Add parallel Print Page Options

BUKU LACHIWIRI

Masalimo 42–72

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya ana a Kora.

42 Monga mbawala ipuma wefuwefu kufunafuna mitsinje yamadzi,
    kotero moyo wanga upuma wefuwefu kufunafuna Inu Mulungu.
Moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Mulungu, lofuna Mulungu wamoyo.
    Kodi ndipite liti kukakumana ndi Mulungu?
Misozi yanga yakhala chakudya changa
    usana ndi usiku,
pamene anthu akunena kwa ine tsiku lonse kuti,
    “Mulungu wako ali kuti?”
Zinthu izi ndimazikumbukira
    pamene ndikukhuthula moyo wanga:
momwe ndinkapitira ndi gulu lalikulu,
    kutsogolera mayendedwe a ku Nyumba ya Mulungu
ndi mfuwu yachimwemwe ndi mayamiko
    pakati pa anthu a pa chikondwerero.

Nʼchifukwa chiyani uli ndi chisoni, iwe moyo wanga?
    Nʼchifukwa chiyani wakhumudwa iwe mʼkati mwanga?
Yembekezera Mulungu,
    pakuti ndidzamulambirabe,
Mpulumutsi wanga ndi     Mulungu wanga.

Moyo wanga uli ndi chisoni mʼkati mwanga
    kotero ndidzakumbukira Inu
kuchokera ku dziko la Yorodani,
    ku mitunda ya Herimoni kuchokera ku phiri la Mizara.
Madzi akuya akuyitana madzi akuya
    mu mkokomo wa mathithi anu;
mafunde anu onse obwera mwamphamvu
    andimiza.

Koma usana Yehova amalamulira chikondi chake,
    nthawi ya usiku nyimbo yake ili nane;
    pemphero kwa Mulungu wa moyo wanga.

Ine ndikuti kwa Mulungu Thanthwe langa,
    “Nʼchifukwa chiyani mwandiyiwala?
Nʼchifukwa chiyani ndiyenera kuyenda ndikulira,
    woponderezedwa ndi mdani?”
10 Mafupa anga ali ndi ululu wakufa nawo
    pamene adani anga akundinyoza,
tsiku lonse akunena kuti,
    “Mulungu wako ali kuti?”

11 Bwanji ukumva chisoni,
    iwe mtima wanga?
Chifukwa chiyani ukuvutika chonchi mʼkati mwanga?
    Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamutamandanso,
    Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.
43 Onetsani kusalakwa kwanga Inu Mulungu;
    ndipo mundinenere mlandu wanga kutsutsana ndi mtundu wosapembedza;
    mundilanditse mʼmanja mwa achinyengo ndi anthu oyipa.
Pajatu Inu Mulungu ndinu mphamvu zanga.
    Nʼchifukwa chiyani mwandikana ine?
Nʼchifukwa chiyani ndiyenera kuyenda ndikulira,
    woponderezedwa ndi mdani?
Tumizani kuwunika kwanu ndi choonadi chanu
    kuti zinditsogolere;
mulole kuti zindifikitse ku phiri lanu loyera,
    kumalo kumene inu mumakhala.
Ndipo ndidzapita ku guwa lansembe la Mulungu,
    kwa Mulungu, chimwemwe changa ndi chikondwerero changa.
Ndidzakutamandani ndi zeze,
    Inu Mulungu wanga.

Nʼchifukwa chiyani uli ndi chisoni iwe moyo wanga?
    Nʼchifukwa chiyani wakhumudwa iwe mʼkati mwanga?
Khulupirira Mulungu,
    pakuti ndidzamutamandabe Iye,
    Mpulumutsi wanga ndi Mulungu wanga.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya ana a Kora.

44 Ife tamva ndi makutu athu, Inu Mulungu;
    makolo athu atiwuza
zimene munachita mʼmasiku awo,
    masiku akalekalewo.
Ndi dzanja lanu munathamangitsa mitundu ya anthu ena
    ndi kudzala makolo athu;
Inu munakantha mitundu ya anthu,
    koma makolo athuwo Inu munawapatsa ufulu.
Sanalande dziko ndi lupanga lawo,
    si mkono wawo umene unawabweretsera chigonjetso,
koma ndi dzanja lanu lamanja, mkono wanu ndi kuwala kwa nkhope yanu,
    pakuti munawakonda.

Inu ndinu Mfumu yanga ndi Mulungu wanga
    amene mumalamulira chigonjetso cha Yakobo.
Kudzera kwa inu ife timabweza adani athu;
    kudzera mʼdzina lanu timapondereza otiwukirawo.
Sindidalira uta wanga,
    lupanga langa silindibweretsera chigonjetso;
koma Inu mumatigonjetsera adani athu,
    mumachititsa manyazi amene amadana nafe.
Timanyadira mwa Mulungu wathu tsiku lonse,
    ndipo tidzatamanda dzina lanu kwamuyaya.

Koma tsopano mwatikana ndi kutichepetsa;
    Inu simupitanso ndi ankhondo athu.
10 Munachititsa ife kubwerera mʼmbuyo pamaso pa mdani
    ndipo amene amadana nafe atilanda katundu.
11 Inu munatipereka kuti tiwonongedwe monga nkhosa
    ndipo mwatibalalitsa pakati pa anthu a mitundu ina.
12 Inu munagulitsa anthu anu pa mtengo wotsika,
    osapindulapo kanthu pa malondawo.

13 Mwachititsa kuti tikhale chochititsa manyazi kwa anthu a mitundu ina,
    chonyozeka ndi chothetsa nzeru kwa iwo amene atizungulira.
14 Mwachititsa kuti tikhale onyozeka pakati pa anthu a mitundu ina;
    anthu amapukusa mitu yawo akationa.
15 Manyazi anga ali pamaso panga tsiku lonse
    ndipo nkhope yanga yaphimbidwa ndi manyazi
16 chifukwa cha mawu otonza a iwo amene amandinyoza ndi kundichita chipongwe,
    chifukwa cha mdani amene watsimikiza kubwezera.

17 Zonsezi zinatichitikira
    ngakhale kuti ifeyo sitinayiwale Inu
    kapena kuonetsa kusakhulupirika pa pangano lanu.
18 Mitima yathu sinabwerere mʼmbuyo;
    mapazi athu sanatayike pa njira yanu.
19 Koma Inu mwatiphwanya ndi kuchititsa kuti tikhale ozunzidwa ndi ankhandwe
    ndipo mwatiphimba ndi mdima waukulu.

