Add parallel Print Page Options

Kuyeretsedwa ku Nthenda ya Khate

14 Yehova anawuza Mose kuti, “Malamulo a munthu wakhate pa tsiku la kuyeretsedwa kwake ndi awa: Abwere naye kwa wansembe. Wansembe atuluke kunja kwa msasa ndipo amuonetsetse wodwalayo. Ngati munthu wakhateyo wachira, wansembe alamule anthu kuti amutengere wodwala woti ayeretsedweyo, mbalame zamoyo ziwiri zomwe Ayuda amaloledwa kudya, nthambi yamkungudza, kansalu kofiirira ndi kanthambi ka hisope. Wansembe alamule anthuwo kuti mbalame imodzi ayiphere mu mʼphika wa dothi pamwamba pa madzi abwino. Kenaka wansembe atenge mbalame yamoyo ija ndi kuyinyika pamodzi ndi nthambi yamkungudza, kansalu kofiirira ndi kanthambi ka hisope kaja mʼmagazi ambalame imene anayiphera pamwamba pa madzi abwino. Wansembe awaze magazi kasanu ndi kawiri pa munthu woti amuyeretse khateyo ndipo alengeze kuti munthuyo ndi woyeretsedwa. Kenaka wansembe awulutsire ku thengo mbalame yamoyoyo.

“Munthu amene wayeretsedwa uja achape zovala zake, amete tsitsi lake lonse, ndipo asambe mʼmadzi. Akatero adzakhala woyeretsedwa. Atatha zimenezi munthuyo apite ku msasa wake koma akhale kunja kwa msasawo kwa masiku asanu ndi awiri. Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri amete tsitsi lake lonse: amete kumutu, ndevu zake, nsidze zake pamodzi ndi tsitsi lina lonse. Kenaka achape zovala zake ndi kusamba mʼmadzi, ndipo adzakhala woyeretsedwa.

10 “Pa tsiku lachisanu ndi chitatu munthuyo atenge ana ankhosa aamuna awiri ndi mwana wankhosa wamkazi wa chaka chimodzi. Zonsezi zikhale zopanda chilema. Atengenso chopereka chachakudya cha ufa wosalala wa makilogalamu atatu wosakaniza ndi mafuta wokwana limodzi mwa magawo atatu a lita. 11 Wansembe amene ati ayeretse munthu wodwalayo amuyimitse munthuyo ali ndi zopereka zake zonse pamaso pa Yehova pa khomo la tenti ya msonkhano.

12 “Ndipo wansembe atenge mwana wankhosa wamwamuna mmodzi ndi kumupereka kuti akhale nsembe yopepesera kupalamula, pamodzi ndi mafuta wokwana limodzi mwa magawo atatu a lita. Wansembe aziweyule zonsezi pamaso pa Yehova kuti zikhale chopereka choweyula. 13 Mwana wankhosayo amuphere pa malo amene amaphera nsembe yopepesera machimo ndi nsembe yopsereza, kutanthauza malo opatulika. Monga zimakhalira ndi chopereka chopepesera machimo, chopereka ichi ndi chake cha wansembe ndipo ndi chopereka choyera kopambana. 14 Wansembe atengeko magazi a nsembe yopepesera kupalamula ndi kuwapaka pa msonga pa khutu lakumanja la munthu woti ayeretsedweyo. Apakenso pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja, ndi chala chachikulu cha ku phazi lakumanja. 15 Wansembe atengeko mafuta pangʼono, nʼkuwathira mʼdzanja lake lamanzere, 16 aviyike chala chake cha ku dzanja lamanja mʼmafuta amene ali mʼdzanja lamanzerewo, ndi kuwaza mafutawo ndi chala chakecho kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova. 17 Wansembe apake mafuta otsala mʼdzanja lake pa khutu lakumanja la munthu amene akuyeretsedwayo. Awapakenso pa chala chake chachikulu cha ku dzanja lamanja ndiponso pa chala chake chachikulu cha ku phazi lakumanja, pamalo pamene anali atapakapo magazi a nsembe yopepesera kupalamula paja. 18 Mafuta onse otsala mʼdzanja la wansembe awathire pamutu pa munthu woti ayeretsedwe uja, ndipo potero adzachita mwambo womupepesera pamaso pa Yehova.

