Add parallel Print Page Options

Msautso ndi Thandizo

33 Tsoka kwa iwe, iwe wowonongawe,
    amene sunawonongedwepo!
Tsoka kwa iwe, iwe mthirakuwiri,
    iwe amene sunanyengedwepo!
Iwe ukadzaleka kuwononga,
    udzawonongedwa,
ukadzasiya umʼthirakuwiri, adzakuwononga,
    ndipo ukadzaleka kuchita zachinyengo adzakunyenga.

Inu Yehova, mutikomere mtima ife;
    tikulakalaka Inu.
Tsiku ndi tsiku mutitchinjirize ndi mkono wanu,
    ndipo mutipulumutse pa nthawi ya masautso.
Mukatulutsa liwu lanu longa bingu mitundu ya anthu imathawa;
    pamene Inu mwadzambatuka mitundu ya anthu imabalalika.
Zofunkha za ku nkhondo za mitundu ina Aisraeli adzazisonkhanitsa ngati mmene limachitira dzombe.
    Iwo adzalumphira zofunkhazo monga mmene limachitira dzombe.

Yehova wakwezeka kwambiri pakuti amakhala pamwamba pa zonse
    adzadzaza Ziyoni ndi chilungamo ndi chipulumutso.
Iye adzakupatsani mtendere pa nthawi yanu,
    adzakupatsani chipulumutso chochuluka, nzeru zambiri ndi chidziwitso chochuluka;
    kuopa Yehova ngati madalitso.

Taonani, anthu awo amphamvu akulira mofuwula mʼmisewu;
    akazembe okhazikitsa mtendere akulira kwambiri.
Mʼmisewu yayikulu mulibe anthu,
    mʼmisewu mulibe anthu a paulendo.
Mdaniyo ndi wosasunga pangano.
    Iye amanyoza mboni.
    Palibe kulemekezana.
Dziko likulira ndipo likunka likutha.
    Nkhalango ya Lebanoni ikuchita manyazi, yafota.
Chigwa cha chonde cha Saroni chasanduka chachidalala.
    Masamba a mitengo ya ku Basani ndi Karimeli akuyoyoka.

10 Yehova akunena kuti, “Tsopano ndidzadzambatuka
    ndipo ndidzaonetsa mphamvu zanga,
    ndipo ndidzakwezedwa.
11 Zolingalira zanu nʼzachabechabe
    ngati udzu wamanyowa.
    Mpweya wamoto udzakupserezani.
12 Anthu a mitundu ina adzatenthedwa ngati miyala ya njereza;
    ndi ngati minga yodulidwa.”

13 Inu amene muli kutali, imvani zimene ndachita;
    inu amene muli pafupi, dziwani mphamvu zanga
14 Mu mzinda wa Ziyoni anthu ochimwa agwidwa ndi mantha;
    anthu osapembedza Mulungu akunjenjemera:
Iwo akunena kuti, “Ndani wa ife angathe kukhala mʼmoto wonyeketsa?
    Ndani wa ife angathe kukhala moto wosatha?”
15 Angathe kuti ndi amene amachita zolungama
    ndi kuyankhula zoona,
amene amakana phindu lolipeza monyenga
    ndipo salola manja ake kulandira ziphuphu,
amene amatseka makutu ake kuti angamve mawu opangana kupha anzawo
    ndipo amatsinzina kuti angaone zoyipa.
16 Munthu wotere ndiye adzakhale pa nsanja,
    kothawira kwake kudzakhala mʼmalinga a mʼmapiri.
Azidzalandira chakudya chake
    ndipo madzi sadzamusowa.

17 Nthawi imeneyo maso a ana adzaona mfumu ya maonekedwe wokongola
    ndi kuona dziko lotambasukira kutali.
18 Mu mtima mwanu muzidzalingalira zoopsa zinachitika kale zija:
    “Ali kuti mkulu wa Asilikali uja?
    Ali kuti wokhometsa misonkho uja?
    Ali kuti mkulu woyangʼanira nsanja?”
19 Simudzawaonanso anthu odzikuza aja,
    anthu aja achiyankhulo chosadziwika,
    chachilendo ndi chosamveka.

20 Taonani Ziyoni, mzinda wa zikondwerero zachipembedzo chathu;
    maso anu adzaona Yerusalemu,
    mzinda wamtendere, tenti imene sidzachotsedwa,
zikhomo zake sizidzazulidwa,
    kapena zingwe zake kuduka.
21 Kumeneko Yehova adzaonetsa ulemerero wake
    ndipo mzindawo udzakhala kasupe wa mitsinje yayikulu.
Ngalawa za zopalasa sizidzapitamo,
    sitima zapamadzi zikuluzikulu sizidzayendamo.
22 Pakuti Yehova ndi woweruza wathu,
    Yehova ndiye wotilamulira,
Yehova ndiye mfumu yathu;
    ndipo ndiye amene adzatipulumutse.

23 Zingwe za sitima zapamadzi za adani athu zamasuka,
    sizikutha kulimbitsa mlongoti wake,
    matanga ake sakutheka kutambasuka.
Ngakhale tidzagawana zofunkha zochuluka kwambiri
    ndipo ngakhale olumala adzatenga zofunkhazo.
24 Palibe ndi mmodzi yemwe wokhala mʼZiyoni adzanene kuti, “Ndikudwala”
    ndipo anthu onse okhala mʼmenemo machimo awo adzakhululukidwa.