Add parallel Print Page Options

12 Efereimu amadya mpweya;
    tsiku lonse amasaka mphepo ya kummawa
    ndipo amachulukitsa mabodza ndi chiwawa.
Amachita mgwirizano ndi Asiriya
    ndipo amatumiza mphatso za mafuta a olivi ku Igupto.
Yehova akuyimba mlandu Yuda;
    Iye adzalanga Yakobo molingana ndi makhalidwe ake,
    adzamulanga molingana ndi ntchito zake.
Akali mʼmimba mwa amayi ake, Yakobo anagwira chidendene cha mʼbale wake;
    iye atakula analimbana ndi Mulungu.
Yakobo analimbana ndi mngelo ndipo anapambana;
    analira napempha kuti amukomere mtima.
Mulungu anakumana naye ku Beteli
    ndipo anayankhula naye kumeneko,
Yehova Mulungu Wamphamvuzonse,
    Yehova ndiye dzina lake lotchuka!
Koma inu muyenera kubwerera kwa Mulungu wanu;
    pitirizani chikondi ndi chiweruzo cholungama,
    ndipo muzidikira Mulungu wanu nthawi zonse.

Munthu wamalonda amagwiritsa ntchito masikelo achinyengo;
    iyeyo amakonda kubera anthu.
Efereimu amadzitama ponena kuti,
    “Ndine wolemera kwambiri; ndili ndi chuma chambiri.
Palibe amene angandiloze chala
    chifukwa cha kulemera kwanga.”

“Ine ndine Yehova Mulungu wako
    amene ndinakutulutsa mu Igupto.
Ndidzakukhazikaninso mʼmatenti,
    monga munkachitira masiku aja pa nthawi ya zikondwerero zanu.
10 Ndinayankhula ndi aneneri,
    ndinawaonetsa masomphenya ambiri,
    ndipo ndinawawuza mafanizo kudzera mwa iwo.”

11 Kodi Giliyadi ndi woyipa?
    Anthu ake ndi achabechabe!
Kodi amapereka nsembe za ngʼombe zazimuna ku Giligala?
    Maguwa awo ansembe adzakhala ngati milu ya miyala
    mʼmunda molimidwa.
12 Yakobo anathawira ku dziko la Aramu,
    Israeli anagwira ntchito kuti apeze mkazi,
    ndipo anaweta nkhosa kuti akwatire mkaziyo.
13 Yehova anagwiritsa ntchito mneneri kuti atulutse Israeli mu Igupto;
    kudzera mwa mneneriyo Iye anawasamalira.
14 Koma Efereimu wamukwiyitsa kwambiri.
    Nʼchifukwa chake Yehova adzawalanga ndi imfa.
    Adzawalanga chifukwa anamuchititsa manyazi kwambiri.