20 Tikanayiwala dzina la Mulungu wathu
    kapena kutambasulira manja athu kwa mulungu wachilendo,
21 kodi Mulungu wathu sakanazidziwa zimenezi,
    pakuti Iye amadziwa zinsinsi zamumtima?
22 Komabe chifukwa cha Inu timakumana ndi imfa tsiku lonse,
    tili ngati nkhosa zoyenera kuti ziphedwe.

23 Dzukani Ambuye! Nʼchifukwa chiyani mukugona!
    Dziwutseni nokha! Musatikane kwamuyaya.
24 Nʼchifukwa chiyani mukubisa nkhope yanu,
    ndi kuyiwala mavuto athu ndi kuponderezedwa kwathu?

25 Tatsitsidwa pansi mpaka pa fumbi;
    matupi athu amatirira pa dothi.
26 Imirirani ndi kutithandiza,
    tiwomboleni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.

Kwa mtsogoleri wamayimbidwe. Monga mwa mayimbidwe a “Maluwa a Kakombo.” Salimo la ana a Kora. Nyimbo ya pa ukwati.

45 Mtima wanga watakasika ndi nkhani yokoma
    pamene ndikulakatula mawu anga kwa mfumu;
    lilime langa ndi cholembera cha wolemba waluso.

Inu ndinu abwino kwambiri kuposa anthu onse
    ndipo milomo yanu inadzozedwa ndi chikondi cha Mulungu chosasinthika,
    popeza Mulungu wakudalitsani kwamuyaya.
Mangirirani lupanga lanu mʼchiwuno mwanu, inu munthu wamphamvu;
    mudziveke nokha ndi ulemerero ndi ukulu wanu.
Mu ukulu wanu mupite mutakwera mwachigonjetso
    mʼmalo mwa choonadi, kudzichepetsa ndi chilungamo;
    dzanja lanu lamanja lionetsere ntchito zanu zoopsa.
Mivi yanu yakuthwa ilase mitima ya adani a mfumu,
    mitundu ya anthu igwe pansi pa mapazi anu.
Mpando wanu waufumu, Inu Mulungu, udzakhala ku nthawi za nthawi;
    ndodo yaufumu yachilungamo idzakhala ndodo yaufumu ya ufumu wanu.
Inu mumakonda chilungamo ndi kudana ndi zoyipa;
    choncho Mulungu, Mulungu wanu, wakukhazikani pamwamba pa anzanu
    pokudzozani ndi mafuta a chimwemwe.
Mikanjo yanu yonse ndi yonunkhira ndi mure ndi aloe ndi kasiya;
    kuchokera ku nyumba zaufumu zokongoletsedwa ndi mnyanga wanjovu
    nyimbo za zoyimbira zazingwe zimakusangalatsani.
Ana aakazi a mafumu ali pakati pa akazi anu olemekezeka;
    ku dzanja lanu lamanja kuli mkwatibwi waufumu ali mu golide wa ku Ofiri.

10 Tamvera, iwe mwana wa mkazi ganizira ndipo tchera khutu;
    iwala anthu ako ndi nyumba ya abambo ako.
11 Mfumu yathedwa nzeru chifukwa cha kukongola kwako;
    mulemekeze pakuti iyeyo ndiye mbuye wako.
12 Mwana wa mkazi wa ku Turo adzabwera ndi mphatso,
    amuna a chuma adzafunafuna kukoma mtima kwako.

13 Wokongola kwambiri ndi mwana wa mfumu ali mʼchipinda mwake,
    chovala chake ndi cholukidwa ndi thonje ndi golide.
14 Atavala zovala zamaluwamaluwa akupita naye kwa mfumu;
    anamwali okhala naye akumutsatira
    ndipo abweretsedwa kwa inu.
15 Iwo akuwaperekeza ndi chimwemwe ndi chisangalalo;
    akulowa mʼnyumba yaufumu.

16 Ana ako aamuna adzatenga malo a makolo ako;
    udzachititsa kuti akhale ana a mfumu mʼdziko lonse.
17 Ndidzabukitsa mbiri yako mʼmibado yonse;
    choncho mitundu yonse idzakutamanda ku nthawi za nthawi.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya ana a Kora. Nyimbo ya anamwali.

46 Mulungu ndiye kothawira kwathu ndi mphamvu yathu,
    thandizo lopezekeratu pa nthawi ya mavuto.
Nʼchifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisunthike,
    ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja,
ngakhale madzi ake atakokoma ndi kuchita thovu,
    ngakhale mapiri agwedezeke ndi kukokoma kwake.

Kuli mtsinje umene njira zake za madzi zimasangalatsa mzinda wa Mulungu,
    malo oyera kumene Wammwambamwamba amakhalako.
Mulungu ali mʼkati mwake, iwo sudzagwa;
    Mulungu adzawuthandiza mmawa.
Mitundu ikupokosera, mafumu akugwa;
    Iye wakweza mawu ake, dziko lapansi likusungunuka.

Yehova Wamphamvuzonse ali ndi ife,
    Mulungu wa Yakobo ndi linga lathu.

Bwerani kuti mudzaone ntchito za Yehova,
    chiwonongeko chimene wachibweretsa pa dziko lapansi.
Iye amathetsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi;
    Iye amathyola uta ndi kupindapinda mkondo;
    amatentha zishango ndi moto.
10 Iye akuti, “Khala chete, ndipo dziwa kuti ndine Mulungu;
    ndidzakwezedwa pakati pa mitundu ya anthu;
    ine ndidzakwezedwa mʼdziko lapansi.”

11 Yehova Wamphamvuzonse ali ndi ife,
    Mulungu wa Yakobo ndi linga lathu.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la ana a Kora.

47 Ombani mʼmanja, inu anthu onse;
    fuwulani kwa Mulungu ndi mawu achimwemwe.
Ndi woopsadi Yehova Wammwambamwamba;
    Mfumu yayikulu ya dziko lonse lapansi!
Iye anatigonjetsera mitundu yambirimbiri ya anthu;
    anayika anthu pansi pa mapazi athu.
Iye anatisankhira cholowa chathu,
    chonyaditsa cha Yakobo, amene anamukonda.
            Sela

Mulungu wakwera, anthu akumufuwulira mwachimwemwe,
    Yehova wakwera, akumuyimbira malipenga.
Imbani matamando kwa Mulungu, imbani matamando;
    imbani matamando kwa mfumu yathu, imbani matamando.

