Add parallel Print Page Options

Yehova anawuza Mose kuti, “Ngati munthu wina aliyense achimwa, nachita zinthu mosakhulupirika kwa Yehova chifukwa cha kunyenga mnzake pokana kumubwezera zimene anamusungitsa, kapena kumubera kapenanso kumulanda, kapena ndi kunama kuti sanatole chinthu chimene chinatayika, kapena kulumbira mwachinyengo pa chinthu chilichonse chimene munthu akachita amachimwa nacho, ndi wopalamula ndithu, ndipo ayenera kubweza zimene anabazo, zimene analanda mwachinyengozo, zimene anamusungitsazo, zimene anatolazo kapena zimene analumbira monyengazo. Pa tsiku limene apezeke kuti wapalamuladi, iye ayenera kumubwezera mwini wake zinthu zonsezi ndi kuwonjezerapo chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse. Pambuyo pake apereke kwa Yehova nsembe yopalamula. Nsembe yake ikhale nkhosa yayimuna yopanda chilema ndipo mtengo wake wogwirizana ndi nsembe yopepesera machimo. Kenaka wansembe achite mwambo wopepesera tchimo la munthuyo pamaso pa Yehova, ndipo adzakhululukidwa chilichonse chomwe anachita kuti akhale wopalamula.”

Nsembe Yopsereza

Yehova anawuza Mose kuti, “Lamula Aaroni ndi ana ake kuti, ‘Lamulo la nsembe yopsereza ndi ili: Nsembe yopserezayo izikhala pa moto pa guwa usiku wonse mpaka mmawa, ndipo moto wa paguwapo uzikhala ukuyaka nthawi zonse. 10 Tsono wansembe avale mkanjo wake wa nsalu yofewa ndi yosalala. Mʼkati avalenso kabudula wofewa, wosalala. Pambuyo pake atenge phulusa la nyama imene yatenthedwa pa guwa lansembe paja ndi kulithira pambali pa guwa lomwelo. 11 Akatero avule zovala zakezo ndi kuvala zovala zina. Kenaka atulutse phulusalo ndi kukaliyika pa malo woyeretsedwa kunja kwa chithando. 12 Moto wa pa guwa uzikhala ukuyaka nthawi zonse, usamazime. Mmawa uliwonse wansembe aziwonjezerapo nkhuni pa motopo ndi kukonza nsembe yopsereza, ndi kutentha mafuta a nsembe yachiyanjano pamenepo. 13 Moto uzikhala ukuyaka pa guwa nthawi zonse ndipo usazimepo.

Nsembe Zachakudya

14 “ ‘Lamulo la nsembe yachakudya ndi ili: ana a Aaroni azibwera nayo nsembeyo pamaso pa Yehova, patsogolo pa guwa. 15 Wansembe mmodzi atapeko dzanja limodzi la ufa wosalala wa nsembe yachakudya ija kuti ukhala ufa wachikumbutso ndi mafuta pamodzi ndi lubani yense amene ali pa nsembe ya chakudyacho, ndipo azitenthe pa guwa kuti zilandiridwe ndi Yehova mʼmalo mwa nsembe yonse kuti zikhale nsembe ya fungo lokomera Yehova. 16 Aaroni ndi ana ake azidya zimene zatsala koma azidya zopanda yisiti ku malo wopatulika, ku bwalo la tenti ya msonkhano. 17 Poziphika asathire yisiti. Ndawapatsa zotsalazo kuti zikhale gawo lawo la nsembe zanga zopsereza. Zonsezi ndi zopatulika kwambiri monga nsembe yopepesera tchimo ndiponso nsembe yopepesera machimo. 18 Mwana aliyense wamwamuna wa Aaroni azidyako za nsembe zopsereza zopereka kwa Yehova. Ndi gawo lake lokhazikika la chopereka chopsereza kwa Yehova pa mibado yanu yonse. Chilichonse chimene chidzakhudza nsembezo chidzakhala chopatulika.’ ”

19 Yehova anawuzanso Mose kuti, 20 “Nsembe imene Aaroni ndi ana ake ayenera kupereka kwa Yehova pa tsiku limene wansembe akudzozedwa ndi iyi: ufa wosalala kilogalamu imodzi ngati chopereka chachakudya cha nthawi zonse. Azipereka theka limodzi mmawa ndipo theka linalo madzulo. 21 Ipangidwe ndi mafuta pa chiwaya ndipo ubwere nayo ili yosakaniza bwino, yophikidwa mitandamitanda monga amachitira ndi nsembe yachakudya. Iphikidwe moti itulutse fungo lokomera Yehova. 22 Mwana wa fuko la Aaroni amene adzadzozedwe kukhala wansembe kulowa mʼmalo mwa Aaroni ndiye amene azidzakonza ndi kupereka nsembeyi kwa Yehova nthawi zonse monga kunalembedwera. 23 Nsembe iliyonse yachakudya ya wansembe izitenthedwa kwathunthu, isamadyedwe.”

