Add parallel Print Page Options

Za Uchimo, Chikhulupiriro ndi Ntchito

17 Yesu anati kwa ophunzira ake, “Zinthu zimene zimachimwitsa sizingalephere kubwera, koma tsoka kwa munthu wozibweretsayo. Kukanakhala bwino kwa iye kuti aponyedwe mʼnyanja atamangiriridwa mwala wamphero mʼkhosi mwake kusiyana kuti achimwitse mmodzi mwa ana aangʼonowa. Nʼchifukwa chake dziyangʼanireni nokha.

“Ngati mʼbale wanu achimwa, mudzudzuleni, ndipo ngati alapa, mukhululukireni. Ngati iye akulakwira kasanu ndi kawiri pa tsiku, ndipo ngati nʼkubweranso kwa iwe kasanu ndi kawiri nati, ‘Ndalapa,’ umukhululukire.”

Atumwiwo anati kwa Ambuye, “Kulitsani chikhulupiriro chathu!”

Yesu anayankha kuti, “Ngati muli ndi chikhulupiriro chachingʼono ngati kambewu kampiru, mukhoza kulamula mtengo wamkuyu uwu kuti, ‘Zulidwa ndi kukadzalidwa mʼnyanja,’ ndipo udzakumverani.

“Tiyerekeze kuti mmodzi mwa inu anali ndi wantchito wolima kapena woweta nkhosa, kodi angawuze wantchitoyo atabwera ku munda kuti, ‘Tsopano bwera kuno khala pansi kuti udye?’ Kodi sangamuwuze kuti, ‘Konzere chakudya cha madzulo, iweyo ukonzeke ndipo undidikirire pamene ndikudya ndi kumwa; kenaka ukhoza kudya ndi kumwa?’ Kodi iye angathokoze wantchitoyo chifukwa chochita chimene anawuzidwa kuchita? 10 Chimodzimodzi inunso, mukachita zonse zimene munawuzidwa, muzinena kuti, ‘Ndife antchito osayenera; tangogwira ntchito yathu basi.’ ”

Yesu Achiritsa Akhate Khumi

11 Tsopano Yesu anayenda mʼmalire a pakati pa Samariya ndi Galileya pa ulendo wake wa ku Yerusalemu. 12 Akulowa mʼmudzi wina, amuna khumi amene anali ndi khate anakumana naye. Iwo anayima patali 13 ndipo anafuwula ndi mawu okweza kuti, “Yesu, Ambuye, tichitireni chifundo!”

14 Iye atawaona, anati, “Pitani kadzionetseni nokha kwa ansembe.” Ndipo pamene iwo ankapita, anachiritsidwa.

15 Mmodzi wa iwo, ataona kuti wachiritsidwa, anabwerera, nayamika Mulungu ndi mawu okweza. 16 Anagwetsa nkhope yake nagwa pa mapazi a Yesu ndi kumuthokoza. Ndipo iye anali Msamariya.

17 Yesu anafunsa kuti, “Kodi amene anachiritsidwa sanalipo khumi? Nanga asanu ndi anayi ena ali kuti? 18 Kodi palibe mmodzi mwa iwo amene anabwerera kudzalemekeza Mulungu kupatula mlendoyu?” 19 Pamenepo anati kwa iye, “Imirira ndipo pita; chikhulupiriro chako chakuchiritsa iwe.”

Za Ufumu wa Mulungu

20 Ndipo Afarisi atamufunsa Iye kuti, ufumu wa Mulungu udzabwera liti, Yesu anayankha kuti, “Mulungu sakhazikitsa ufumu wake mooneka ndi maso, 21 kapenanso kuti anthu adzati, ‘Uwu uli apa,’ kapena ‘Uwo uli apo,’ Pakuti taonani ufumu wa Mulungu uli pakati panu.”

22 Kenaka Iye anati kwa ophunzira ake, “Masiku akubwera pamene inu mudzalakalaka mutaona tsiku limodzi la masiku a Mwana wa Munthu, koma simudzaliona. 23 Anthu adzakuwuzani kuti, ‘Uyo ali apoyo!’ kapena ‘Uyu ali apa!’ Musawathamangire iwo. 24 Pakuti monga mphenzi ingʼanima ndi kuwala kuchokera mbali ina ya thambo kufikira inzake, koteronso adzakhala ali Mwana wa Munthu pa tsiku lake. 25 Koma poyamba ayenera kuzunzika mu zambiri ndi kukanidwa ndi mʼbado uno.

26 “Monga mmene zinkachitikira nthawi ya Nowa, momwemonso zidzachitikanso nthawi ya Mwana wa Munthu. 27 Anthu ankadya, kumwa, kukwatira ndi kukwatiwa mpaka tsiku limene Nowa analowa mʼchombo. Pomwepo chigumula chinafika ndi kuwawononga onsewo.

28 “Zinalinso chimodzimodzi nthawi ya Loti. Anthu ankadya ndi kumwa, kugula ndi kugulitsa, kudzala ndi kumanga. 29 Koma tsiku limene Loti anachoka ku Sodomu, moto ndi sulufule zinavumbwa kuchokera kumwamba ndi kuwawononga onsewo.