Pakuti Mulungu ndi mfumu ya dziko lonse lapansi;
    imbirani Iye salimo la matamando.
Mulungu akulamulira mitundu ya anthu;
    Mulungu wakhala pa mpando wake waufumu woyera.
Anthu otchuka mwa anthu a mitundu ina asonkhana
    monga anthu a Mulungu wa Abrahamu,
pakuti mafumu a dziko lapansi ndi ake a Mulungu;
    Iye wakwezedwa kwakukulu.

Nyimbo. Salimo la ana a Kora.

48 Wamkulu ndi Yehova, ndi woyenera kwambiri matamando
    mu mzinda wa Mulungu wathu, phiri lake loyera.
Lokongola mu utali mwake,
    chimwemwe cha dziko lonse lapansi.
Malo aatali kwambiri a Zafoni ndiye Phiri la Ziyoni,
    mzinda wa Mfumu yayikulu.
Mulungu ali mu malinga ake;
    Iye wadzionetsa yekha kuti ndiye malinga akewo.

Pamene mafumu anasonkhana pamodzi,
    pamene anayendera pamodzi kudzalimbana nafe,
iwo anaona mzindawo ndipo anadabwa kwambiri;
    anathawa ndi mantha aakulu.
Pomwepo anagwidwa nako kunjenjemera,
    ululu wonga wa mkazi woyembekezera pa nthawi yochira.
Inu munawawononga monga sitima zapamadzi za ku Tarisisi
    zitawonongeka ndi mphepo ya kummawa.

Monga momwe tinamvera,
    kotero ife tinaona
mu mzinda wa Yehova Wamphamvuzonse,
    mu mzinda wa Mulungu wathu.
    Mulungu adzawuteteza kwamuyaya.

Mʼkati mwa Nyumba yanu Mulungu,
    ife timalingaliramo zachikondi chanu chosasinthika.
10 Monga dzina lanu, Inu Mulungu,
    matamando anu amafika ku malekezero a dziko lapansi
    dzanja lanu lamanja ladzaza ndi chilungamo.
11 Phiri la Ziyoni likukondwera,
    midzi ya Yuda ndi yosangalala
    chifukwa cha maweruzo anu.

12 Yendayendani mu Ziyoni, uzungulireni mzindawo,
    werengani nsanja zake.
13 Yangʼanitsitsani bwino mipanda yake,
    penyetsetsani malinga ake,
    kuti mudzafotokoze za izo ku mʼbado wotsatira.
14 Pakuti Mulungu uyu ndi Mulungu wathu ku nthawi zosatha;
    Iye adzakhala mtsogoleri wathu mpaka ku mapeto.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la ana a Kora.

49 Imvani izi anthu a mitundu yonse;
    mvetserani, nonse amene mumakhala pa dziko lonse,
anthu wamba pamodzi ndi anthu odziwika,
    olemera pamodzinso ndi osauka:
Pakamwa panga padzayankhula mawu anzeru;
    mawu ochokera mu mtima mwanga adzapereka nzeru.
Ndidzatchera khutu langa ku mwambo,
    ndi pangwe ndidzafotokoza momveka mwambi wanga.

Ine ndichitirenji mantha pamene masiku oyipa afika,
    pamene achinyengo oyipa andizungulira.
Iwo amene adalira kulemera kwawo
    ndi kutamandira kuchuluka kwa chuma chawo?
Palibe munthu amene angawombole moyo wa mnzake
    kapena kuperekera mnzake dipo kwa Mulungu.
Dipo la moyo ndi la mtengowapatali,
    palibe malipiro amene angakwanire,
kuti iye akhale ndi moyo mpaka muyaya
    ndi kusapita ku manda.

10 Pakuti onse amaona kuti anthu anzeru amamwalira;
    opusa ndi opanda nzeru chimodzimodzinso amawonongeka
    ndipo amasiyira chuma chawo anthu ena.
11 Manda awo adzakhala nyumba zawo mpaka muyaya,
    malo awo okhalako kwa nthawi yonse ya mibado yawo,
    ngakhale anatchula malo mayina awo.

12 Ngakhale munthu akhale wachuma chotani,
    adzafa ngati nyama.

13 Izi ndi zimene zimachitikira iwo amene amadzidalira okha,
    ndi owatsatira awo amene amavomereza zimene amayankhula.
            Sela
14 Monga nkhosa iwo ayenera kupita ku manda,
    ndipo imfa idzawadya.
Olungama adzawalamulira mmawa;
    matupi awo adzavunda mʼmanda,
    kutali ndi nyumba zawo zaufumu.
15 Koma Mulungu adzawombola moyo wanga kuchoka ku manda;
    ndithu Iye adzanditengera kwa Iye mwini.

16 Usavutike mu mtima pamene munthu akulemera,
    pamene ulemerero wa nyumba yake ukuchulukirachulukira;
17 Pakuti sadzatenga kanthu pamodzi naye pamene wamwalira,
    ulemerero wake sudzapita pamodzi naye.
18 Ngakhale pamene munthuyo ali moyo amadziyesa wodala,
    ndipo ngakhale atamandidwe pamene zinthu zikumuyendera bwino,
19 iyeyo adzakakhala pamodzi ndi mʼbado wa makolo ake,
    amene sadzaonanso kuwala.

20 Munthu amene ali ndi chuma koma wopanda nzeru
    adzafa ngati nyama yakuthengo.

Salimo la Asafu.

50 Wamphamvuyo, Yehova Mulungu,
    akuyankhula ndi kuyitanitsa dziko lapansi
    kuyambira kotulukira dzuwa mpaka kumene limalowera.
Kuchokera ku Ziyoni, mokongola kwambiri
    Mulungu akuwala.
Mulungu wathu akubwera ndipo sadzakhala chete;
    moto ukunyeketsa patsogolo pake,
    ndipo pomuzungulira pali mphepo yamkuntho
Iye akuyitanitsa zamumlengalenga
    ndi za pa dziko lapansi kuti aweruze anthu ake.
Mundisonkhanitsire okhulupirika anga,
    amene anachita pangano ndi ine pochita nsembe.
Ndipo mayiko akumwamba akulengeza chilungamo chake,
    pakuti Mulungu mwini ndi woweruza.

