Add parallel Print Page Options

Kuponya Chakudya pa Madzi

11 Ponya chakudya chako pa madzi,
    udzachipezanso patapita masiku ambiri.
Ndalama zako uzisungitse kwa anthu asanu ndi awiri, inde kwa anthu asanu ndi atatu,
    pakuti sudziwa ndi tsoka lanji limene likubwera pa dziko.

Ngati mitambo yadzaza ndi madzi,
    imagwetsa mvula pa dziko lapansi.
Mtengo ukagwera cha kummwera kapena cha kumpoto,
    ndiye kuti udzagonera kumene wagwerako.
Amene amayangʼana mphepo sadzadzala;
    amene amayangʼana mitambo sadzakolola.

Momwe sudziwira mayendedwe a mphepo,
    kapena momwe mzimu umalowera mʼthupi la mwana mʼmimba mwa amayi,
momwemonso sungathe kudziwa ntchito za Mulungu,
    Mlengi wa zinthu zonse.

Dzala mbewu zako mmawa
    ndipo madzulo usamangoti manja lobodo,
pakuti sudziwa chimene chidzapindula,
    mwina ichi kapena icho,
    kapena mwina zonse ziwiri zidzachita bwino.

Kumbukira Mlengi Wako

Kuwala nʼkwabwino,
    ndipo maso amasangalala kuona dzuwa.
Munthu akakhala wa zaka zambiri,
    mulekeni akondwerere zaka zonsezo,
koma iye azikumbukira masiku a mdima,
    pakuti adzakhala ochuluka.
    Chilichonse chimene chikubwera ndi chopanda phindu.

Kondwera mnyamata iwe, pamene ukanali wamngʼono,
    ndipo mtima wako usangalale pa nthawi ya unyamata wako.
Tsatira zimene mtima wako ukufuna,
    ndiponso zimene maso ako akuona,
koma dziwa kuti pa zinthu zonsezo
    Mulungu adzakuweruza.
10 Choncho uchotse zokusautsa mu mtima mwako,
    upewe zokupweteka mʼthupi mwako,
    pakuti unyamata ndi ubwana ndi zopandapake.