Add parallel Print Page Options

Ufumu Wachilungamo

32 Taonani, kudzakhala mfumu ina imene idzalamulira mwachilungamo,
    ndipo akalonga ake adzaweruza molungama.
Munthu aliyense adzakhala ngati pothawirapo mphepo
    ndi malo obisalirapo namondwe,
adzakhala ngati mitsinje ya mʼchipululu,
    ngati mthunzi wa thanthwe lalikulu la mʼdziko lowuma.

Ndipo maso a anthu openya sadzakhalanso otseka,
    ndipo makutu a anthu akumva adzamvetsetsa.
Anthu a mtima wopupuluma adzadziwa ndi kuchita zinthu mofatsa,
    ndipo anthu ovutika kuyankhula adzayankhula mosadodoma ndi momveka.
Chitsiru sichidzatchedwanso munthu waulemu wake
    ndipo munthu woyipa sadzalemekezedwa.
Pakuti munthu opusa amayankhula zauchitsiru,
    amaganiza kuchita zoyipa:
Iye amachita zoyipira Mulungu,
    ndipo amafalitsa zolakwika zokhudza Yehova;
anjala sawapatsa chakudya
    ndipo aludzu sawapatsa madzi.
Munthu woyipa njira zake ndi zoyipanso,
    iye kwake nʼkulingalira zinthu zoyipa.
Amalingalira zakuti awononge anthu aumphawi ndi mabodza ake
    ngakhale kuti waumphawiyo akuyankhula zoona.
Koma munthu wolemekezeka amalingaliranso kuchita zinthu zabwino,
    Iye amakhazikika pa zinthu zabwinozo.

Akazi a ku Yerusalemu

Khalani maso, inu akazi
    amene mukungokhala wopanda kulingalira kuti kunja kulinji
ndipo imvani mawu anga.
    Inu akazi odzitama, imvani zimene ndikunena!
10 Pakapita chaka ndi masiku pangʼono
    inu akazi amatama mudzanjenjemera;
chifukwa mitengo ya mphesa idzakanika
    ndipo zipatso sizidzaoneka.
11 Nthunthumirani inu okhala mosatekesekanu;
    ndipo njenjemerani, inu akazi omadzikhulupirira nokhanu.
Vulani zovala zanu,
    ndipo valani ziguduli mʼchiwuno mwanu.
12 Dzigugudeni pachifuwa mwachisoni chifukwa minda yachonde,
    ndi mphesa yawonongeka.
13 Mʼdziko la anthu anga
    mwamera minga ndi mkandankhuku.
Zoona, mulilire nyumba zonse zachikondwerero
    ndi mzinda uno umene unali wachisangalalo.
14 Nyumba yaufumu idzasiyidwa,
    mzinda waphokoso udzakhala wopanda anthu;
malinga ndi nsanja zidzasanduka chipululu mpaka muyaya.
    Abulu adzasangalalamo ndipo ziweto zidzapezamo msipu.
15 Yehova adzatipatsa mzimu wake,
    ndipo dziko lachipululu lidzasanduka munda wachonde,
    ndipo munda wachonde udzakhala ngati nkhalango.
16 Tsono mʼchipululu mudzakhala chiweruzo cholungama
    ndipo mʼminda yachonde mudzakhala chilungamo.
17 Mtendere udzakhala chipatso chachilungamo;
    zotsatira za chilungamo zidzakhala bata ndi kudzidalira mpaka muyaya.
18 Anthu anga adzakhala mʼmidzi yamtendere,
    mʼnyumba zodalirika,
    ndi malo osatekeseka a mpumulo.
19 Ngakhale nkhalango idzawonongedwa ndi matalala
    ndipo mzinda udzagwetsedwa mpaka pansi,
20 inutu mudzakhala odalitsika ndithu.
    Mudzadzala mbewu zanu mʼmbali mwa mtsinje uliwonse,
    ndipo ngʼombe zanu ndi abulu anu zidzadya paliponse.