Imvani inu anthu anga, ndipo Ine ndidzayankhula,
    iwe Israeli, ndipo Ine ndidzayankhula mokutsutsa;
    ndine Mulungu, Mulungu wako.
Sindikudzudzula chifukwa cha nsembe zako,
    kapena nsembe zako zopsereza zimene zili pamaso panga nthawi zonse.
Ine sindikufuna ngʼombe yayimuna kuchokera mʼkhola lako
    kapena mbuzi za mʼkhola lako,
10 pakuti nyama iliyonse yakunkhalango ndi yanga
    ndiponso ngʼombe za ku mapiri ochuluka.
11 Ine ndimadziwa mbalame iliyonse mʼmapiri
    ndiponso zolengedwa zonse zakutchire ndi zanga.
12 Ndikanakhala ndi njala sindikanakuwuzani,
    pakuti dziko lonse ndi zonse zimene zili mʼmenemo ndi zanga.
13 Kodi ndimadya nyama ya ngʼombe zazimuna
    kapena kumwa magazi a mbuzi?
14 “Pereka nsembe zachiyamiko kwa Mulungu,
    kwaniritsa malonjezo ako kwa Wammwambamwamba.
15 Ndipo undiyitane pa tsiku lako la masautso;
    Ine ndidzakulanditsa, ndipo udzandilemekeza.”

16 Koma kwa woyipa, Mulungu akuti,

“Kodi uli ndi mphamvu yanji kuti uzinena malamulo anga
    kapena kutenga pangano langa pa milomo yako?
17 Iwe umadana ndi malangizo anga
    ndipo umaponyera kumbuyo kwako mawu anga.
18 Ukaona wakuba umamutsatira,
    umachita maere ako pamodzi ndi achigololo
19 Umagwiritsa ntchito pakamwa pako pa zinthu zoyipa
    ndipo umakonza lilime lako kuchita chinyengo.
20 Nthawi zonse umayankhula motsutsana ndi mʼbale wako
    ndipo umasinjirira mwana wa amayi ako enieni.
21 Wachita zimenezi ndipo Ine ndinali chete;
    umaganiza kuti ndine wofanana nawe
koma ndidzakudzudzula
    ndipo ndidzakutsutsa pamaso pako.

22 “Ganizira izi, iwe amene umayiwala Mulungu
    kuti ndingakukadzule popanda wokupulumutsa:
23 Iye amene amapereka nsembe yamayamiko amandilemekeza,
    ndipo amakonza njira zake kuti ndimuonetse
    chipulumutso cha Mulungu.”

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Pamene Mneneri Natani anabwera kwa iye atachita chigololo ndi Batiseba.

51 Mundichitire chifundo, Inu Mulungu,
    molingana ndi chikondi chanu chosasinthika;
molingana ndi chifundo chanu chachikulu
    mufafanize mphulupulu zanga.
Munditsuke zolakwa zanga zonse
    ndipo mundiyeretse kuchotsa tchimo langa.

Pakuti ndikudziwa mphulupulu zanga,
    ndipo tchimo langa lili pamaso panga nthawi zonse.
Motsutsana ndi Inu, Inu nokha, ndachimwa
    ndipo ndachita zoyipa pamaso panu,
Kotero kuti inu mwapezeka kuti ndinu wolungama
    pamene muyankhula ndi pamene muweruza.
Zoonadi ine ndinali wochimwa pomwe ndimabadwa,
    wochimwa kuyambira pa nthawi imene amayi anga anakhala woyembekezera ine.
Zoonadi inu mumafuna choonadi mu ziwalo zamʼkati mwanga;
    mumandiphunzitsa nzeru mʼkati mwanga mwenimweni.

Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera,
    munditsuke ndipo ndidzayera kuposa matalala
Mundilole ndimve chimwemwe ndi chisangalalo,
    mulole kuti mafupa amene mwawamphwanya akondwere.
Mufulatire machimo anga
    ndi kufafaniza zolakwa zanga zonse.

10 Mulenge mʼkati mwanga mtima woyera Inu Mulungu
    ndi kukonzanso mzimu wokhazikika mwa ine.
11 Musandichotse pamaso panu
    kapena kuchotsa Mzimu wanu Woyera mwa ine.
12 Bwezeretsani mwa ine chimwemwe cha chipulumutso chanu
    ndipo mundipatse mzimu wofuna kumvera kuti undilimbitse.

13 Pamenepo ndidzaphunzitsa anthu amphulupulu njira zanu
    kuti ochimwa adzabwerere kwa inu.
14 Mundipulumutse ku tchimo lokhetsa magazi, Inu Mulungu,
    Mulungu wa chipulumutso changa,
    ndipo lilime langa lidzayimba zachilungamo chanu.
15 Inu Ambuye tsekulani milomo yanga,
    ndipo pakamwa panga padzalengeza matamando anu.
16 Inu simusangalatsidwa ndi nsembe wamba.
    Ndikanapereka nsembe yopsereza, Inu simukondwera nayo.
17 Nsembe za Mulungu ndi mzimu wosweka;
    mtima wosweka ndi wachisoni
    Inu Mulungu simudzawunyoza.

18 Mwa kukoma mtima kwanu mupange Ziyoni kuti alemere;
    mumange makoma a Yerusalemu.
19 Kotero kudzakhala nsembe zachilungamo,
    nsembe yonse yopsereza yokondweretsa Inu;
    ndipo ngʼombe zazimuna zidzaperekedwa pa guwa lanu la nsembe.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe, ndakatulo ya Davide; pamene Doegi Mwedomu anapita kwa Sauli ndi kunena kuti “Davide wapita ku nyumba ya Ahimeleki.”

52 Nʼchifukwa chiyani ukudzitamandira ndi zoyipa, iwe munthu wamphamvu?
    Nʼchifukwa chiyani ukudzitamandira tsiku lonse,
    iwe munthu wochititsa manyazi pamaso pa Mulungu?
Tsiku lonse umakhalira kuganizira za kuwononga ena;
    lilime lako lili ngati lumo lakuthwa,
    ntchito yako nʼkunyenga.
Iwe umakonda choyipa mʼmalo mwa kuyankhula choonadi.
    Umakonda kunama kupambana kuyankhula zoona.
            Sela
Umakonda mawu onse opweteka,
    iwe lilime lachinyengo!