19 “Kenaka wansembe apereke nsembe yopepesera machimo kuti achite mwambo womupepesera munthu woti ayeretsedwe khate lake uja. Atatha kuchita zimenezi, wansembe aphe nyama ya nsembe yopsereza 20 ndi kuyipereka pa guwa, pamodzi ndi nsembe yachakudya. Akatero ndiye kuti wansembe wachita mwambo wopepesera munthu wodzayeretsedwayo, ndipo adzakhala woyera.

21 “Ngati munthu woti ayeretsedweyo ndi wosauka ndipo sangathe kupeza zinthu zimenezi, apereke mwana wankhosa wamwamuna monga nsembe yopepesera kupalamula ndipo ayiweyule pochita mwambo womupepesera. Aperekenso kilogalamu imodzi ya ufa wosalala osakaniza ndi mafuta kuti ikhale nsembe yachakudya, pamodzi ndi mafuta wokwanira limodzi mwa magawo atatu a lita. 22 Aperekenso njiwa ziwiri kapena mawunda awiri zomwe iye angathe kuzipeza. Imodzi ikhale nsembe yopepesera machimo, ndi inayo ikhale ya nsembe yopsereza.

23 “Pa tsiku lachisanu ndi chitatu zonsezo abwere nazo kwa wansembe, pa khomo pa tenti ya msonkhano, pamaso pa Yehova kuti munthuyo ayeretsedwe. 24 Wansembe atenge mwana wankhosa wopereka nsembe yopepesera kupalamula, pamodzi ndi mafuta aja, ndipo aziweyule kuti zikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova. 25 Wansembe aphe nkhosa yopereka nsembe yopepesera kupalamula ndipo atenge magazi ake ndi kuwapaka pa msonga ya khutu lakumanja la munthu amene ayeretsedweyo. Awapakenso pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja, ndiponso pa chala chachikulu cha ku phazi lakumanja. 26 Kenaka wansembe athire mafuta mʼdzanja lake lamanzere, 27 ndipo ndi chala chake cha ku dzanja lamanja awaze mafutawo kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova. 28 Apakenso mafuta omwewo amene ali mʼdzanja lake lamanja pa msonga ya khutu la kudzanja lamanja la munthu amene akuyeretsedwayo. Apakenso pa chala chachikulu cha phazi lakumanja, pamalo pamene anapakapo magazi a nsembe yopepesera kupalamula. 29 Mafuta onse otsala amene ali mʼdzanja la wansembe awapake pamutu pa munthu amene ayeretsedweyo kuti amuchitire mwambo wopepesera machimo pamaso pa Yehova. 30 Ndipo munthuyo apereke njiwa ziwiri kapena mawunda ankhunda awiri, molingana ndi mmene anapezeramo, 31 imodzi ikhale ya nsembe yopepesera machimo ndipo inayo ikhale ya nsembe yopsereza, pamodzi ndi chopereka chachakudya. Akatero ndiye kuti wansembe wachita mwambo wopepesera machimo a munthu woti ayeretsedwe.

32 “Amenewa ndi malamulo a munthu wakhate amene alibe zinthu zoti apereke pamene akuyeretsedwa.

