Add parallel Print Page Options

Mawu a Mfumu Lemueli

31 Nawa mawu a mfumu Lemueli wa ku Massa amene anamuphunzitsa amayi ake:

Nʼchiyani mwana wanga? Nʼchiyani mwana wa mʼmimba mwanga?
    Nʼchiyani iwe mwana wanga amene ndinachita kupempha ndi malumbiro?
Usapereke mphamvu yako kwa akazi.
    Usamayenda nawo amenewa popeza amawononga ngakhale mafumu.

Iwe Lemueli si choyenera kwa mafumu,
    mafumu sayenera kumwa vinyo.
    Olamulira asamalakalake chakumwa choledzeretsa
kuopa kuti akamwa adzayiwala malamulo a dziko,
    nayamba kukhotetsa zinthu zoyenera anthu osauka.
Perekani chakumwa choledzeretsa kwa amene ali pafupi kufa,
    vinyo kwa amene ali pa mavuto woopsa;
amwe kuti ayiwale umphawi wawo
    asakumbukirenso kuvutika kwawo.

Yankhula mʼmalo mwa amene sangathe kudziyankhulira okha.
    Uwayankhulire anthu onse osiyidwa pa zonse zowayenera.
Yankhula ndi kuweruza mwachilungamo.
    Uwateteze amphawi ndi osauka.

Mathero: Mkazi Wangwiro

10 Kodi mkazi wangwiro angathe kumupeza ndani?
    Ndi wokwera mtengo kuposa miyala yamtengowapatali.
11 Mtima wa mwamuna wake umamukhulupirira
    ndipo mwamunayo sasowa phindu.
12 Masiku onse a moyo wake
    mkaziyo amachitira mwamuna wake zabwino zokhazokha osati zoyipa.
13 Iye amafunafuna ubweya ndi thonje;
    amagwira ntchito ndi manja ake mwaufulu.
14 Iye ali ngati sitima zapamadzi za anthu amalonda,
    amakatenga chakudya chake kutali.
15 Iye amadzuka kusanache kwenikweni;
    ndi kuyamba kukonzera a pa banja pake chakudya
    ndi kuwagawira ntchito atsikana ake antchito.
16 Iye amalingalira za munda ndi kuwugula;
    ndi ndalama zimene wazipeza amalima munda wamphesa.
17 Iye amavala zilimbe
    nagwira ntchito mwamphamvu ndi manja ake.
18 Iye amaona kuti malonda ake ndi aphindu,
    choncho nyale yake sizima usiku wonse.
19 Iye amadzilukira thonje
    ndipo yekha amagwira chowombera nsalu.
20 Iye amachitira chifundo anthu osauka
    ndipo amapereka chithandizo kwa anthu osowa.
21 Iye saopa kuti banja lake lifa ndi kuzizira pa nyengo yachisanu;
    pakuti onse amakhala atavala zovala zofunda.
22 Iye amadzipangira yekha zoyala pa bedi pake;
    amavala zovala zabafuta ndi zapepo.
23 Mwamuna wake ndi wodziwika pa chipata cha mzinda,
    ndipo amakhala pakati pa akuluakulu a mʼdzikomo.
24 Iye amasoka nsalu zabafuta nazigulitsa;
    amaperekanso mipango kwa anthu amalonda.
25 Mphamvu ndi ulemu zimakhala ngati chovala chake;
    ndipo amaseka osaopa zamʼtsogolo.
26 Iye amayankhula mwanzeru,
    amaphunzitsa anthu mwachikondi.
27 Iye amayangʼanira makhalidwe a anthu a pa banja lake
    ndipo sachita ulesi ndi pangʼono pomwe.
28 Ana ake amamunyadira ndipo amamutcha kuti wodala;
    ndipo mwamuna wake, amamuyamikira nʼkumati,
29 “Pali akazi ambiri amene achita zinthu zopambana
    koma iwe umawaposa onsewa.”
30 Nkhope yachikoka ndi yonyenga, ndipo kukongola nʼkosakhalitsa;
    koma mkazi amene amaopa Yehova ayenera kutamandidwa.
31 Mupatseni mphotho chifukwa cha zimene iye wachita
    ndipo ntchito zake zimutamande ku mabwalo.