Zoonadi Mulungu adzakutsitsa kupita ku chiwonongeko chamuyaya:
    iye adzakukwatula ndi kukuchotsa mʼtenti yako;
    iye adzakuzula kuchoka mʼdziko la amoyo.
Olungama adzaona zimenezi ndi kuchita mantha;
    adzamuseka nʼkumanena kuti,
“Pano tsopano pali munthu
    amene sanayese Mulungu linga lake,
koma anakhulupirira chuma chake chambiri
    nalimbika kuchita zoyipa!”

Koma ine ndili ngati mtengo wa olivi
    wobiriwira bwino mʼnyumba ya Mulungu;
ndimadalira chikondi chosatha cha Mulungu
    kwa nthawi za nthawi.
Ine ndidzakutamandani kwamuyaya chifukwa cha zimene mwachita;
    chifukwa cha zimene mwachita; mʼdzina lanu ndidzayembekezera
    pakuti dzina lanulo ndi labwino. Ndidzakutamandani pamaso pa oyera mtima anu.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a Mahalati. Ndakatulo ya Davide.

53 Chitsiru chimati mu mtima mwake,
    “Kulibe Mulungu.”
Iwo ndi oyipa ndipo njira zawo ndi zonyansa;
    palibe ndi mmodzi yemwe amene amachita chabwino.

Mulungu kumwamba amayangʼana pansi pano
    pa ana a anthu
kuti aone ngati alipo wina wanzeru,
    wofunafuna Mulungu.
Aliyense wabwerera,
    iwo onse pamodzi akhala oyipa;
palibe ndi mmodzi yemwe amene amachita chabwino,
    ngakhale mmodzi.

Kodi anthu ochita zoyipawa adzaphunziradi;
    anthu amene amadya anthu anga monga mmene anthu amadyera buledi,
    ndipo sapemphera kwa Mulungu?
Iwo anali pamenepo atathedwa nzeru ndi mantha aakulu
    pamene panalibe kanthu kochititsa mantha.
Mulungu anamwazamwaza mafupa a anthu amene anakuthirani nkhondo;
    inuyo munawachititsa manyazi, pakuti Mulungu anawanyoza.

Ndithu, chipulumutso cha Israeli nʼchochokera ku Ziyoni!
    Pamene Mulungu adzabwezeretsanso ulemerero wa anthu ake,
    lolani Yakobo akondwere ndi Israeli asangalale!

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Ndakatulo ya Davide. Pamene anthu a ku Zifi anapita kwa Sauli ndipo anati, “Kodi Davide sakubisala pakati pathu.”

54 Pulumutseni Inu Mulungu, mwa dzina lanu;
    onetsani kuti ndine wosalakwa mwamphamvu yanu.
Imvani pemphero langa, Inu Mulungu
    mvetserani mawu a pakamwa panga.

Alendo akundithira nkhondo;
    anthu ankhanza akufunafuna moyo wanga,
    anthu amene salabadira za Mulungu.

Zoonadi Mulungu ndi thandizo langa;
    Ambuye ndiye amene amandichirikiza ine.

Lolani kuti choyipa chifike pa iwo amene amandichita chipongwe;
    mwa kukhulupirika kwanu awonongeni.

Ine ndidzapereka nsembe yaufulu kwa Inu;
    ndidzatamanda dzina lanu, Inu Yehova,
    pakuti ndi labwino.
Pakuti Iyeyo wandipulumutsa ku masautso anga onse,
    ndipo maso anga apenya kupambana kwa pa adani anga.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya Davide. Pa zoyimbira za zingwe.

55 Mvetserani pemphero langa, Inu Mulungu,
    musakufulatire kupempha kwanga,
    mverani ndipo mundiyankhe.
Maganizo anga akundisautsa ndipo ndathedwa nzeru
    chifukwa cha mawu a adani anga,
    chifukwa cha kupondereza kwa anthu oyipa;
pakuti andidzetsera masautso
    ndipo akundizunza mu mkwiyo wawo.

Mtima wanga ukupweteka mʼkati mwanga;
    mantha a imfa andigwera.
Mantha ndi kunjenjemera zandizinga;
    mantha aakulu andithetsa nzeru.
Ndinati, “Ndithu, ndikanakhala ndi mapiko ankhunda!
    Ndikanawulukira kutali ndi kukapuma.
Ndikanathawira kutali
    ndi kukakhala mʼchipululu.
Ndikanathamangira kumalo anga a chitetezo;
    kutali ndi mphepo yaukali ndi yamkuntho.”

Sokonezani maganizo a oyipa, Inu Ambuye, tsutsani mawu awo;
    pakuti ine ndikuona chiwawa ndi mkangano mu mzinda.
10 Usana ndi usiku iwo akuzungulirazungulira pa makoma ake;
    nkhwidzi ndi kuzunza kuli mʼkati mwake.
11 Mphamvu zowononga zili pa ntchito mu mzinda;
    kuopseza ndi mabodza sizichoka mʼmisewu yake.

12 Akanakhala mdani akundinyoza, ine
    ndikanapirira;
akanakhala mdani akudzikweza yekha kutsutsana nane,
    ndikanakabisala.
13 Koma iweyo mnzanga, mnzanga woyenda naye,
    bwenzi langa la pondaapanʼpondepo, ndi amene ukuchita zimenezi.
14 Mnzanga amene nthawi ina tinkasangalala
    pa chiyanjano chokoma ku nyumba ya Mulungu.

15 Mulole imfa itenge adani anga mwadzidzidzi;
    alowe mʼmanda ali amoyo
    pakuti choyipa chili pakati pawo.

16 Koma ine ndinafuwulira kwa Mulungu,
    ndipo Yehova anandipulumutsa.
17 Madzulo, mmawa ndi masana
    ndimalira mowawidwa mtima,
    ndipo Iye amamva mawu anga.
18 Iye amandiwombola ine osavulazidwa
    pa nkhondo imene yafika kulimbana nane,
    ngakhale kuti ndi ambiri amene akunditsutsa.
19 Mulungu amene ali pa mpando wake kwamuyaya,
    adzandimenyera nkhondo; adzawatsitsa adani anga,
chifukwa safuna kusintha njira zawo zoyipa
    ndipo saopa Mulungu.