Za Ndere za Mʼnyumba

33 “Yehova anawuza Mose ndi Aaroni kuti, 34 Mukakalowa mʼdziko la Kanaani limene ndikukupatsani kuti likhale lanu, ndipo Ine ndikakabweretsa ndere zoyanga mʼnyumba mʼdziko limenelo, 35 mwini wake nyumbayo adzapite kwa wansembe ndi kukamuwuza kuti, ‘Ndaona chinthu chooneka ngati ndere mʼnyumba mwanga.’ 36 Tsono wansembe alamule kuti anthu atulutse zinthu zonse mʼnyumbamo iye asanalowemo ndi kukaonetsetsa ndereyo kuti mʼnyumbamo musapezeke chinthu choti achitchule chodetsedwa. Izi zitachitika, wansembe alowe mʼnyumbamo ndi kukaonamo. 37 Iye aonetsetse nderezo. Tsono akapeza kuti nderezo zili mʼkhoma la nyumba, ndipo ngati zili ndi mawanga obiriwira kapena ofiirira, komanso zikuoneka kuti zalowerera mpaka mʼkati mwa khoma, 38 wansembe atuluke mʼnyumbamo ndi kupita pa khomo, ndipo ayitseke nyumbayo masiku asanu ndi awiri. 39 Pa tsiku la chisanu ndi chiwiri wansembe abwerenso kudzayangʼana mʼnyumbamo. Ngati ndere yafalikira mʼmakoma a nyumbayo, 40 wansembe alamule kuti anthu agumule miyala imene muli nderezo ndipo akayitaye kudzala la kunja kwa mzinda. 41 Wansembe awuze anthu kuti apale makoma onse a mʼkati mwa nyumbayo, ndipo zopalidwazo akazitaye ku malo odetsedwa a kunja kwa mudzi. 42 Tsono anthuwo atenge miyala ina ndi kuyilowetsa mʼmalo mwa miyala imene anagumula ija ndipo atenge dothi latsopano ndi kumata nyumbayo.

43 “Ngati ndere iwonekanso mʼnyumbamo atagumula kale miyala ndiponso atayipala kale ndi kuyimatanso, 44 wansembe apite kukayionetsetsenso ndipo ngati nderezo zafalikira mʼnyumbamo, ndiye kuti ndere zimenezo ndi zoopsa. Nyumba imeneyo ndi yodetsedwa. 45 Agwetse nyumbayo, ndipo miyala yake, matabwa pamodzi ndi dothi lake lonse, zonse akazitaye kudzala lodetsedwa, kunja kwa mzinda.

46 “Aliyense amene alowa mʼnyumbamo itatsekedwa adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 47 Munthu amene wagona mʼnyumbamo kapena kudyeramo ayenera kuchapa zovala zake.

48 “Koma ngati pambuyo pa kuyimata, wansembe abwera kudzaonetsetsa mʼnyumbamo napeza kuti ndereyo sinafalikire, iye alengeze kuti nyumbayo ndi yoyeretsedwa, chifukwa ndereyo yatha. 49 Kuti nyumbayo iyeretsedwe, mwini wake atenge mbalame ziwiri, kanthambi kamkungudza, kansalu kofiirira ndi kachitsamba ka hisope. 50 Wansembe aphe mbalame imodzi pamwamba pa madzi abwino mu mʼphika wa dothi. 51 Kenaka atenge kanthambi kamkungudza, kachitsamba ka hisope, kansalu kofiirira pamodzi ndi mbalame yamoyo ija, zonsezi aziviyike mʼmagazi a mbalame yophedwa ija, ndiponso mʼmadzi abwino aja, ndipo awaze nyumbayo kasanu ndi kawiri 52 Akatero ndiye kuti wayeretsa nyumbayo ndi magazi a mbalame, madzi abwino, mbalame yamoyo, kanthambi kamkungudza, kachitsamba ka hisope ndi kansalu kofiirira. 53 Kenaka ayiwulutsire mbalame yamoyo ija kuthengo, kunja kwa mzinda. Pamenepo ndiye kuti wansembe wachita mwambo wopepesera nyumbayo, ndipo idzakhala yoyeretsedwa.”

54 Amenewa ndiwo malamulo a nthenda ya khate, bala lonyerenyetsa, 55 nguwi za pa zovala, ndere za mʼnyumba, 56 khate la chithupsa, khate la mʼbuko ndi khate la banga 57 kuti mudziwe ngati chinthucho ndi choyeretsedwa kapena chodetsedwa.

