Add parallel Print Page Options

Miyambo ya Solomoni

10 Miyambo ya Solomoni:

Mwana wanzeru amakondweretsa abambo ake,
    koma mwana wopusa amamvetsa amayi ake chisoni.

Chuma chochipeza mwachinyengo sichipindulitsa,
    koma chilungamo chimapulumutsa ku imfa.

Yehova salola kuti munthu wolungama azikhala ndi njala;
    koma amalepheretsa zokhumba za anthu oyipa.

Wochita zinthu mwaulesi amasauka,
    koma wogwira ntchito mwakhama amalemera.

Amene amakolola nthawi yachilimwe ndi mwana wanzeru,
    koma amene amangogona nthawi yokolola ndi mwana wochititsa manyazi.

Madalitso amakhala pa mutu wa munthu wolungama,
    koma pakamwa pa munthu woyipa pamaphimba chiwawa.

Munthu wolungama anzake adzamukumbukira ngati mdalitso,
    koma dzina la munthu woyipa lidzayiwalika.

Munthu wa mtima wanzeru amasamala malamulo,
    koma chitsiru chomangolongolola chidzawonongeka.

Munthu woyenda mwangwiro amayenda mosatekeseka;
    koma amene amayenda njira yokhotakhota adzadziwika.

10 Aliyense wotsinzinira maso mwachinyengo amabweretsa mavuto,
    koma wodzudzula chitsiru molimba mtima amabweretsa mtendere.

11 Pakamwa pa munthu wolungama ndi kasupe wamoyo,
    koma pakamwa pa munthu woyipa pamabisa chiwawa.

12 Udani umawutsa mikangano,
    koma chikondi chimaphimba zolakwa zonse.

13 Nzeru imapezeka pa milomo ya munthu wozindikira zinthu,
    koma pa msana pa munthu wopanda nzeru sipachoka chikwapu.

14 Anzeru amasunga chidziwitso
    koma pakamwa pa chitsiru pamatulutsa zowononga.

15 Chuma cha munthu wolemera
    ndiye chitetezo chake; koma umphawi ndiye chiwonongeko cha osauka.

16 Moyo ndiye malipiro a munthu wolungama,
    koma phindu la anthu oyipa ndi uchimo ndi imfa.

17 Wosamalira malangizo amayenda mʼnjira ya moyo,
    koma wonyoza chidzudzulo amasochera.

18 Amene amabisa chidani chake ndi munthu wonama,
    ndipo amene amafalitsa miseche ndi chitsiru.

19 Mawu akachuluka zolakwa sizisowa,
    koma amene amasunga pakamwa pake ndi wanzeru.

20 Mawu a munthu wolungama ali ngati siliva wabwino kwambiri,
    koma mtima wa munthu woyipa ndi wopanda phindu.

21 Milomo ya anthu olungama imalimbikitsa ambiri;
    koma chitsiru chimafa chifukwa chosowa nzeru.

22 Mdalitso wa Yehova ndiwo umabweretsa chuma,
    ntchito za munthu siziwonjezerapo kanthu.

23 Kwa chitsiru kuchita zinthu zoyipa ndiye chinthu chomusangalatsa,
    koma kwa munthu womvetsa bwino zinthu nzeru ndiyo imamusangalatsa.

24 Chimene munthu woyipa amachiopa chidzamuchitikira;
    chimene munthu wolungama amachilakalaka adzachipeza.

25 Pamene namondwe wawomba, anthu oyipa amachotsedwa,
    koma anthu olungama amakhazikika mpaka muyaya.

26 Momwe amakhalira vinyo wosasa mʼkamwa ndi momwe umakhalira utsi mʼmaso,
    ndi momwenso amakhalira munthu waulesi kwa amene amutuma.