20 Mnzanga woyenda naye wathira nkhondo abwenzi ake;
    iye akuphwanya pangano ake.
21 Mawu ake ndi osalala kuposa batala
    komabe nkhondo ili mu mtima mwake;
mawu ake ndi osalala kwambiri kuposa mafuta,
    komatu mawuwo ndi malupanga osololoka.

22 Tulani nkhawa zanu kwa Yehova
    ndipo Iye adzakulimbitsani;
    Iye sadzalola kuti wolungama agwe.
23 Koma Inu Mulungu mudzawatsitsa anthu oyipa
    kulowa mʼdzenje lachiwonongeko;
anthu okhetsa magazi ndi anthu achinyengo
    sadzakhala moyo theka la masiku awo,

koma ine ndimadalira Inu.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Njiwa pa Mtengo wa Thundu wa Kutali.” Mikitamu ya Davide, pamene Afilisti anamugwira ku Gati.

56 Mundichitire chifundo Inu Mulungu, pakuti anthu akundithamangitsa kwambiri;
    tsiku lonse akundithira nkhondo.
Ondinyoza akundithamangitsa tsiku lonse,
    ambiri akumenyana nane monyada.

Ndikachita mantha
    ndimadalira Inu.
Mwa Mulungu, amene mawu ake ine ndimatamanda,
    mwa Mulungu ine ndimadaliramo; sindidzachita mantha.
    Kodi munthu amene amafa angandichite chiyani?

Tsiku lonse amatembenuza mawu anga;
    nthawi zonse amakonza zondivulaza.
Iwo amakambirana, amandibisalira,
    amayangʼanitsitsa mayendedwe anga
    ndipo amakhala ndi chidwi chofuna kuchotsa moyo wanga.

Musalole konse kuti athawe;
    mu mkwiyo wanu Mulungu mugwetse mitundu ya anthu.
Mulembe za kulira kwanga,
    mulembe chiwerengero cha misozi yanga mʼbuku lanu.
    Kodi zimenezi sizinalembedwe mʼbuku lanulo?

Adani anga adzabwerera mʼmbuyo
    pamene ndidzalirira kwa Inu.
    Pamenepo ndidzadziwa kuti Mulungu ali ku mbali yanga.
10 Mwa Mulungu amene mawu ake ndimawatamanda,
    mwa Yehova amene mawu ake ndimawatamanda,
11 mwa Mulungu ine ndimadalira ndipo sindidzachita mantha.
    Kodi munthu angandichite chiyani?

12 Ndiyenera kuchita zomwe ndinalumbira kwa Mulungu;
    ndidzapereka nsembe zanga zachiyamiko kwa inu.
13 Pakuti mwawombola moyo wanga ku imfa
    ndi mapazi anga kuti ndingagwe,
kuti ndiyende pamaso pa Mulungu
    mʼkuwala kwa moyo.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Musawononge.” Ndakatulo ya Davide, pamene anathawa Sauli kupita ku phanga.

57 Mundichitire chifundo, Inu Mulungu mundichitire chifundo,
    pakuti mwa Inu moyo wanga umathawiramo.
Ndidzathawira mu mthunzi wa mapiko anu
    mpaka chiwonongeko chitapita.

Ine ndikufuwulira kwa Mulungu Wammwambamwamba,
    kwa Mulungu amene amakwaniritsa cholinga chake pa ine.
Mulungu amanditumizira kuchokera kumwamba ndi kundipulumutsa,
    kudzudzula iwo amene akundithamangitsa kwambiri.
    Mulungu amatumiza chikondi chake ndi kukhulupirika kwake.

Ine ndili pakati pa mikango,
    ndagona pakati pa zirombo zolusa;
anthu amene mano awo ndi milomo yawo ndi mivi,
    malilime awo ndi malupanga akuthwa.

Mukwezekedwe Inu Mulungu, kuposa mayiko onse akumwamba;
    mulole kuti ulemerero wanu ukhale pa dziko lonse lapansi.

Iwo anatchera mapazi anga ukonde
    ndipo ndinawerama pansi mosautsidwa.
Anakumba dzenje mʼnjira yanga
    koma agweramo okha mʼmenemo.

Mtima wanga ndi wokhazikika, Inu Mulungu
    mtima wanga ndi wokhazikika.
    Ndidzayimba nyimbo, nyimbo yake yamatamando.
Dzuka moyo wanga!
    Dzukani zeze ndi pangwe!
    Ndidzadzuka mʼbandakucha.

Ndidzakutamandani Ambuye, pakati pa mitundu ya anthu,
    ndidzayimba za Inu pakati pa mayiko.
10 Pakuti chikondi chanu nʼchachikulu, kufikira ku mayiko akumwamba;
    kukhulupirika kwanu kwafika ku mitambo.

11 Mukwezekedwe Inu Mulungu kuposa mayiko akumwamba,
    mulole kuti ulemerero wanu ukhale pa dziko lonse lapansi.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Musawononge.” Ndakatulo ya Davide.

58 Kodi inu olamulira mumayankhuladi molungama?
    Kodi mumaweruza mwachilungamo pakati pa anthu?
Ayi, mʼmitima mwanu mumakonzekera zosalungama,
    ndipo manja anu amatulutsa zachiwawa pa dziko lapansi.
Ngakhale kuchokera tsiku lawo lobadwa oyipa amasochera;
    kuchokera mʼmimba ya amayi awo, iwo ndi otayika ndipo amayankhula mabodza.
Ululu wawo uli ngati ululu wa njoka,
    ngati uja wa mphiri imene yatseka mʼmakutu mwake.
Imene simva liwu la munthu wamatsenga,
    ngakhale akhale wa luso lotani munthu wamatsengayo.

Gululani mano mʼkamwa mwawo, Inu Mulungu,
    Yehova khadzulani mano a mikango!
Mulole kuti asowe ngati madzi oyenda
    pamene iwo akoka uta mulole kuti mivi yawo ikhale yosathwa.
Akhale ngati nkhono imene imasungunuka pamene ikuyenda;
    ngati mwana wakufa asanabadwe, iwo asaone dzuwa.