Amenewa ndiwo malamulo a nthenda zonse za khate.

Cleansing From Defiling Skin Diseases

14 The Lord said to Moses, “These are the regulations for any diseased person at the time of their ceremonial cleansing, when they are brought to the priest:(A) The priest is to go outside the camp and examine them.(B) If they have been healed of their defiling skin disease,[a](C) the priest shall order that two live clean birds and some cedar wood, scarlet yarn and hyssop(D) be brought for the person to be cleansed.(E) Then the priest shall order that one of the birds be killed over fresh water in a clay pot.(F) He is then to take the live bird and dip it, together with the cedar wood, the scarlet yarn and the hyssop, into the blood of the bird that was killed over the fresh water.(G) Seven times(H) he shall sprinkle(I) the one to be cleansed of the defiling disease, and then pronounce them clean. After that, he is to release the live bird in the open fields.(J)

“The person to be cleansed must wash their clothes,(K) shave off all their hair and bathe with water;(L) then they will be ceremonially clean.(M) After this they may come into the camp,(N) but they must stay outside their tent for seven days. On the seventh day(O) they must shave off all their hair;(P) they must shave their head, their beard, their eyebrows and the rest of their hair. They must wash their clothes and bathe themselves with water, and they will be clean.(Q)

10 “On the eighth day(R) they must bring two male lambs and one ewe lamb(S) a year old, each without defect, along with three-tenths of an ephah[b](T) of the finest flour mixed with olive oil for a grain offering,(U) and one log[c] of oil.(V) 11 The priest who pronounces them clean shall present(W) both the one to be cleansed and their offerings before the Lord at the entrance to the tent of meeting.(X)

12 “Then the priest is to take one of the male lambs and offer it as a guilt offering,(Y) along with the log of oil; he shall wave them before the Lord as a wave offering.(Z) 13 He is to slaughter the lamb in the sanctuary area(AA) where the sin offering[d] and the burnt offering are slaughtered. Like the sin offering, the guilt offering belongs to the priest;(AB) it is most holy. 14 The priest is to take some of the blood of the guilt offering and put it on the lobe of the right ear of the one to be cleansed, on the thumb of their right hand and on the big toe of their right foot.(AC) 15 The priest shall then take some of the log of oil, pour it in the palm of his own left hand,(AD) 16 dip his right forefinger into the oil in his palm, and with his finger sprinkle some of it before the Lord seven times.(AE) 17 The priest is to put some of the oil remaining in his palm on the lobe of the right ear of the one to be cleansed, on the thumb of their right hand and on the big toe of their right foot, on top of the blood of the guilt offering.(AF) 18 The rest of the oil in his palm the priest shall put on the head of the one to be cleansed(AG) and make atonement for them before the Lord.

19 “Then the priest is to sacrifice the sin offering and make atonement for the one to be cleansed from their uncleanness.(AH) After that, the priest shall slaughter the burnt offering 20 and offer it on the altar, together with the grain offering, and make atonement for them,(AI) and they will be clean.(AJ)

21 “If, however, they are poor(AK) and cannot afford these,(AL) they must take one male lamb as a guilt offering to be waved to make atonement for them, together with a tenth of an ephah[e] of the finest flour mixed with olive oil for a grain offering, a log of oil, 22 and two doves or two young pigeons,(AM) such as they can afford, one for a sin offering and the other for a burnt offering.(AN)

