Add parallel Print Page Options

Kudwala kwa Hezekiya

38 Nthawi imeneyo Mfumu Hezekiya anadwala ndipo anali pafupi kufa. Mneneri Yesaya mwana wa Amozi anapita kukamuona ndipo anati “Yehova akuti: Konza bwino nyumba yako, pakuti ukufa; suchira.”

Hezekiya anatembenuka nayangʼana kukhoma, napemphera kwa Yehova kuti, “Inu Yehova, kumbukirani momwe ndayendera pamaso panu mokhulupirika ndi modzipereka ndipo ndakhala ndikuchita zabwino pamaso panu.” Ndipo Hezekiya analira mosweka mtima.

Ndipo Yehova analamula Yesaya kuti: “Pita kwa Hezekiya ndipo ukamuwuze kuti, ‘Yehova, Mulungu wa kholo lake Davide akuti: Ndamva pemphero lako ndipo misozi yako ndayiona; ndidzakuwonjezera zaka 15 pa moyo wako. Ndipo ndidzakupulumutsa, iwe pamodzi ndi mzindawu mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya, Ine ndidzawuteteza mzindawu.

“ ‘Ichi ndi chizindikiro cha Yehova kwa iwe kutsimikiza kuti Yehova adzachita zimene walonjeza: Chithunzithunzi chimene dzuwa likuchititsa pa makwerero a Ahazi ndidzachibweza mʼmbuyo makwerero khumi.’ ” Ndipo chithunzithunzi chinabwerera mʼmbuyo makwerero khumi.

Ndakatulo ya Hezekiya mfumu ya ku Yuda imene analemba atadwala ndi kuchira:

10 Ine ndinaganiza kuti
    ndidzapita ku dziko la akufa
    pamene moyo ukukoma.
11 Ndinaganiza kuti, “Sindidzaonanso Yehova,
    mʼdziko la anthu amoyo,
sindidzaonanso mtundu wa anthu
    kapena kukhala pamodzi ndi amene amakhala pa dziko lapansi lino.
12 Nyumba yanga yasasuka
    ndipo yachotsedwa.
Ngati tenti ya mʼbusa mwapindapinda moyo wanga,
    ngati munthu wowomba nsalu;
    kuyambira usana mpaka usiku mwakhala mukundisiya.
13 Ndinkalira kupempha chithandizo usiku wonse mpaka mmawa;
    koma Inu Yehova munaphwanya mafupa anga ngati mkango,
    ndipo mwakhala mukundisiya.
14 Ndinkalira ngati namzeze kapena chumba,
    ndinkabuwula ngati nkhunda yodandaula.
Maso anga anatopa nʼkuyangʼana mlengalenga.
    Inu Ambuye, ine ndili mʼmavuto bwerani mudzandithandize!”

15 Koma ine ndinganene chiyani?
    Yehova wayankhula nane, ndipo Iye ndiye wachita zimenezi.
Chifukwa cha kuwawa kwa mtima wanga,
    ine ndidzayenda modzichepetsa masiku amoyo wanga onse.
16 Ambuye, masiku anga ali mʼmanja mwanu.
    Mzimu wanga upeza moyo mwa Inu.
Munandichiritsa ndi
    kundikhalitsa ndi moyo.
17 Ndithudi, ine ndinamva zowawa zotere
    kuti ndikhale ndi moyo;
Inu munandisunga
    kuti ndisapite ku dzenje la chiwonongeko
chifukwa mwakhululukira
    machimo anga onse.
18 Pakuti akumanda sangathe kukutamandani,
    akufa sangayimbe nyimbo yokutamandani.
Iwo amene akutsikira ku dzenje
    sangakukhulupirireni.
19 Amoyo, amoyo okha ndiwo amakutamandani,
    monga mmene ndikuchitira ine lero lino;
abambo amawuza ana awo za
    kukhulupirika kwanu.

20 Yehova watipulumutsa.
    Tiyeni tiyimbe ndi zoyimbira za zingwe
masiku onse a moyo wathu
    mʼNyumba ya Yehova.

21 Yesaya anati, “Anthu atenge mʼbulu wankhunyu ndipo apake pa chithupsacho ndipo Hezekiya adzachira.”

22 Hezekiya nʼkuti atafunsa kuti, “Kodi chizindikiro chako nʼchiyani chotsimikiza kuti ndidzapita ku Nyumba ya Yehova?”