Add parallel Print Page Options

16 Zolinga za mu mtima ndi za munthu,
    koma kwa Yehova ndiye kumachokera yankho.

Zochita zonse za munthu zimaoneka zabwino pamaso pake,
    koma Yehova ndiye amasanthula zolinga zako.

Pereka ntchito zako zonse mʼmanja mwa Yehova,
    ndipo zolinga zako zidzachitikadi.

Yehova amachita zonse ndi cholinga chake,
    ngakhale anthu oyipa kuti aone tsiku latsoka.

Munthu aliyense wodzikuza amamunyansa Yehova.
    Koma dziwani izi: Iwo sadzakhala osalangidwa.

Chifukwa cha chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika, munthu amakhululukidwa machimo ake;
    chifukwa cha kuopa Yehova munthu amapewa zoyipa.

Pamene makhalidwe a munthu akondweretsa Yehova,
    ngakhale adani ake amakhala naye mwa mtendere.

Kuli bwino kukhala ndi zinthu pangʼono zozipeza mwachilungamo,
    kusiyana ndi kukhala ndi zinthu zambiri zozipeza popanda chilungamo.

Mtima wa munthu umalingalira zochita,
    koma Yehova ndiye amakhazikitsa njira zake.

10 Mawu a mfumu ali ngati mawu ochokera kwa Mulungu;
    ndipo pakamwa pake sipalakwa poweruza mlandu.

11 Miyeso ndi masikelo achilungamo zimachokera kwa Yehova;
    miyala yonse yoyesera ya mʼthumba anayipanga ndi Yehova.

12 Kuchita zoyipa kumanyansa mafumu,
    pakuti chilungamo ndiye maziko a ufumu wake.

13 Mawu owona amakondweretsa mfumu.
    Iyo imakonda munthu woyankhula choonadi.

14 Ukali wa mfumu ndi mthenga wa imfa,
    koma munthu wanzeru amawupepesa ukaliwo.

15 Kuwala kwa nkhope ya mfumu kumapatsa moyo;
    ndipo kukoma mtima kwake kuli ngati mitambo ya mvula nthawi ya chilimwe.

16 Nʼkwabwino kwambiri kupeza nzeru kupambana golide.
    Kukhala womvetsa bwino zinthu nʼkwabwino kupambana ndi kukhala ndi siliva.

17 Msewu wa munthu wowongoka mtima umapewa zoyipa;
    wopenyetsetsa kumene akupita amasunga moyo wake.

18 Kunyada kumafikitsa ku chiwonongeko,
    ndipo munthu wodzikuza adzagwa.

19 Nʼkwabwino kukhala ndi mtima wodzichepetsa pakati pa anthu oponderezedwa,
    kusiyana ndi kugawana zolanda ndi anthu onyada.

20 Munthu womvera malangizo zinthu zimamuyendera bwino,
    ndipo wodala ndi amene amadalira Yehova.

21 A mtima wanzeru amatchedwa ozindikira zinthu,
    ndipo mawu ake okoma amawonjezera nzeru.

22 Kumvetsa zinthu ndi kasupe wa moyo kwa iwo amene ali nako,
    koma uchitsiru umabweretsa chilango kwa zitsiru.

23 Mtima wanzeru umathandiza munthu kuyankhula mwa nzeru,
    ndipo mawu ake amawonjezera nzeru.

24 Mawu okometsera ali ngati chisa cha njuchi,
    amakoma mu mtima ndipo amalimbitsa thupi.

25 Pali njira ina yooneka ngati yowongoka kwa munthu
    koma kumatsiriziro kwake ndi imfa.

26 Njala ya munthu wantchito imamuthandiza kulimbikira;
    njalayo imamukakamiza kuchitapo kanthu.

27 Munthu wopanda pake amakonzekera kuchita zoyipa
    ndipo mawu ake ali ngati moto wopsereza.

28 Munthu woyipa mtima amayambitsa mikangano,
    ndipo miseche imalekanitsa anthu okondana kwambiri.

29 Munthu wandewu amakopa mnansi wake,
    ndipo amamuyendetsa njira imene si yabwino.

30 Amene amatsinzinira maso ake amalingalira zinthu zokhota;
    amene amachita msunamo amakonzeka kuchita zoyipa.

31 Imvi zili ngati chipewa chaufumu chaulemerero;
    munthu amazipeza akakhala moyo wolungama.

32 Munthu wosapsa mtima msanga amaposa munthu wankhondo,
    munthu wowugwira mtima wake amaposa amene amalanda mzinda.

33 Maere amaponyedwa pa mfunga,
    koma ndiye Yehova amene amalongosola zonse.