23 “On the eighth day they must bring them for their cleansing to the priest at the entrance to the tent of meeting,(AO) before the Lord.(AP) 24 The priest is to take the lamb for the guilt offering,(AQ) together with the log of oil,(AR) and wave them before the Lord as a wave offering.(AS) 25 He shall slaughter the lamb for the guilt offering and take some of its blood and put it on the lobe of the right ear of the one to be cleansed, on the thumb of their right hand and on the big toe of their right foot.(AT) 26 The priest is to pour some of the oil into the palm of his own left hand,(AU) 27 and with his right forefinger sprinkle some of the oil from his palm seven times before the Lord. 28 Some of the oil in his palm he is to put on the same places he put the blood of the guilt offering—on the lobe of the right ear of the one to be cleansed, on the thumb of their right hand and on the big toe of their right foot. 29 The rest of the oil in his palm the priest shall put on the head of the one to be cleansed, to make atonement for them before the Lord.(AV) 30 Then he shall sacrifice the doves or the young pigeons, such as the person can afford,(AW) 31 one as a sin offering and the other as a burnt offering,(AX) together with the grain offering. In this way the priest will make atonement before the Lord on behalf of the one to be cleansed.(AY)

32 These are the regulations for anyone who has a defiling skin disease(AZ) and who cannot afford the regular offerings(BA) for their cleansing.

Cleansing From Defiling Molds

33 The Lord said to Moses and Aaron, 34 “When you enter the land of Canaan,(BB) which I am giving you as your possession,(BC) and I put a spreading mold in a house in that land, 35 the owner of the house must go and tell the priest, ‘I have seen something that looks like a defiling mold in my house.’ 36 The priest is to order the house to be emptied before he goes in to examine the mold, so that nothing in the house will be pronounced unclean. After this the priest is to go in and inspect the house. 37 He is to examine the mold on the walls, and if it has greenish or reddish(BD) depressions that appear to be deeper than the surface of the wall, 38 the priest shall go out the doorway of the house and close it up for seven days.(BE) 39 On the seventh day(BF) the priest shall return to inspect the house. If the mold has spread on the walls, 40 he is to order that the contaminated stones be torn out and thrown into an unclean place outside the town.(BG) 41 He must have all the inside walls of the house scraped and the material that is scraped off dumped into an unclean place outside the town. 42 Then they are to take other stones to replace these and take new clay and plaster the house.

43 “If the defiling mold reappears in the house after the stones have been torn out and the house scraped and plastered, 44 the priest is to go and examine it and, if the mold has spread in the house, it is a persistent defiling mold; the house is unclean.(BH) 45 It must be torn down—its stones, timbers and all the plaster—and taken out of the town to an unclean place.

46 “Anyone who goes into the house while it is closed up will be unclean till evening.(BI) 47 Anyone who sleeps or eats in the house must wash their clothes.(BJ)

48 “But if the priest comes to examine it and the mold has not spread after the house has been plastered, he shall pronounce the house clean,(BK) because the defiling mold is gone. 49 To purify the house he is to take two birds and some cedar wood, scarlet yarn and hyssop.(BL) 50 He shall kill one of the birds over fresh water in a clay pot.(BM) 51 Then he is to take the cedar wood, the hyssop,(BN) the scarlet yarn and the live bird, dip them into the blood of the dead bird and the fresh water, and sprinkle the house seven times.(BO) 52 He shall purify the house with the bird’s blood, the fresh water, the live bird, the cedar wood, the hyssop and the scarlet yarn. 53 Then he is to release the live bird in the open fields(BP) outside the town. In this way he will make atonement for the house, and it will be clean.(BQ)

54 These are the regulations for any defiling skin disease,(BR) for a sore, 55 for defiling molds(BS) in fabric or in a house, 56 and for a swelling, a rash or a shiny spot,(BT) 57 to determine when something is clean or unclean.

These are the regulations for defiling skin diseases and defiling molds.(BU)

Footnotes

  1. Leviticus 14:3 The Hebrew word for defiling skin disease, traditionally translated “leprosy,” was used for various diseases affecting the skin; also in verses 7, 32, 54 and 57.
  2. Leviticus 14:10 That is, probably about 11 pounds or about 5 kilograms
  3. Leviticus 14:10 That is, about 1/3 quart or about 0.3 liter; also in verses 12, 15, 21 and 24
  4. Leviticus 14:13 Or purification offering; also in verses 19, 22 and 31
  5. Leviticus 14:21 That is, probably about 3 1/2 pounds or about 1.6 kilograms