Add parallel Print Page Options

Mawu a Yobu

26 Pamenepo Yobu anayankha kuti,

“Wamuthandizadi munthu wopanda mphamvu!
    Walimbitsadi dzanja la munthu wofowoka!
Wapereka malangizo kwa munthu amene alibe nzeru!
    Ndipotu waonetsadi nzeru zochuluka!
Kodi wakuthandiza ndani kuti uyankhule mawu awa?
    Ndipo ndi mzimu wa yani umene unayankhula pakamwa pako?

“Mizimu ya anthu akufa ikunjenjemera pansi pa madzi,
    ndi zonse zokhala mʼmadzimo.
Dziko la anthu akufa ndi lapululu pamaso pa Mulungu;
    chiwonongeko ndi chosaphimbidwa.
Mulungu anayala thambo la kumpoto pa phompho;
    Iye anakoloweka dziko lapansi mʼmalo mwake pamene panali popanda nʼkanthu komwe.
Amasunga madzi ambiri mʼmitambo yake,
    koma mitamboyo siphulika chifukwa cha kulemera kwa madziwo.
Iye amaphimba mwezi wowala,
    amawuphimba ndi mitambo yake.
10 Mulungu anawalembera madzi malire wonga uta,
    kukhala malire pakati pa kuwunika ndi mdima.
11 Mizati yochirikiza mitambo yakumwamba imanjenjemera,
    ndi kudabwa pa kudzudzula kwake.
12 Ndi mphamvu zake anatontholetsa nyanja;
    ndi nzeru zake anakantha chirombo cha mʼmadzi chija chotchedwa Rahabe.
13 Ndi mpweya wake anayeretsa zamumlengalenga,
    dzanja lake linapha chinjoka chothawa chija.
14 Zimenezi ndi pangʼono chabe mwa ntchito yake;
    tingomva pangʼono za Iye ngati kunongʼona!
    Kodi ndani angathe kudziwa kukula kwa mphamvu zake?”