Add parallel Print Page Options

135 Tamandani Yehova.

Tamandani dzina la Yehova;
    mutamandeni, inu atumiki a Yehova,
amene mumatumikira mʼnyumba ya Yehova,
    mʼmabwalo a nyumba ya Mulungu wathu.

Tamandani Yehova, pakuti Yehova ndi wabwino;
    imbani nyimbo zotamanda dzina lake, pakuti nʼkokoma kutero,
Pakuti Yehova wasankha Yakobo kuti akhale wake,
    Israeli kuti akhale chuma chake chapamtima.

Ndikudziwa kuti Yehova ndi wamkulu,
    kuti Ambuye athu ndi wamkulu kuposa milungu yonse.
Yehova amachita chilichonse chimene chimamukomera,
    kumwamba ndi dziko lapansi,
    ku nyanja zazikulu ndi ku malo ake onse akuya.
Iye amatulutsa mitambo kuchokera ku malekezero a dziko lapansi,
    amatumiza zingʼaningʼani pamodzi ndi mvula
    ndipo amatulutsa mphepo ku malo ake osungiramo.

Anakantha ana oyamba kubadwa a Igupto,
    ana oyamba kubadwa a anthu ndi nyama.
Iye anatumiza zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa pakati pako, iwe Igupto,
    kutsutsana ndi Farao pamodzi ndi atumiki ake onse.
10 Iye anakantha mitundu yambiri ya anthu
    ndi kupha mafumu amphamvu:
11 Sihoni mfumu ya Aamori,
    Ogi mfumu ya Basani,
    ndi maufumu onse a ku Kanaani;
12 ndipo anapereka dziko lawo ngati cholowa,
    cholowa cha anthu ake Aisraeli.

13 Dzina lanu, Inu Yehova, ndi losatha mpaka muyaya,
    mbiri yanu, Inu Yehova, idziwika mibado yonse.
14 Pakuti Yehova adzaonetsa kuti anthu ake ngosalakwa,
    ndipo adzachitira chifundo atumiki ake.

15 Mafano a mitundu ya anthu ndi siliva ndi golide,
    opangidwa ndi manja a anthu.
16 Pakamwa ali napo koma sayankhula
    maso ali nawo, koma sapenya;
17 makutu ali nawo, koma sakumva
    ndipo mʼkamwa mwawo mulibe mpweya uliwonse.
18 Iwo amene amapanga mafanowo adzakhala ngati mafanowo,
    chimodzimodzinso iwo amene amadalira mafanowo.

19 Inu nyumba ya Israeli, tamandani Yehova;
    inu nyumba ya Aaroni, tamandani Yehova;
20 Inu nyumba ya Levi, tamandani Yehova;
    Inu amene mumaopa Iye, tamandani Yehova.
21 Wodalitsika ndi Yehova kuchokera mʼZiyoni,
    amene amakhala mu Yerusalemu.

Tamandani Yehova.