Add parallel Print Page Options

Kwa mtsogoleri wamayimbidwe. Salimo la Davide.

109 Mulungu amene ndimakutamandani,
    musakhale chete,
pakuti anthu oyipa ndi achinyengo
    atsekula pakamwa pawo kutsutsana nane;
    iwo ayankhula motsutsana nane ndi malilime abodza.
Andizungulira ndi mawu audani,
    amandinena popanda chifukwa.
Mʼmalo mwa chikondi changa amandineneza,
    koma ine ndine munthu wapemphero.
Iwo amandibwezera zoyipa mʼmalo mwa zabwino,
    ndi udani mʼmalo mwa chikondi changa.

Sankhani munthu woyipa kuti amutsutse iye;
    lolani wotsutsa ayime ku dzanja lake lamanja.
Pamene aweruzidwa, apezeke kuti ndi wolakwa,
    ndipo mapemphero ake amutsutse.
Masiku ake akhale owerengeka;
    munthu wina atenge malo ake a utsogoleri.
Ana ake akhale amasiye
    ndipo mkazi wake akhale wopanda mwamuna.
10 Ana ake akhale oyendayenda ndi opemphapempha;
    apirikitsidwe kuchoka pa mabwinja a nyumba zawo.
11 Wokongoza alande zonse zimene ali nazo;
    alendo afunkhe ntchito za manja ake.
12 Pasapezeke ndi mmodzi yemwe womukomera mtima
    kapena kumvera chisoni ana ake amasiye.
13 Zidzukulu zake zithe nʼkufa,
    mayina awo afafanizidwe mu mʼbado wotsatirawo.
14 Mphulupulu za makolo ake zikumbukiridwe pamaso pa Yehova;
    tchimo la amayi ake lisadzafafanizidwe.
15 Machimo awo akhale pamaso pa Yehova nthawi zonse,
    kuti Iye achotse chikumbutso chawo pa dziko lapansi.

16 Pakuti iye sanaganizirepo zochita chifundo,
    koma anazunza mpaka kuwapha anthu osauka
    ndi osweka mtima.
17 Anakonda kutemberera,
    matembererowo abwerere kwa iye;
sanakondwe nʼkudalitsa anthu ena,
    choncho madalitso akhale kutali naye.
18 Anavala kutemberera ngati chovala;
    kutemberera kunalowa mʼthupi lake ngati madzi,
    kulowa mʼmafupa ake ngati mafuta.
19 Matemberero akhale ngati chofunda chodzikutira nacho,
    ngati lamba wovala tsiku ndi tsiku.
20 Awa akhale malipiro ochokera kwa Yehova pa onditsutsa anga,
    kwa iwo amene amayankhula zoyipa za ine.

21 Koma Inu Ambuye Wamphamvuzonse,
    muchite nane molingana ndi dzina lanu,
    chifukwa cha ubwino wa chikondi chanu, pulumutseni.
22 Pakuti ndine wosauka ndi wosowa,
    ndipo mtima wanga ukuwawa mʼkati mwanga.
23 Ndikuzimirira ngati mthunzi wa kumadzulo,
    ndapirikitsidwa ngati dzombe.
24 Mawondo anga afowoka chifukwa cha kusala zakudya,
    thupi langa lawonda ndi mutu wanga womwe.
25 Ndine chinthu chotonzedwa kwa otsutsana nane;
    akandiona, amapukusa mitu yawo.

26 Thandizeni Inu Yehova Mulungu wanga;
    pulumutseni molingana ndi chikondi chanu.
27 Adaniwo adziwe kuti limeneli ndi dzanja lanu,
    kuti Inu Yehova mwachita zimenezi.
28 Angathe kutemberera, koma Inu mudzadalitsa;
    pamene iwo andiputa adzachititsidwa manyazi,
    koma mtumiki wanu adzasangalala.
29 Onditsutsa adzavekedwa mnyozo,
    ndipo adzadzifunditsa manyazi ngati chovala.

30 Ndi pakamwa panga ndidzathokoza Yehova kwambiri;
    ndidzamutamanda mʼgulu lalikulu la anthu.
31 Popeza Iye amayima ku dzanja lamanja la munthu wosowayo,
    kupulumutsa moyo wake kwa iwo amene agamula molakwa.