Nsembe Yopepesera Tchimo

24 Yehova anawuza Mose kuti 25 “Uza Aaroni ndi ana ake kuti, ‘Malamulo a nsembe ya tchimo ndi awa: Nsembeyi iziphedwa pamaso pa Yehova pa malo pamene mumaphera nsembe yopsereza popeza ndi nsembe yopatulika. 26 Wansembe amene apereke nsembeyi adyere ku malo wopatulika ndiye kuti mʼbwalo la tenti ya msonkhano. 27 Chilichonse chimene chidzakhudza nsembeyo chidzakhala chopatulika, ndipo ngati magazi ake agwera pa chovala, muchape chovalacho pa malo opatulika. 28 Mʼphika wadothi umene aphikira nyamayo auphwanye. Koma ngati yaphikidwa mu mʼphika wa mkuwa, awukweche ndi kuwutsukuluza ndi madzi. 29 Munthu wamwamuna aliyense wa mʼbanja la wansembe angathe kuyidya popeza nsembeyi ndi yopatulika kwambiri. 30 Koma nsembe yopepesera tchimo imene magazi ake amabwera nawo mu tenti ya msonkhano kudzachita mwambo wopepesera tchimo ku malo opatulika isadyedwe, mʼmalo mwake itenthedwe.’ ”

[a]The Lord said to Moses: “If anyone sins and is unfaithful to the Lord(A) by deceiving a neighbor(B) about something entrusted to them or left in their care(C) or about something stolen, or if they cheat(D) their neighbor, or if they find lost property and lie about it,(E) or if they swear falsely(F) about any such sin that people may commit— when they sin in any of these ways and realize their guilt, they must return(G) what they have stolen or taken by extortion, or what was entrusted to them, or the lost property they found, or whatever it was they swore falsely about. They must make restitution(H) in full, add a fifth of the value to it and give it all to the owner on the day they present their guilt offering.(I) And as a penalty they must bring to the priest, that is, to the Lord, their guilt offering,(J) a ram from the flock, one without defect and of the proper value.(K) In this way the priest will make atonement(L) for them before the Lord, and they will be forgiven for any of the things they did that made them guilty.”

The Burnt Offering

The Lord said to Moses: “Give Aaron and his sons this command: ‘These are the regulations for the burnt offering(M): The burnt offering is to remain on the altar hearth throughout the night, till morning, and the fire must be kept burning on the altar.(N) 10 The priest shall then put on his linen clothes,(O) with linen undergarments next to his body,(P) and shall remove the ashes(Q) of the burnt offering that the fire has consumed on the altar and place them beside the altar. 11 Then he is to take off these clothes and put on others, and carry the ashes outside the camp to a place that is ceremonially clean.(R) 12 The fire on the altar must be kept burning; it must not go out. Every morning the priest is to add firewood(S) and arrange the burnt offering on the fire and burn the fat(T) of the fellowship offerings(U) on it. 13 The fire must be kept burning on the altar continuously; it must not go out.

The Grain Offering

14 “‘These are the regulations for the grain offering:(V) Aaron’s sons are to bring it before the Lord, in front of the altar. 15 The priest is to take a handful of the finest flour and some olive oil, together with all the incense(W) on the grain offering,(X) and burn the memorial[b] portion(Y) on the altar as an aroma pleasing to the Lord. 16 Aaron and his sons(Z) shall eat the rest(AA) of it, but it is to be eaten without yeast(AB) in the sanctuary area;(AC) they are to eat it in the courtyard(AD) of the tent of meeting.(AE) 17 It must not be baked with yeast; I have given it as their share(AF) of the food offerings presented to me.(AG) Like the sin offering[c] and the guilt offering, it is most holy.(AH) 18 Any male descendant of Aaron may eat it.(AI) For all generations to come(AJ) it is his perpetual share(AK) of the food offerings presented to the Lord. Whatever touches them will become holy.[d](AL)’”

19 The Lord also said to Moses, 20 “This is the offering Aaron and his sons are to bring to the Lord on the day he[e] is anointed:(AM) a tenth of an ephah[f](AN) of the finest flour(AO) as a regular grain offering,(AP) half of it in the morning and half in the evening. 21 It must be prepared with oil on a griddle;(AQ) bring it well-mixed and present the grain offering broken[g] in pieces as an aroma pleasing to the Lord. 22 The son who is to succeed him as anointed priest(AR) shall prepare it. It is the Lord’s perpetual share and is to be burned completely.(AS) 23 Every grain offering of a priest shall be burned completely; it must not be eaten.”

The Sin Offering

24 The Lord said to Moses, 25 “Say to Aaron and his sons: ‘These are the regulations for the sin offering:(AT) The sin offering is to be slaughtered before the Lord(AU) in the place(AV) the burnt offering is slaughtered; it is most holy. 26 The priest who offers it shall eat it; it is to be eaten in the sanctuary area,(AW) in the courtyard(AX) of the tent of meeting.(AY) 27 Whatever touches any of the flesh will become holy,(AZ) and if any of the blood is spattered on a garment, you must wash it in the sanctuary area. 28 The clay pot(BA) the meat is cooked in must be broken; but if it is cooked in a bronze pot, the pot is to be scoured and rinsed with water. 29 Any male in a priest’s family may eat it;(BB) it is most holy.(BC) 30 But any sin offering whose blood is brought into the tent of meeting to make atonement(BD) in the Holy Place(BE) must not be eaten; it must be burned up.(BF)

Footnotes

  1. Leviticus 6:1 In Hebrew texts 6:1-7 is numbered 5:20-26, and 6:8-30 is numbered 6:1-23.
  2. Leviticus 6:15 Or representative
  3. Leviticus 6:17 Or purification offering; also in verses 25 and 30
  4. Leviticus 6:18 Or Whoever touches them must be holy; similarly in verse 27
  5. Leviticus 6:20 Or each
  6. Leviticus 6:20 That is, probably about 3 1/2 pounds or about 1.6 kilograms
  7. Leviticus 6:21 The meaning of the Hebrew for this word is uncertain.