Add parallel Print Page Options

27 Ndipo Yobu anapitiriza kuyankhula kwake:

“Ndithu pali Mulungu wamoyo, amene wakana kundiweruza molungama,
    Wamphamvuzonse, amene wawawitsa mtima wanga,
nthawi zonse pamene ndili ndi moyo,
    mpweya wa Mulungu uli mʼmphuno mwanga,
pakamwa panga sipadzatuluka mawu oyipa,
    lilime langa silidzayankhula zachinyengo.
Sindidzavomereza kuti inu mukunena zoona;
    mpaka imfa yanga, sindidzataya ungwiro wanga.
Ndidzasunga chilungamo changa ndipo sindidzalola kuti chindichokere;
    chikumbumtima changa sichidzanditsutsa nthawi yonse ya moyo wanga.

“Mdani wanga akhale ngati woyipa,
    wondiwukira akhale ngati munthu wosalungama!
Nanga chiyembekezo cha munthu wosapembedza nʼchiyani pamene aphedwa,
    pamene Mulungu achotsa moyo wake?
Kodi Mulungu amamva kulira kwake
    pamene zovuta zamugwera?
10 Kodi adzapeza chikondwerero mwa Wamphamvuzonse?
    Kodi adzapemphera kwa Mulungu nthawi zonse?

11 “Ndidzakuphunzitsani za mphamvu ya Mulungu ndipo
    sindidzabisa njira za Wamphamvuzonse.
12 Inu mwadzionera nokha zonsezi.
    Nanga bwanji mukuyankhula zopanda pake?

13 “Pano pali chilango chimene Mulungu amasungira woyipa,
    cholowa chimene munthu wankhanza amalandira kuchokera kwa Wamphamvuzonse.
14 Angakhale ana ake achuluke chotani adzaphedwa ndi lupanga ndipo
    zidzukulu zake zidzasowa zakudya.
15 Amene adzatsalireko adzafa ndi mliri,
    ndipo akazi awo amasiye sadzawalira.
16 Ngakhale aunjike siliva ngati fumbi,
    ndi kukundika zovala ngati mchenga,
17 zimene wasungazo wolungama ndiye adzavale,
    ndipo anthu osalakwa ndiwo adzagawane siliva wakeyo.
18 Nyumba imene akuyimanga ili ngati mokhala kadziwotche,
    ili ngati msasa umene mlonda amamanga.
19 Amapita kokagona ali wolemera koma kutha kwake nʼkomweko;
    akatsekula maso ake, chuma chake chonse chapita.
20 Zoopsa zimamukokolola ngati madzi achigumula;
    mphepo yamkuntho imamunyamula usiku.
21 Mphepo ya kummawa imamuwulutsa ndipo iye saonekanso ndipo
    imamuchotsa pamalo pake.
22 Imakuntha pa iye osamuchitira chisoni,
    pamene akuyesa kuthawa mphamvu zake mwaliwiro.
23 Mphepoyo imamuwomba ndithu
    ndipo kuchokera pamalo pake imamuopseza.”