Add parallel Print Page Options

Tsiku la Mwambo Wopepesera Machimo

16 Atafa ana awiri a Aaroni amene anaphedwa atapita pamaso pa Yehova mosayenera, Yehova anayankhula ndi Mose. Yehova anawuza Mose kuti, “Uza mchimwene wako Aaroni kuti asamalowe ku Malo Wopatulika, kuseri kwa katani, pamaso pa chivundikiro cha Bokosi la Chipangano nthawi iliyonse imene akufuna kuopa kuti angadzafe, pakuti Ine ndimaoneka mu mtambo umene uli pamwamba pa chivundikiro cha Bokosi la Chipangano.

“Aaroni azilowa Malo Wopatulika Kwambiri motere: azitenga mwana wangʼombe wamwamuna kuti akhale nsembe yopepesera machimo ndi nkhosa yayimuna kuti ikhale nsembe yopsereza. Azivala mwinjiro wopatulika wa nsalu yosalala, azivalanso kabudula wa mʼkati wa nsalu yosalala, azimanga lamba wa nsalu yosalala, ndipo avalenso nduwira ya nsalu yosalala kumutu. Zimenezi ndi nsalu zopatulika ndipo atasamba thupi lonse azivala zimenezi. Kuchokera pa gulu la Aisraeli, Aaroni azitenga mbuzi zazimuna ziwiri kuti zikhale nsembe yopepesera machimo ndi nkhosa yayimuna kuti ikhale nsembe yopsereza.

“Aaroni apereke ngʼombe yayimuna kuti ikhale yopepesera machimo a iye mwini kuti achite mwambo wopepesera machimo ake pamodzi ndi a banja lake. Kenaka atenge mbuzi ziwiri zija ndipo aziyimike pamaso pa Yehova pa khomo la tenti ya msonkhano. Aaroni ndiye achite maere pa mbuzi ziwirizo kuti imodzi ikhale ya Yehova, ndipo inayo ikhale ya Azazele. Aaroni abwere ndi mbuzi imene maere aonetsa kuti ndi ya Yehova, ndipo apereke kuti ikhale nsembe yopereka chifukwa cha tchimo. 10 Koma mbuzi imene maere aonetsa kuti ndi yosenza machimo, apereke ya moyo pamaso pa Yehova, kuti achite mwambo wopepesera machimo pa mbuziyo poyitumiza ku chipululu kuti ikhale ya Azazele.

11 “Aaroni apereke ngʼombe yayimuna kuti ikhale nsembe yopepesera machimo ake. Ndiye achite mwambo wopepesera machimo a iye mwini wake pamodzi ndi banja lake. Pambuyo pake aphe ngʼombe yopepesera machimo ake aja. 12 Kenaka iye atenge chofukizira chodzaza ndi makala a moto ochokera pa guwa lansembe pamaso pa Yehova. Atengenso lubani wonunkhira ndi woperapera wokwanira manja awiri, ndipo alowe naye kuseri kwa katani. 13 Athire lubani pa moto pamaso pa Yehova kuti utsi wa lubaniyo uphimbe chivundikiro chimene chili pamwamba pa Bokosi la Chipangano, kuti Aaroniyo asafe. 14 Ndipo atenge magazi ena a ngʼombeyo, awawaze ndi chala chake pa chivundikiro cha kummawa; kenaka awaze magaziwo ndi chala chake kasanu ndi kawiri patsogolo pa chivundikirocho.

15 “Kenaka Aaroni aphe mbuzi ya nsembe yopepesera machimo a anthu, ndipo magazi ake alowe nawo kuseri kwa katani ndi kuchita chimodzimodzi monga anachitira ndi magazi a ngʼombe aja: Aaroni awaze magaziwo pa chivundikiro chija ndi patsogolo pa chivundikirocho. 16 Pamenepo ndiye kuti wansembeyo wachita mwambo wopepesera ku Malo Wopatulika chifukwa cha kudetsedwa ndi kuwukira kwa Aisraeli pa machimo ena aliwonse amene achita. Achite chimodzimodzi ndi tenti ya msonkhano imenenso ili yodetsedwa chifukwa cha machimo awo. 17 Mu tenti ya msonkhano musakhale munthu ndi mmodzi yemwe nthawi imene Aaroni akupita kukachita mwambo wopepesera ku Malo Wopatulika mpaka atatulukako. Musakhale munthu mu tenti ya msonkhano mpaka atachita mwambo wopepesera machimo a iye mwini wake, banja lake ndi gulu lonse la Aisraeli.