Miphika yanu isanagwire moto waminga ya mkandankhuku,
    kaya iyo ndi yobiriwira kapena yowuma, oyipa adzachotsedwa.
10 Olungama adzasangalala poona kubwezera chilango,
    pamene adzasambitsa mapazi awo mʼmagazi a anthu oyipa.
11 Ndipo anthu adzanena kuti,
    “Zoonadi, olungama amalandirabe mphotho;
    zoonadi kuli Mulungu amene amaweruza dziko lapansi.”

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Musawononge.” Ndakatulo ya Davide. Pamene Sauli anatumiza anthu kuti akalondere nyumba ya Davide ndi cholinga choti amuphe.

59 Landitseni kwa adani anga, Inu Mulungu;
    munditeteze kwa anthu amene auka kutsutsana nane.
Landitseni kwa anthu ochita zoyipa
    ndipo mundipulumutse kwa anthu okhetsa magazi.

Onani momwe iwo akundibisalira!
    Anthu owopsa agwirizana zolimbana nane;
    osati chifukwa cha mlandu kapena tchimo langa, Inu Yehova.
Ine sindinachite cholakwa, koma iwo ndi okonzeka kundithira nkhondo.
    Dzukani kuti mundithandize; penyani mavuto anga!
Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli,
    dzidzutseni nokha kuti mulange anthu a mitundu ina yonse;
    musaonetse chifundo chanu kwa anthu oyipa achinyengowa.

Iwo amabweranso madzulo
    akuchita phokoso ngati agalu
    ndi kumangoyendayenda mu mzinda.
Onani zomwe amalavula mʼkamwa mwawo;
    iwo amalavula malupanga kuchokera pa milomo yawo,
    ndipo amanena kuti, “Ndani angatimve?”
Koma Inu Yehova, mumawaseka,
    mumayinyoza mitundu yonseyo.

Inu mphamvu yanga, ine ndiyangʼana kwa inu;
Inu Mulungu, ndinu linga langa. 10     Mulungu wanga wachikondi.

Mulungu adzapita patsogolo panga
    ndipo adzandilola kunyada pa iwo amene amandinyoza.
11 Koma musawaphe, Inu Ambuye chishango chathu,
    kuopa kuti anthu anga angayiwale.
Mwa mphamvu zanu,
    lolani kuti azingoyendayenda ndipo muwatsitse.
12 Chifukwa cha machimo a pakamwa pawo
    chifukwa cha mawu a milomo yawo,
    iwo akodwe mʼkunyada kwawo.
Chifukwa cha matemberero ndi mabodza amene ayankhula
13     muwawononge mu ukali (wanu)
    muwawononge mpaka atheretu.
Pamenepo zidzadziwika ku malekezero a dziko lapansi
    kuti Mulungu amalamulira Yakobo.

14 Iwo amabweranso madzulo,
    akuchita phokoso ngati agalu
    ndi kumangoyenda mu mzinda.
15 Iwo amayendayenda kufuna chakudya
    ndipo amawuwa ngati sanakhute.
16 Koma ine ndidzayimba za mphamvu yanu,
    mmawa ndidzayimba zachikondi chanu;
pakuti ndinu linga langa,
    pothawirapo panga mʼnthawi ya mavuto.

17 Inu mphamvu yanga, ndiyimba matamando kwa inu;
    Inu Mulungu, ndinu linga langa, Mulungu wanga wachikondi.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Kakombo wa Pangano.” Mikitamu ya Davide yophunzitsira. Pamene anamenyana ndi Mesopotamiya ndi Aramu-Zoba, ndi pamene Yowabu anabwerera ndi kukantha Aedomu 12,000 mʼChigwa cha Mchere.

60 Inu Mulungu mwatikanatu ife, ndipo mwatiwonongera otiteteza.
    Inu mwatikwiyira, tsopano tibwezeretseni mwakale!
Inu mwagwedeza dziko ndipo mwalingʼamba,
    konzani mingʼalu yake pakuti ikugwedezeka kwambiri.
Inu mwaonetsa anthu anu nthawi za mavuto;
    inu mwatipatsa vinyo amene watichititsa kudzandira.

Koma kwa iwo amene amaopa Inu, Inu mwakweza mbendera
    kuti tisonkhanireko pothawa uta.

Tipulumutseni ndi kutithandiza ndi dzanja lanu lamanja,
    kuti iwo amene mumawakonda apulumutsidwe.
Mulungu wayankhula kuchokera ku malo ake opatulika:
    “Mwakupambana ndidzagawa Sekemu
    ndipo ndidzayeza malire a chigwa cha Sukoti.
Giliyadi ndi wanga, Manase ndi wanganso;
    Efereimu ndi chipewa changa chodzitetezera,
    Yuda ndi ndodo yanga yaufumu
Mowabu ndi mbale yanga yosambira,
    pa Edomu ndidzaponyapo nsapato yanga,
    pa Filisitiya ndidzafuwula mwakupambana.”

Adzandifikitse ndani ku mzinda wotetezedwa?
    Ndani adzanditsogolera ku Edomu?
10 Kodi si Inu Mulungu, Inu amene mwatikana ife
    ndipo simutuluka pamodzi ndi magulu athu ankhondo.
11 Tipatseni chithandizo kuti tilimbane ndi mdani wathu,
    pakuti thandizo lochokera kwa munthu ndi lopanda phindu.
12 Chifukwa cha Mulungu, ife tidzapeza chipambano
    ndipo tidzapondaponda adani athu.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Loyimbidwa ndi zipangizo za zingwe.

61 Imvani kulira kwanga, Inu Mulungu;
    mvetserani pemphero langa.

Kuchokera ku malekezero a dziko lapansi ine ndimayitana Inu
    ndimayitana pomwe mtima wanga ukufowoka;
    tsogolereni ku thanthwe lalitali kuposa ineyo.
Pakuti Inu mwakhala pothawirapo panga,
    nsanja yolimba polimbana ndi adani anga.

Ine ndikulakalaka kukhala mʼtenti yanu kwamuyaya
    ndi kupeza chitetezo mu mthunzi wa mapiko anu.
Pakuti Inu Mulungu mwamva malumbiro anga;
    mwandipatsa cholowa cha iwo amene amaopa dzina lanu.

