Add parallel Print Page Options

Chionetsero cha Kuzingidwa kwa Yerusalemu

Mulungu anati, “Iwe mwana wa munthu, tsopano tenga njerwa, uliyike pamaso pako ndipo ujambulepo chithunzi cha mzinda wa Yerusalemu. Ndipo uwuzinge mzindawo motere: uwumangire nsanja zowuzinga, uwumbire mitumbira ya nkhondo, uwumangire misasa ya nkhondo ndipo uyike zida zogumulira kuzungulira mzindawo. Kenaka utenge chiwaya chachitsulo uchiyike ngati khoma lachitsulo pakati pa iwe ndi mzindawo. Uyangʼanitsitse mzindawo ndipo udzakhala wozingidwa ndi nsanja za nkhondo. Choncho umangire nsanja zankhondo. Chimenechi chidzakhala chizindikiro kwa Aisraeli.

“Tsono iwe ugonere kumanzere kwako ndipo ndidzayika pa iwe tchimo la Aisraeli. Iwe udzasenza tchimolo masiku onse amene udzagonere mbali imeneyo. Ine ndakuyikira masiku okwana 390 malingana ndi zaka za machimo awo. Umu ndi mmene udzasenzere machimo a Aisraeli.

“Utatha zimenezo udzagonerenso mbali ya kudzanja lamanja, ndipo udzasenza machimo a anthu a ku Yuda masiku makumi anayi, tsiku lililonse kuyimira chaka chimodzi. Tsono udzayangʼanitsitse nsanja za nkhondo zozinga. Dzanja la mkanjo wako utalikwinya ndi dzanja lako utakweza, udzalosere modzudzula Yerusalemu. Ine ndidzakumanga ndi zingwe kotero kuti sudzatha kutembenukira uku ndi uku mpaka utatsiriza masiku akuzingidwa ako.

“Tsono tenga tirigu ndi barele, nyemba ndi mphodza, mapira ndi mchewere; ndipo uyike zonsezi mʼmbale imodzi ndipo upange buledi wako. Uzidya pa masiku 390 amene udzakhala ukugonera mbali imodzi. 10 Uyeze theka la kilogalamu la chakudyacho kuti uzidya tsiku lililonse kamodzi kokha. 11 Uyezenso zikho ziwiri zamadzi ndipo uzimwa tsiku ndi tsiku. 12 Uzidya chakudya chako ngati momwe amadyera keke ya barele. Uzidzaphika chakudyacho anthu akuona pogwiritsa ntchito ndowe ya munthu ngati nkhuni.” 13 Yehova anati, “Chimodzimodzi anthu a Israeli adzadya chakudya chodetsedwa ku mayiko achilendo kumene Ine ndidzawapirikitsira.”

14 Koma ine ndinati, “Zisatero, Ambuye Yehova! Ine sindinadziyipitsepo pa zachipembedzo. Kuyambira ubwana wanga mpaka tsopano, sindinadyepo kanthu kalikonse kopezeka katafa kapena kophedwa ndi zirombo za kutchire. Palibe nyama yodetsedwa pa zachipembedzo imene inalowa pakamwa panga.”

15 Iye anati, “Chabwino, ndidzakulola kuti uphike buledi wako ndi ndowe za ngʼombe mʼmalo mwa ndowe za munthu.”

16 Pambuyo pake anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, anthu a ku Yerusalemu ndidzawachepetsera chakudya. Anthuwo adzadya chakudya chochita kuyeza ndipo azidzadya mwa nkhawa. Azidzamwanso madzi ochita kuyeza ndiponso mwa mantha. 17 Ndidzachita zimenezi kuti adzasowe chakudya ndi madzi. Choncho adzachita nkhawa akumapenyana ndipo adzatheratu ndi kuwonda chifukwa cha machimo awo.”

Siege of Jerusalem Symbolized

“Now, son of man, take a block of clay, put it in front of you and draw the city of Jerusalem on it. Then lay siege to it: Erect siege works against it, build a ramp(A) up to it, set up camps against it and put battering rams around it.(B) Then take an iron pan,(C) place it as an iron wall between you and the city and turn your face toward(D) it. It will be under siege, and you shall besiege it. This will be a sign(E) to the people of Israel.(F)

“Then lie on your left side and put the sin of the people of Israel upon yourself.[a] You are to bear their sin for the number of days you lie on your side. I have assigned you the same number of days as the years of their sin. So for 390 days you will bear the sin of the people of Israel.

“After you have finished this, lie down again, this time on your right side, and bear the sin(G) of the people of Judah. I have assigned you 40 days, a day for each year.(H) Turn your face(I) toward the siege of Jerusalem and with bared arm prophesy against her. I will tie you up with ropes so that you cannot turn from one side to the other until you have finished the days of your siege.(J)

“Take wheat and barley, beans and lentils, millet and spelt;(K) put them in a storage jar and use them to make bread for yourself. You are to eat it during the 390 days you lie on your side. 10 Weigh out twenty shekels[b](L) of food to eat each day and eat it at set times. 11 Also measure out a sixth of a hin[c] of water and drink it at set times.(M) 12 Eat the food as you would a loaf of barley bread; bake it in the sight of the people, using human excrement(N) for fuel.” 13 The Lord said, “In this way the people of Israel will eat defiled food among the nations where I will drive them.”(O)

14 Then I said, “Not so, Sovereign Lord!(P) I have never defiled myself. From my youth until now I have never eaten anything found dead(Q) or torn by wild animals. No impure meat has ever entered my mouth.(R)

15 “Very well,” he said, “I will let you bake your bread over cow dung instead of human excrement.”

16 He then said to me: “Son of man, I am about to cut off(S) the food supply in Jerusalem. The people will eat rationed food in anxiety and drink rationed water in despair,(T) 17 for food and water will be scarce.(U) They will be appalled at the sight of each other and will waste away because of[d] their sin.(V)

Footnotes

  1. Ezekiel 4:4 Or upon your side
  2. Ezekiel 4:10 That is, about 8 ounces or about 230 grams
  3. Ezekiel 4:11 That is, about 2/3 quart or about 0.6 liter
  4. Ezekiel 4:17 Or away in