Add parallel Print Page Options

Za Ufumu Wamtendere wa Mesiya

11 Padzatuluka mphukira pa tsinde la Yese
    ndipo nthambi idzaphukira kuchokera ku mizu yake.
Mzimu wa Yehova udzakhala pa iye
    Mzimu wanzeru ndi wa kumvetsa zinthu,
    Mzimu wauphungu ndi wamphamvu,
    Mzimu wachidziwitso ndi wakuopa Yehova.
Ndipo kuopa Yehova ndiye chidzakhale chinthu chomukondweretsa.

Iye sadzaweruza potsata zooneka pamaso,
    kapena kugamula mlandu potsata zakumva;
koma amphawi adzawaweruza mwachilungamo,
    adzaweruza mwachilungamo mlandu wa anthu osauka a dziko lapansi.
Iye adzakantha dziko lapansi ndi mawu ake;
    atalamula Iyeyu anthu oyipa adzaphedwa.
Chilungamo chidzakhala ngati lamba wake
    ndipo kukhulupirika kudzakhala ngati chomangira mʼchiwuno mwake.

Mʼmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wankhosa,
    kambuku adzagona pansi pamodzi ndi mwana wambuzi,
mwana wangʼombe ndi mwana wa mkango adzadyera limodzi
    ndipo mwana wamngʼono adzaziweta.
Ngʼombe yayikazi ndi chimbalangondo zidzadya pamodzi,
    ana awo adzagona pamodzi,
    ndipo mkango udzadya udzu ngati ngʼombe.
Mwana wakhanda adzasewera pa dzenje la mamba,
    ndipo mwana wamngʼono adzapisa dzanja lake ku phanga la mphiri osalumidwa.
Sipadzakhala chilichonse chopweteka kapena chowononga
    pa phiri lopatulika la Yehova,
pakuti anthu a dziko lapansi adzadzaza ndi nzeru yotha kudziwa Yehova
    monga momwe nyanja imadzazira ndi madzi.

10 Tsiku limenelo mfumu yatsopano yochokera pa Muzu wa Yese idzakhala ngati chizindikiro kwa anthu a mitundu yonse. Mitundu ya anthu idzasonkhana kwa Iye, ndipo malo awo okhalapo adzakhala aulemerero. 11 Tsiku limenelo Ambuye adzatambasula dzanja lake kachiwiri kuti awombole anthu ake otsalira ku Asiriya, ku Igupto, ku Patirosi, Kusi, ku Elamu, ku Sinana, ku Hamati ndi pa zilumba za nyanja yamchere.

12 Adzakwezera mitundu ya anthu mbendera,
    ndipo adzasonkhanitsa otayika a ku Israeli;
Iye adzasonkhanitsa anthu obalalika a ku Yuda
    kuchokera ku mbali zonse zinayi za dziko lapansi.
13 Nsanje ya Efereimu idzatha,
    ndipo adani a Yuda adzatha;
Efereimu sadzachitira nsanje Yuda,
    ngakhale Yuda sadzamuda Efereimu.
14 Yuda ndi Efereimu adzathira nkhondo pa Afilisti mbali ya kumadzulo;
    ndipo onsewo pamodzi adzalanda zinthu za anthu a kummawa.
Adzalimbana ndi Edomu ndi Mowabu,
    ndipo Aamoni adzawagonjera.
15 Yehova adzaphwetsa
    mwendo wa nyanja ya Igupto;
adzatambasula dzanja lake ndipo adzawombetsa mphepo yotentha
    pa mtsinje wa Yufurate.
Iye adzawugawa mtsinjewo kukhala timitsinje tisanu ndi tiwiri
    kuti anthu athe kuwoloka powuma atavala nsapato.
16 Padzakhala msewu waukulu woti ayendepo anthu ake otsalira
    amene anatsalira ku Asiriya,
monga mmene panali msewu waukulu woyendapo Israeli
    pamene amachokera ku Igupto.