Add parallel Print Page Options

Zeba ndi Zalimuna

Aefereimu anafunsa Gideoni kuti, “Nʼchifukwa chiyani watichita zimenezi? Bwanji sunatiyitane pamene umakamenyana ndi Amidiyani?” Iwo anamudzudzula kwambiri.

Koma iye anawayankha kuti, “Nʼchiyani ndachita kuyerekeza ndi zimene mwachita inu? Kodi zimene mwachita inu Aefereimu si zazikulu kuposa zimene fuko langa la Abiezeri lachita? Mulungu wapereka mafumu a Midiyani, Orebu ndi Zeebu mʼmanja mwanu. Ndachita chiyani kuyerekeza ndi zimene mwachita inu?” Atanena izi, anthuwo mitima yawo inatsika.

Gideoni anafika ndi kuwoloka mtsinje wa Yorodani pamodzi ndi anthu 300 amene anali naye. Ngakhale kuti anali otopa anapirikitsabe adani awo. Atafika ku Sukoti anapempha anthu a kumeneko kuti, “Chonde apatseniko buledi ankhondo angawa pakuti atopa. Koma ine ndikupirikitsa Zeba ndi Zalimuna, mafumu a Midiyani.”

Koma atsogoleri a Sukoti anayankha kuti, “Kodi Zeba ndi Zalimuna mwawagonjetsa kale kuti tipatse buledi ankhondo akowa?”

Gideoni anayankha kuti, “Mwatero! Yehova akapereka Zeba ndi Zalimuna mʼdzanja langa, ndidzakukwapulani ndi matsatsa a minga ya mʼchipululu.”

Atachoka pamenepo anapita ku Penueli ndipo anapemphanso buledi kwa anthu a kumeneko, koma iwo anamuyankha monga anayankhira anthu a ku Sukoti aja. Gideoni anawawuzanso kuti, “Ndikamadzabwerera nditawagonjetsa, ndidzagwetsa nsanja iyi.”

10 Nthawi iyi nʼkuti Zeba ndi Zalimuna ali ku Karikori ndi ankhondo pafupifupi 15,000. Amenewa ndiwo anatsalako mwa ankhondo a anthu akummawa; pakuti anafa ankhondo 120,000. 11 Gideoni anadzera njira ya anthu a matenti kummawa kwa Noba ndi Yogibeha ndipo anawathira nkhondo popeza ankhondo awo anali osakonzekera. 12 Zeba ndi Zalimuna, mafumu awiri a Amidiyani anathawa koma Gideoni anawathamangitsa mpaka kuwagwira. Koma ankhondo awo onse anathawa ndi mantha.

13 Ndipo Gideoni mwana wa Yowasi, pobwera kuchokera ku nkhondo anadzera njira ya ku chikweza cha Heresi. 14 Kumeneko iye anagwira mnyamata wa ku Sukoti ndipo atamufunsa, mnyamatayo anamulembera mayina a akuluakulu ndi atsogoleri 77 a ku Sukoti. 15 Kenaka Gideoni anabwera kwa anthu a ku Sukoti ndi kunena kuti, “Awa ndi Zeba ndi Zalimuna, mafumu awiri munkandinena nawo aja kuti, ‘Kodi Zeba ndi Zalimuna wawagonjetsa kale mmene ukuti tiwapatse buledi anthu ako otopawa?’ ” 16 Tsono Gideoni anatenga akuluakulu a mu mzindawo ndipo anagwira matsatsa a minga za mʼchipululu ndi kuwakwapula nawo. 17 Anagwetsa nsanja ya ku Penueli ndi kupha amuna onse a mu mzindawo.

18 Kenaka anafunsa Zeba ndi Zalimuna kuti, “Kodi anthu a ku Tabori amene munawapha aja anali a maonekedwe otani?” Iwo anayankha kuti, “Anali anthu a maonekedwe ngati inu. Aliyense ankaoneka ngati mwana wa mfumu?”

Iwo anayankha kuti, “Anthu ngati inu, aliyense wooneka ngati mwana wa mfumu.”

19 Ndipo Gideoni anayankha kuti, “Ndikulumbira pa Mulungu, mukanapanda kuwapha nanenso sindikanakuphani. Ndi abale anga amenewo, ana a amayi anga enieni.” 20 Tsono anawuza Yetero, mwana wake wachisamba kuti, “Tiye, ipha anthu amenewa!” Koma chifukwa Yeteri anali wamngʼono sanasolole lupanga lake, popeza anachita mantha.

21 Tsono Zeba ndi Zalimuna anawuza Gideoni kuti, “Bwera utiphe ndiwe chifukwa uli ndi mphamvu za munthu wamkulu.” Choncho Gideoni anapita nawapha natenganso zokongoletsera zimene zinali pa makosi a ngamira zawo.

Efodi ya Gideoni

22 Aisraeli anati kwa Gideoni, “Inu muzitilamulira, mwana wanu ndi zidzukulu zanu, chifukwa mwatipulumutsa mʼmanja mwa Amidiyani.”

23 Koma Gideoni anawawuza kuti, “Sindidzakulamulirani, mwana wanganso sadzakulamulirani. Koma Yehova ndiye adzakulamulirani.” 24 Gideoni anatinso, “Ine ndikupemphani chinthu chimodzi. Aliyense wa inu andipatse ndolo zomwe anafunkha ku nkhondo.” (Adani aja anali ndi ndolo zagolide popeza anali Aismaeli).

25 Iwo anayankha kuti, “Ife tikupatsani ndithu ndolozi.” Choncho anayala chinsalu, ndipo aliyense anaponyapo ndolo zimene anafunkha. 26 Tsono kulemera kwa ndolo zagolide zimene anapereka kunali makilogalamu makumi awiri, osawerengera kulemera kwa mphande, mkanda wamʼkhosi, zovala zapepo za mafumu a Midiyani ndiponso malamba azitsulo za mʼmakosi a ngamira zawo. 27 Gideoni anagwiritsa ntchito golide uja kupanga efodi, ndipo anakamuyika ku mzinda wake ku Ofura. Tsono Aisraeli onse anasiya kupembedza Yehova nayamba kupembedza efodiyo kumeneko. Ichi chinasanduka msampha kwa Gideoni ndi banja lake lonse.

Imfa ya Gideoni

28 Choncho Amidiyani anagonjetsedwa ndi Aisraeli ndipo sanayeserenso kuwawukira. Ndipo dzikolo linakhala pa mtendere kwa zaka 40 pamene Gideoni anali ndi moyo.

29 Yeru-Baala mwana wa Yowasi anapita kukakhala kwawo. 30 Ana a Gideoni anali 70 popeza anali ndi akazi ambiri. 31 Mdzakazi wake amene anali ku Sekemu, anabereka naye mwana wamwamuna, amene anamutcha Abimeleki. 32 Gideoni mwana wa Yowasi anamwalira atakalamba ndipo anayikidwa mʼmanda a abambo ake, Yowasi ku Ofura mzinda wa Mwabiezeri.

33 Atangomwalira Gideoni, Aisraeli anayambanso kupembedza Abaala. Iwo anasandutsa Baala-Beriti kukhala mulungu wawo. 34 Aisraeli sanakumbukirenso Yehova Mulungu wawo amene anawapulumutsa mʼmanja mwa adani awo mbali zonse. 35 Ndiponso sanachite zinthu zokomera banja la Yeru-Baala (ndiye kuti Gideoni) chifukwa cha zabwino zonse zimene iye anawachitira.