30 “Zidzakhalanso choncho Mwana wa Munthu akadzaonekera. 31 Tsiku limenelo munthu amene ali pa denga la nyumba yake, ndi katundu wake ali mʼnyumbamo, asadzatsike kukatenga. Chimodzimodzinso, munthu amene adzakhale ali ku munda asadzabwerere kukatenga chilichonse. 32 Kumbukirani mkazi wa Loti! 33 Aliyense amene ayesetsa kusunga moyo wake adzawutaya, ndipo aliyense amene ataya moyo wake adzawusunga. 34 Ine ndikukuwuzani inu, usiku umenewo anthu awiri adzagona pa mphasa imodzi; wina adzatengedwa ndipo wina adzasiyidwa. 35 Amayi awiri adzakhala pamodzi akusinja; wina adzatengedwa ndi wina adzasiyidwa. 36 Amuna awiri adzakhala akulima mʼmunda; wina adzatengedwa ndi wina adzasiyidwa.”

37 Iwo anafunsa kuti, “Ambuye, kodi zimenezi zidzachitikira kuti?”

Iye anayankha kuti, “Kumene kuli mtembo, nʼkumene makwangwala amasonkhanako.”

Sin, Faith, Duty

17 Jesus said to his disciples: “Things that cause people to stumble(A) are bound to come, but woe to anyone through whom they come.(B) It would be better for them to be thrown into the sea with a millstone tied around their neck than to cause one of these little ones(C) to stumble.(D) So watch yourselves.

“If your brother or sister[a] sins against you, rebuke them;(E) and if they repent, forgive them.(F) Even if they sin against you seven times in a day and seven times come back to you saying ‘I repent,’ you must forgive them.”(G)

The apostles(H) said to the Lord,(I) “Increase our faith!”

He replied, “If you have faith as small as a mustard seed,(J) you can say to this mulberry tree, ‘Be uprooted and planted in the sea,’ and it will obey you.(K)

“Suppose one of you has a servant plowing or looking after the sheep. Will he say to the servant when he comes in from the field, ‘Come along now and sit down to eat’? Won’t he rather say, ‘Prepare my supper, get yourself ready and wait on me(L) while I eat and drink; after that you may eat and drink’? Will he thank the servant because he did what he was told to do? 10 So you also, when you have done everything you were told to do, should say, ‘We are unworthy servants; we have only done our duty.’”(M)

Jesus Heals Ten Men With Leprosy

11 Now on his way to Jerusalem,(N) Jesus traveled along the border between Samaria and Galilee.(O) 12 As he was going into a village, ten men who had leprosy[b](P) met him. They stood at a distance(Q) 13 and called out in a loud voice, “Jesus, Master,(R) have pity on us!”

14 When he saw them, he said, “Go, show yourselves to the priests.”(S) And as they went, they were cleansed.

15 One of them, when he saw he was healed, came back, praising God(T) in a loud voice. 16 He threw himself at Jesus’ feet and thanked him—and he was a Samaritan.(U)

17 Jesus asked, “Were not all ten cleansed? Where are the other nine? 18 Has no one returned to give praise to God except this foreigner?” 19 Then he said to him, “Rise and go; your faith has made you well.”(V)

The Coming of the Kingdom of God(W)

20 Once, on being asked by the Pharisees when the kingdom of God would come,(X) Jesus replied, “The coming of the kingdom of God is not something that can be observed, 21 nor will people say, ‘Here it is,’ or ‘There it is,’(Y) because the kingdom of God is in your midst.”[c]

22 Then he said to his disciples, “The time is coming when you will long to see one of the days of the Son of Man,(Z) but you will not see it.(AA) 23 People will tell you, ‘There he is!’ or ‘Here he is!’ Do not go running off after them.(AB) 24 For the Son of Man in his day[d] will be like the lightning,(AC) which flashes and lights up the sky from one end to the other. 25 But first he must suffer many things(AD) and be rejected(AE) by this generation.(AF)

26 “Just as it was in the days of Noah,(AG) so also will it be in the days of the Son of Man. 27 People were eating, drinking, marrying and being given in marriage up to the day Noah entered the ark. Then the flood came and destroyed them all.

28 “It was the same in the days of Lot.(AH) People were eating and drinking, buying and selling, planting and building. 29 But the day Lot left Sodom, fire and sulfur rained down from heaven and destroyed them all.

30 “It will be just like this on the day the Son of Man is revealed.(AI) 31 On that day no one who is on the housetop, with possessions inside, should go down to get them. Likewise, no one in the field should go back for anything.(AJ) 32 Remember Lot’s wife!(AK) 33 Whoever tries to keep their life will lose it, and whoever loses their life will preserve it.(AL) 34 I tell you, on that night two people will be in one bed; one will be taken and the other left. 35 Two women will be grinding grain together; one will be taken and the other left.”(AM) [36] [e]

37 “Where, Lord?” they asked.

He replied, “Where there is a dead body, there the vultures will gather.”(AN)

Footnotes

  1. Luke 17:3 The Greek word for brother or sister (adelphos) refers here to a fellow disciple, whether man or woman.
  2. Luke 17:12 The Greek word traditionally translated leprosy was used for various diseases affecting the skin.
  3. Luke 17:21 Or is within you
  4. Luke 17:24 Some manuscripts do not have in his day.
  5. Luke 17:36 Some manuscripts include here words similar to Matt. 24:40.