Add parallel Print Page Options

116 Ndimakonda Yehova pakuti Iyeyo amamva mawu anga;
    Iye amamva kulira kwanga kopempha chifundo.
Pakuti ananditchera khutu,
    ndidzayitana Iye masiku onse a moyo wanga.

Zingwe za imfa zinandizinga,
    zoopsa za ku dziko la anthu akufa zinandigwera;
    ndinapeza mavuto ndi chisoni.
Pamenepo ndinayitana dzina la Yehova:
    “Inu Yehova, pulumutseni!”

Yehova ndi wokoma mtima ndi wolungama
    Mulungu wathu ndi wodzaza ndi chifundo.
Yehova amateteza munthu wodzichepetsa mtima;
    pamene ndinali ndi chosowa chachikulu, Iye anandipulumutsa.

Pumula iwe moyo wanga,
    pakuti Yehova wakuchitira zokoma.

Pakuti Inu Yehova mwapulumutsa moyo wanga ku imfa,
    maso anga ku misozi,
    mapazi anga kuti angapunthwe,
kuti ine ndiyende pamaso pa Yehova
    mʼdziko la anthu amoyo.
10 Ine ndinakhulupirira; choncho ndinati,
    “Ndasautsidwa kwambiri.”
11 Ndipo ndili mʼnkhawa yanga ndinati,
    “Anthu onse ndi abodza.”

12 Ndingamubwezere chiyani Yehova,
    chifukwa cha zokoma zake zonse zimene wandichitira?
13 Ndidzakweza chikho cha chipulumutso
    ndipo ndidzayitana dzina la Yehova.
14 Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova
    pamaso pa anthu ake onse.

15 Imfa ya anthu oyera mtima
    ndi yamtengowapatali pamaso pa Yehova.
16 Inu Yehova, zoonadi ndine mtumiki wanu:
    ndine mtumiki wanu, mwana wa mdzakazi wanu;
    Inu mwamasula maunyolo anga.

17 Ndidzapereka nsembe yachiyamiko kwa Inu
    ndipo ndidzayitanira pa dzina la Yehova.
18 Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova
    pamaso pa anthu ake onse,
19 mʼmabwalo a nyumba ya Yehova,
    mʼkati mwako iwe Yerusalemu.

Tamandani Yehova.