Add parallel Print Page Options

115 Kwa ife ayi Yehova, kwa ife ayi
    koma ulemerero ukhale pa dzina lanu,
    chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika ndiponso chifukwa cha kukhulupirika kwanu.

Chifukwa chiyani anthu a mitundu ina akunena kuti,
    “Mulungu wawo ali kuti?”
Mulungu wathu ali kumwamba;
    Iye amachita chilichonse chimene chimamukondweretsa.
Koma mafano awo ndi siliva ndi golide,
    opangidwa ndi manja a anthu.
Pakamwa ali napo koma sayankhula,
    maso ali nawo koma sapenya;
makutu ali nawo koma samva,
    mphuno ali nazo koma sanunkhiza;
manja ali nawo koma akakhudza samva kanthu;
    mapazi ali nawo koma sayenda;
    kapena pakhosi pawo kutulutsa mawu.
Anthu amene amapanga mafanowo adzafanana nawo,
    chimodzimodzinso onse amene amadalira mafanowo.

Inu Aisraeli, dalirani Yehova;
    Iye ndiye thandizo lanu ndi chishango chanu.
10 Iwe nyumba ya Aaroni, dalira Yehova;
    Iye ndiye thandizo lako ndi chishango chako.
11 Inu amene mumaopa Iye, dalirani Yehova;
    Iye ndiye thandizo lanu ndi chishango chanu.

12 Yehova watikumbukira ndipo adzatidalitsa:
    adzadalitsa nyumba ya Israeli,
    adzadalitsa nyumba ya Aaroni,
13 adzadalitsa iwo amene amaopa Yehova;
    aangʼono ndi aakulu omwe.

14 Yehova akuwonjezereni madalitso;
    inuyo pamodzi ndi ana anu.
15 Mudalitsidwe ndi Yehova,
    Wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.

16 Kumwamba ndi kwa Yehova,
    koma dziko lapansi Iye walipereka kwa anthu.
17 Si anthu akufa amene amatamanda Yehova,
    amene amatsikira kuli chete;
18 ndi ife amene timatamanda Yehova,
    kuyambira tsopano mpaka muyaya.

Tamandani Yehova.