“ ‘Lupanga, lupanga,
    alisolola kuti liphe anthu,
alipukuta kuti liwononge
    ndi kuti lingʼanime ngati mphenzi.
29 Zimene akuti akuona mʼmasomphenya zokhudza inu ndi zabodza.
    Mawula awo okhudza inu ndi abodzanso.
Mudzakhala pamodzi ndi anthu oyipa
    amene tsiku lawo lafika,
ndiye kuti nthawi
    ya kulangidwa kwawo komaliza.

30 “ ‘Bwezerani lupanga mʼchimake.
    Ku malo kumene inu munabadwira,
mʼdziko la makolo anu,
    ndidzakuweruzani.
31 Ndidzakhuthula ukali wanga pa inu,
    ndipo mkwiyo wanga udzakuyakirani.
Ndidzakuperekani mʼmanja mwa anthu ankhanza;
    anthu odziwa bwino kuwononga zinthu.
32 Mudzakhala ngati nkhuni pa moto.
    Ena adzakhetsa magazi anu mʼdziko lanu lomwe.
Simudzakumbukiridwanso
    pakuti Ine Yehova ndayankhula.’ ”

Babylon as God’s Sword of Judgment

21 [a]The word of the Lord came to me:(A) “Son of man, set your face against(B) Jerusalem and preach against the sanctuary.(C) Prophesy against(D) the land of Israel and say to her: ‘This is what the Lord says: I am against you.(E) I will draw my sword(F) from its sheath and cut off from you both the righteous and the wicked.(G) Because I am going to cut off the righteous and the wicked, my sword(H) will be unsheathed against everyone from south to north.(I) Then all people will know that I the Lord have drawn my sword(J) from its sheath; it will not return(K) again.’(L)

“Therefore groan, son of man! Groan before them with broken heart and bitter grief.(M) And when they ask you, ‘Why are you groaning?(N)’ you shall say, ‘Because of the news that is coming. Every heart will melt with fear(O) and every hand go limp;(P) every spirit will become faint(Q) and every leg will be wet with urine.’(R) It is coming! It will surely take place, declares the Sovereign Lord.”

The word of the Lord came to me: “Son of man, prophesy and say, ‘This is what the Lord says:

“‘A sword, a sword,
    sharpened and polished—
10 sharpened for the slaughter,(S)
    polished to flash like lightning!

“‘Shall we rejoice in the scepter of my royal son? The sword despises every such stick.(T)

11 “‘The sword is appointed to be polished,(U)
    to be grasped with the hand;
it is sharpened and polished,
    made ready for the hand of the slayer.
12 Cry out and wail, son of man,
    for it is against my people;
    it is against all the princes of Israel.
They are thrown to the sword
    along with my people.
Therefore beat your breast.(V)

13 “‘Testing will surely come. And what if even the scepter, which the sword despises, does not continue? declares the Sovereign Lord.’

14 “So then, son of man, prophesy
    and strike your hands(W) together.
Let the sword strike twice,
    even three times.
It is a sword for slaughter—
    a sword for great slaughter,
    closing in on them from every side.(X)
15 So that hearts may melt with fear(Y)
    and the fallen be many,
I have stationed the sword for slaughter[b]
    at all their gates.
Look! It is forged to strike like lightning,
    it is grasped for slaughter.(Z)
16 Slash to the right, you sword,
    then to the left,
    wherever your blade is turned.
17 I too will strike my hands(AA) together,
    and my wrath(AB) will subside.
I the Lord have spoken.(AC)

18 The word of the Lord came to me: 19 “Son of man, mark out two roads for the sword(AD) of the king of Babylon to take, both starting from the same country. Make a signpost(AE) where the road branches off to the city. 20 Mark out one road for the sword to come against Rabbah of the Ammonites(AF) and another against Judah and fortified Jerusalem. 21 For the king of Babylon will stop at the fork in the road, at the junction of the two roads, to seek an omen: He will cast lots(AG) with arrows, he will consult his idols,(AH) he will examine the liver.(AI) 22 Into his right hand will come the lot for Jerusalem, where he is to set up battering rams, to give the command to slaughter, to sound the battle cry,(AJ) to set battering rams against the gates, to build a ramp(AK) and to erect siege works.(AL) 23 It will seem like a false omen to those who have sworn allegiance to him, but he will remind(AM) them of their guilt(AN) and take them captive.

24 “Therefore this is what the Sovereign Lord says: ‘Because you people have brought to mind your guilt by your open rebellion, revealing your sins in all that you do—because you have done this, you will be taken captive.

25 “‘You profane and wicked prince of Israel, whose day has come,(AO) whose time of punishment has reached its climax,(AP) 26 this is what the Sovereign Lord says: Take off the turban, remove the crown.(AQ) It will not be as it was: The lowly will be exalted and the exalted will be brought low.(AR) 27 A ruin! A ruin! I will make it a ruin! The crown will not be restored until he to whom it rightfully belongs shall come;(AS) to him I will give it.’(AT)

28 “And you, son of man, prophesy and say, ‘This is what the Sovereign Lord says about the Ammonites(AU) and their insults:

“‘A sword,(AV) a sword,
    drawn for the slaughter,
polished to consume
    and to flash like lightning!
29 Despite false visions concerning you
    and lying divinations(AW) about you,
it will be laid on the necks
    of the wicked who are to be slain,
whose day has come,
    whose time of punishment has reached its climax.(AX)

30 “‘Let the sword return to its sheath.(AY)
    In the place where you were created,
in the land of your ancestry,(AZ)
    I will judge you.
31 I will pour out my wrath on you
    and breathe(BA) out my fiery anger(BB) against you;
I will deliver you into the hands of brutal men,
    men skilled in destruction.(BC)
32 You will be fuel for the fire,(BD)
    your blood will be shed in your land,
you will be remembered(BE) no more;
    for I the Lord have spoken.’”

Footnotes

  1. Ezekiel 21:1 In Hebrew texts 21:1-32 is numbered 21:6-37.
  2. Ezekiel 21:15 Septuagint; the meaning of the Hebrew for this word is uncertain.