Add parallel Print Page Options

Pamene ndichiritsa Israeli,
machimo a Efereimu amaonekera poyera
    ndiponso milandu ya Samariya sibisika.
Iwo amachita zachinyengo,
    mbala zimathyola nyumba,
    achifwamba amalanda anthu katundu mʼmisewu.
Koma sazindikira kuti Ine
    ndimakumbukira zoyipa zawo zonse.
Azunguliridwa ndi zolakwa zawo;
    ndipo sizichoka mʼmaso mwanga.

“Anthuwa amasangalatsa mfumu ndi zoyipa zawozo,
    akalonga amasekerera mabodza awo.
Onsewa ndi anthu azigololo,
    otentha ngati moto wa mu uvuni,
umene wophika buledi sasonkhezera
    kuyambira pamene akukanda buledi mpaka atafufuma.
Pa tsiku la chikondwerero cha mfumu yathu
    akalonga amaledzera ndi vinyo,
    ndipo amalowa mʼgulu la anthu achipongwe.
Mitima yawo ili ngati uvuni;
    amayandikira Mulungu mwachiwembu.
Ukali wawo umanyeka usiku wonse,
    mmawa umayaka ngati malawi a moto.
Onsewa ndi otentha ngati uvuni,
    amapha olamulira awo.
Mafumu awo onse amagwa,
    ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amandiyitana Ine.

“Efereimu wasakanikirana ndi mitundu ya anthu ena;
    Efereimu ndi buledi amene wapsa mbali imodzi.
Alendo atha mphamvu zake,
    koma iye sakuzindikira.
Tsitsi lake layamba imvi
    koma iye sakudziwa.
10 Kunyada kwake Israeli kukumutsutsa,
    koma pa zonsezi
iye sakubwerera kwa Yehova Mulungu wake
    kapena kumufunafuna.

11 “Efereimu ali ngati nkhunda
    yopusa yopanda nzeru.
Amayitana Igupto
    namapita ku Asiriya.
12 Akamadzapita, ndidzawakola ndi ukonde wanga;
    ndidzawagwetsa pansi ngati mbalame zamumlengalenga.
Ndikadzamva kuti asonkhana pamodzi
    ndidzawakola.
13 Tsoka kwa iwo,
    chifukwa andisiya Ine!
Chiwonongeko kwa iwo,
    chifukwa andiwukira!
Ndimafunitsitsa kuwapulumutsa
    koma amayankhula za Ine monama.
14 Iwo salirira kwa Ine kuchokera pansi pa mtima,
    koma amalira mofuwula ali pa bedi pawo.
Amadzichekacheka chifukwa chofuna tirigu ndi vinyo watsopano,
    koma amandifulatira.
15 Ine ndinawaphunzitsa ndikuwalimbitsa,
    koma amandikonzera chiwembu.
16 Iwo satembenukira kwa Wammwambamwamba;
    ali ngati uta woonongeka.
Atsogoleri awo adzaphedwa ndi lupanga
    chifukwa cha mawu awo achipongwe.
Motero iwo adzasekedwa
    mʼdziko la Igupto.