Add parallel Print Page Options

27 Usamanyadire za mawa,
    pakuti sudziwa zimene zidzachitike pa tsikulo.

Munthu wina akutamande, koma osati wekha;
    mlendo akakutamanda, ndiponi koma osati ndi pakamwa pako.

Mwala ndi wolemera ndipo mchenganso ndi wolemera kwambiri,
    koma makani a chitsiru ndi oposa zonsezo kulemera kwake.

Mkwiyo umadzetsa nkhanza ndipo kupsa mtima kumachititsa zoopsa.
    Koma nsanje imachita zoopsa zopambana.

Kudzudzula munthu poyera nʼkwabwino
    kuposa chikondi chobisika.

Munthu amene amakukonda ngakhale akupweteke zili bwino,
    koma mdani wako amakupsompsona mwachinyengo.

Iye amene wakhuta amayipidwa ndi chisa cha uchi,
    koma kwa munthu wanjala ngakhale chimene chili chowawa chimamukomera.

Munthu amene wasochera ku nyumba kwake,
    ali monga mbalame imene yasochera pa chisa chake.

Mafuta ndi zonunkhira zimasangalatsa mtima,
    ndipo kukoma mtima kwa bwenzi kwagona pa malangizo ake.

10 Usasiye bwenzi lako ndiponso bwenzi la abambo ako,
    ndipo usapite ku nyumba ya mʼbale wako pamene wakumana ndi mavuto;
    mnzako wokhala naye pafupi amaposa mʼbale wako wokhala kutali.

11 Mwana wanga, khala wanzeru, ndipo ukondweretse mtima wanga;
    pamenepo ine ndidzatha kuyankha aliyense amene amandinyoza.

12 Munthu wochenjera akaona choopsa amabisala,
    koma munthu wopusa amangopitirira ndipo amakumana ndi mavuto.

13 Utenge chovala cha munthu amene waperekera mlendo chikole;
    ngati chigwiriro chifukwa waperekera chikole mlendo wosadziwika.

14 Ngati munthu apatsa mnzake moni mofuwula mmamawa kwambiri,
    anthu adzamuyesa kuti akutemberera.

15 Mkazi wolongolola ali ngati
    mvula yamvumbi.
16 Kumuletsa mkazi wotereyu zimenezi zili ngati kuletsa mphepo
    kapena kufumbata mafuta mʼdzanja.

17 Chitsulo chimanoledwa ndi chitsulo chinzake,
    chomwechonso munthu amanoledwa ndi munthu mnzake.

18 Amene amasamalira mtengo wamkuyu adzadya zipatso zake,
    ndipo iye amene amasamalira mbuye wake adzalandira ulemu.

19 Monga momwe nkhope imaonekera mʼmadzi,
    chomwechonso mtima wa munthu umadziwika ndi ntchito zake.

20 Manda sakhuta,
    nawonso maso a munthu sakhuta.

21 Siliva amasungunulira mu uvuni ndipo golide mʼngʼanjo,
    chomwechonso munthu amadziwika ndi zomwe akudzitamandira nazo.

22 Ngakhale utakonola chitsiru mu mtondo
    ndi musi ngati chimanga,
    uchitsiru wakewo sudzachoka.

23 Uzidziwe bwino nkhosa zako momwe zilili.
    Kodi usamalire bwino ziweto zako?
24 Paja chuma sichikhala mpaka muyaya,
    ndipo ufumu sukhala mpaka mibado yonse.
25 Pamene udzu watha, msipu nʼkumera;
    ndipo atatuta udzu wa ku mapiri,
26 ana ankhosa adzakupatsani chovala
    ndipo pogulitsa mbuzi mudzapeza ndalama yogulira munda.
27 Mudzakhala ndi mkaka wambuzi wambiri
    kuti muzidya inuyo ndi banja lanu
    ndi kudyetsa antchito anu aakazi.