Add parallel Print Page Options

28 Munthu woyipa amathawa ngakhale palibe wina womuthamangitsa,
    koma wolungama ndi wolimba mtima ngati mkango.

Pamene mʼdziko muli kuwukirana, dzikolo limakhala ndi olamulira ambiri,
    koma anthu omvetsa ndi odziwa zinthu bwino ndiwo angakhazikitse bata mʼdzikolo nthawi yayitali.

Munthu wosauka amene amapondereza osauka anzake
    ali ngati mvula yamkuntho imene imawononga mbewu mʼmunda.

Amene amakana malamulo amatamanda anthu oyipa,
    koma amene amasunga malamulo amatsutsana nawo.

Anthu oyipa samvetsa za chiweruzo cholungama,
    koma amene amafuna kuchita zimene Yehova afuna amachimvetsetsa bwino.

Munthu wosauka wa makhalidwe abwino
    aposa munthu wolemera wa makhalidwe okhotakhota.

Amene amasunga malamulo ndi mwana wozindikira zinthu,
    koma amene amayenda ndi anthu adyera amachititsa manyazi abambo ake.

Amene amachulukitsa chuma chake polandira chiwongoladzanja chochuluka
    amakundikira chumacho anthu ena, amene adzachitira chifundo anthu osauka.

Wokana kumvera malamulo
    ngakhale pemphero lake lomwe limamunyansa Yehova.

10 Amene amatsogolera anthu olungama kuti ayende mʼnjira yoyipa
    adzagwera mu msampha wake womwe,
    koma anthu opanda cholakwa adzalandira cholowa chabwino.

11 Munthu wolemera amadziyesa kuti ndi wanzeru,
    koma munthu wosauka amene ali ndi nzeru zodziwa zinthu amamutulukira.

12 Pamene olungama apambana pamakhala chikondwerero chachikulu;
    koma pamene anthu oyipa apatsidwa ulamuliro, anthu amabisala.

13 Wobisa machimo ake sadzaona mwayi,
    koma aliyense amene awulula ndi kuleka machimowo, adzalandira chifundo.

14 Ndi wodala munthu amene amaopa Yehova nthawi zonse,
    koma amene aumitsa mtima wake adzagwa mʼmavuto.

15 Ngati mkango wobuma kapena chimbalangondo cholusa
    ndi mmenenso amakhalira munthu woyipa akamalamulira anthu osauka.

16 Wolamulira amene samvetsa zinthu ndiye amakhala wankhanza
    koma amene amadana ndi phindu lopeza mwachinyengo adzakhala ndi moyo wautali.

17 Munthu amene wapalamula mlandu wopha munthu
    adzakhala wothawathawa mpaka imfa yake;
    wina aliyense asamuthandize.

18 Amene amayenda mokhulupirika adzapulumutsidwa
    koma amene njira zake ndi zokhotakhota adzagwa mʼdzenje.

19 Amene amalima mʼmunda mwake adzakhala ndi chakudya chochuluka,
    koma amene amangosewera adzakhala mʼmphawi.

20 Munthu wokhulupirika adzadalitsika kwambiri,
    koma wofuna kulemera mofulumira adzalangidwa.

21 Kukondera si kwabwino,
    ena amachita zolakwazo chifukwa cha kachidutswa ka buledi.

22 Munthu wowumira amafunitsitsa kulemera
    koma sazindikira kuti umphawi udzamugwera.

23 Amene amadzudzula mnzake potsiriza pake
    mnzakeyo adzamukonda kwambiri, kupambana amene amanena mawu oshashalika.

24 Amene amabera abambo ake kapena amayi ake
    namanena kuti “kumeneko sikulakwa,”
    ndi mnzake wa munthu amene amasakaza.

25 Munthu wadyera amayambitsa mikangano,
    koma amene amadalira Yehova adzalemera.

26 Amene amadzidalira yekha ndi chitsiru,
    koma amene amatsata nzeru za ena adzapulumuka.

27 Amene amapereka kwa osauka sadzasowa kanthu,
    koma amene amatsinzina maso ake adzatembereredwa kwambiri.

28 Pamene anthu oyipa apatsidwa ulamuliro anthu amabisala,
    koma anthu oyipa akawonongeka olungama amapeza bwino.