27 Kuopa Yehova kumatalikitsa moyo;
    koma zaka za anthu oyipa zidzafupikitsidwa.

28 Chiyembekezo cha olungama chimapatsa chimwemwe,
    koma chiyembekezo cha anthu ochimwa chidzafera mʼmazira.

29 Njira za Yehova ndi linga loteteza anthu ochita zabwino,
    koma wochita zoyipa adzawonongeka.

30 Munthu wolungama sadzachotsedwa, pamalo pake
    koma oyipa sadzakhazikika pa dziko.

31 Pakamwa pa munthu wolungama pamatulutsa za nzeru,
    koma lilime lokhota lidzadulidwa.

32 Milomo ya anthu olungama imadziwa zoyenera kuyankhula,
    koma pakamwa pa anthu ochimwa pamatulutsa zokhota zokhazokha.

Proverbs of Solomon

10 The proverbs(A) of Solomon:(B)

A wise son brings joy to his father,(C)
    but a foolish son brings grief to his mother.

Ill-gotten treasures have no lasting value,(D)
    but righteousness delivers from death.(E)

The Lord does not let the righteous go hungry,(F)
    but he thwarts the craving of the wicked.(G)

Lazy hands make for poverty,(H)
    but diligent hands bring wealth.(I)

He who gathers crops in summer is a prudent son,
    but he who sleeps during harvest is a disgraceful son.(J)

Blessings crown the head of the righteous,
    but violence overwhelms the mouth of the wicked.[a](K)

The name of the righteous(L) is used in blessings,[b]
    but the name of the wicked(M) will rot.(N)

The wise in heart accept commands,
    but a chattering fool comes to ruin.(O)

Whoever walks in integrity(P) walks securely,(Q)
    but whoever takes crooked paths will be found out.(R)

10 Whoever winks maliciously(S) causes grief,
    and a chattering fool comes to ruin.

11 The mouth of the righteous is a fountain of life,(T)
    but the mouth of the wicked conceals violence.(U)

12 Hatred stirs up conflict,
    but love covers over all wrongs.(V)

13 Wisdom is found on the lips of the discerning,(W)
    but a rod is for the back of one who has no sense.(X)

14 The wise store up knowledge,(Y)
    but the mouth of a fool invites ruin.(Z)

15 The wealth of the rich is their fortified city,(AA)
    but poverty is the ruin of the poor.(AB)

16 The wages of the righteous is life,(AC)
    but the earnings of the wicked are sin and death.(AD)

17 Whoever heeds discipline shows the way to life,(AE)
    but whoever ignores correction leads others astray.

18 Whoever conceals hatred with lying lips(AF)
    and spreads slander is a fool.

19 Sin is not ended by multiplying words,
    but the prudent hold their tongues.(AG)

20 The tongue of the righteous is choice silver,
    but the heart of the wicked is of little value.

21 The lips of the righteous nourish many,
    but fools die for lack of sense.(AH)

22 The blessing of the Lord(AI) brings wealth,(AJ)
    without painful toil for it.(AK)

23 A fool finds pleasure in wicked schemes,(AL)
    but a person of understanding delights in wisdom.

24 What the wicked dread(AM) will overtake them;(AN)
    what the righteous desire will be granted.(AO)

25 When the storm has swept by, the wicked are gone,
    but the righteous stand firm(AP) forever.(AQ)

26 As vinegar to the teeth and smoke(AR) to the eyes,
    so are sluggards to those who send them.(AS)

27 The fear of the Lord adds length to life,(AT)
    but the years of the wicked are cut short.(AU)

28 The prospect of the righteous is joy,
    but the hopes of the wicked come to nothing.(AV)

29 The way of the Lord is a refuge for the blameless,
    but it is the ruin of those who do evil.(AW)

30 The righteous will never be uprooted,
    but the wicked will not remain in the land.(AX)

31 From the mouth of the righteous comes the fruit of wisdom,(AY)
    but a perverse tongue(AZ) will be silenced.

32 The lips of the righteous know what finds favor,(BA)
    but the mouth of the wicked only what is perverse.(BB)

Footnotes

  1. Proverbs 10:6 Or righteous, / but the mouth of the wicked conceals violence
  2. Proverbs 10:7 See Gen. 48:20.