18 “Kenaka, Aaroniyo akatuluka apite ku guwa limene lili pamaso pa Yehova ndi kulichitira mwambo wolipepesera. Atengeko magazi a ngʼombe yayimuna ndiponso magazi a mbuzi ndi kuwapaka pa nyanga zonse za guwa lansembe. 19 Magazi ena awawaze pa guwalo ndi chala chake kasanu ndi kawiri kuliyeretsa ndi kulipatula kuchotsa zodetsa za Aisraeli.

20 “Aaroni akatsiriza mwambo wopepesera Malo Wopatulika, tenti ya msonkhano ndi guwa, azibwera ndi mbuzi yamoyo kudzayipereka nsembe. 21 Aaroni asanjike manja ake pa mutu wa mbuziyo ndipo awulule pa mbuziyo zoyipa zonse ndi zowukira zonse za Aisraeli, kutanthauza machimo awo onse. Machimowo awayike pa mutu wa mbuziyo. Kenaka munthu amene anasankhidwa athamangitsire mbuziyo ku chipululu. 22 Mbuziyo isenze machimo awo onse ndi kupita nawo kutali ndipo munthuyo aleke mbuziyo kuti ipite ku chipululuko.

23 “Pambuyo pake Aaroni alowe mu tenti ya msonkhano ndi kuvula zovala zosalala zija zimene anavala polowa ku Malo Wopatulika ndi kuzisiya komweko. 24 Asambe thupi lonse ku Malo Wopatulika ndi kuvala zovala zake za nthawi zonse. Kenaka atuluke ndi kukapereka nsembe yopsereza ya iye mwini, ndiponso nsembe yopsereza yoperekera anthu. Akatero ndiye kuti wachita mwambo wopepesera machimo a iye mwini wake ndi a anthu. 25 Mafuta a nyama yopepesera machimo awatenthe pa guwa lansembe.

26 “Tsono munthu amene anaperekeza mbuzi yosenza machimo ija achape zovala zake ndi kusamba. Pambuyo pake alowe ku msasa. 27 Ngʼombe ndi mbuzi zoperekera nsembe yopepesera machimo zimene magazi ake anabwera nawo kuti achitire mwambo wopepesera Malo Wopatulika, azitulutsire kunja kwa msasa. Koma zikopa zake, nyama yake ndi matumbo ake azitenthe. 28 Munthu amene azitenthe achape zovala zake ndi kusamba. Pambuyo pake alowe mu msasa.

29 “Ili likhale lamulo lanu lamuyaya: Mwezi wachisanu ndi chiwiri, pa tsiku la khumi la mwezi, mugonje pamaso pa Yehova. Musamagwire ntchito iliyonse, kaya ndinu mbadwa kapena mlendo amene akukhala pakati panu, 30 chifukwa tsiku limeneli kudzachitika mwambo wopepesera machimo anu, kukuyeretsani kuti mukhale oyeretsedwa ku machimo anu pamaso pa Yehova. 31 Limeneli ndi tsiku lanu la Sabata lopumula, ndipo muzigonja pamaso pa Yehova. Limeneli ndi lamulo lanu la muyaya. 32 Wansembe amene wadzozedwa ndi kupatulidwa kuti akhale wansembe kulowa mʼmalo mwa abambo ake ndiye azichita mwambo wopepesera machimo atavala zovala zake zosalala ndi zopatulika. 33 Adzachite mwambo wopepesera machimo Malo Wopatulika, tenti ya msonkhano ndi guwa lansembe. Adzachitenso mwambo wopepesera anzake ndi gulu lonse la anthu.

34 “Ili likhale lamulo lanu lamuyaya. Mwambo wopepesera machimo uzichitika kamodzi pa chaka chifukwa cha machimo a anthu onse.”

Ndipo Mose anachita monga momwe Yehova analamulira.