Wonjezerani masiku a moyo wa mfumu,
    zaka zake kwa mibado yochuluka.
Iye akhale pa mpando waufumu pamaso pa Mulungu kwamuyaya;
    ikani chikondi chanu ndi kukhulupirika kwanu kuti zimuteteze.

Kotero ndidzayimba matamando kwamuyaya pa dzina lanu
    ndi kukwaniritsa malumbiro anga tsiku ndi tsiku.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Kutsata mayimbidwe a Yedutuni. Salimo la Davide.

62 Moyo wanga umapeza mpumulo mwa Mulungu yekha;
    chipulumutso changa chimachokera kwa Iye.
Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa;
    Iye ndi linga langa, choncho sindidzagwedezeka.

Kodi nonsenu mudzalimbana naye munthu mpaka liti?
    Kodi mudzamugwetsa pansi ngati khoma losalimba,
    ngati mpanda wogwedezeka?
Iwo akufunitsitsa kumugwetsa
    kuti achoke pa malo ake apamwamba.
    Iwo amakondweretsedwa ndi mabodza.
Ndi pakamwa pawo amadalitsa
    koma mʼmitima yawo amatemberera.

Peza mpumulo mwa Mulungu yekhayo iwe moyo wanga;
    chiyembekezo changa chichokera mwa Iye.
Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa;
    Iyeyo ndi linga langa; sindidzagwedezeka.
Chipulumutso changa ndi ulemu wanga zimachokera kwa Mulungu:
    Iye ndiye thanthwe langa lamphamvu; Mulungu ndiye pothawira panga.
Dalirani Iye nthawi zonse, inu anthu;
    khuthulani mitima yanu kwa Iye,
    pakuti Mulungu ndiye pothawirapo pathu.
            Sela

Anthu wamba ndi mpweya chabe;
    anthu apamwamba ndi bodza chabe;
ngati atayezedwa pa sikelo iwo ndi chabe;
    iwowo pamodzi ndi mpweya ndi chabe
10 Musadalire kulanda mwachinyengo
    kapena katundu wobedwa;
ngakhale chuma chanu chichuluke,
    musayike mtima wanu pa icho.

11 Mulungu wayankhula kamodzi,
    ine ndamvapo zinthu ziwiri;
choyamba nʼchakuti Inu Mulungu ndinu wamphamvu,
12     komanso Inu Ambuye, chikondi chanu nʼchosasinthika.
Chachiwiri nʼchakuti mumamuchitira munthu
    molingana ndi ntchito zake.

Salimo la Davide. Pamene anali mʼchipululu cha Yuda.

63 Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga,
    moona mtima ine ndimakufunafunani;
moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Inu,
    thupi langa likulakalaka inu,
mʼdziko lowuma ndi lotopetsa
    kumene kulibe madzi.

Inu ndinakuonani ku malo anu opatulika
    ndipo ndinapenya mphamvu zanu ndi ulemerero wanu.
Chifukwa chikondi chanu
    ndi choposa moyo, milomo yanga idzakulemekezani.
Ndidzakutamandani masiku onse a moyo wanga,
    ndipo mʼdzina lanu ndidzakweza manja anga.
Mudzakhutitsa moyo wanga ndi zonona.
    Ine ndidzakutamandani ndi mawu anthetemya.

Pa bedi panga ndimakumbukira inu;
    ndimaganiza za Inu nthawi yonse ya usiku.
Chifukwa ndinu thandizo langa,
    ine ndimayimba mu mthunzi wa mapiko anu.
Moyo wanga umakangamira Inu;
    dzanja lanu lamanja limandigwiriziza.

Iwo amene akufunafuna moyo wanga adzawonongedwa;
    adzatsikira kunsi kozama kwa dziko lapansi.
10 Iwo adzaperekedwa ku lupanga
    ndi kukhala chakudya cha ankhandwe.

11 Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu;
    onse amene amalumbira mʼdzina la Mulungu adzalemekeza Mulunguyo,
    koma pakamwa pa anthu onama padzatsekedwa.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

64 Ndimvereni Mulungu pomwe ndikunena madandawulo anga;
    tetezani moyo wanga ku chiopsezo cha mdani.
Ndibiseni ku chiwembu cha anthu oyipa,
    ku gulu laphokoso la anthu ochita zoyipa.

Iwo amanola malilime awo ngati malupanga,
    amaponya mawu awo olasa ngati mivi.
Iwo amaponya mivi yawo ali pa malo wobisala kwa munthu wosalakwa;
    amamulasa modzidzimutsa ndi mopanda mantha.

Iwo amalimbikitsana wina ndi mnzake pa chikonzero chawo choyipa,
    amayankhula zobisa misampha yawo;
    ndipo amati, “Adzayiona ndani?”
Iwo amakonzekera zosalungama ndipo amati,
    “Takonza ndondomeko yabwino kwambiri!”
    Ndithu maganizo ndi mtima wa munthu ndi zachinyengo.

Koma Mulungu adzawalasa ndi mivi;
    mwadzidzidzi adzakanthidwa.
Iye adzatembenuza milomo yawoyo kuwatsutsa
    ndi kuwasandutsa bwinja;
    onse amene adzawaona adzagwedeza mitu yawo mowanyoza.

Anthu onse adzachita mantha;
    adzalengeza ntchito za Mulungu
    ndi kulingalira mozama zomwe Iye wazichita.
10 Lolani wolungama akondwere mwa Yehova
    ndi kubisala mwa Iye,
    owongoka mtima onse atamande Iye!

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Nyimbo.

65 Matamando akudikira Inu Mulungu mu Ziyoni;
    kwa inu malumbiro athu adzakwaniritsidwa.
Inu amene mumamva pemphero,
    kwa inu anthu onse adzafika.
Pamene tinathedwa nzeru ndi machimo,
    Inu munakhululukira mphulupulu zathu.
Odala iwo amene inu muwasankha
    ndi kuwabweretsa pafupi kukhala mʼmabwalo anu!
Ife tadzazidwa ndi zinthu zabwino za mʼNyumba mwanu,
    za mʼNyumba yanu yoyera.

Mumatiyankha ife ndi ntchito zodabwitsa zachilungamo,
    Inu Mulungu Mpulumutsi wathu,
chiyembekezo cha mathero onse a dziko lapansi
    ndi cha nyanja zomwe zili kutali kwambiri,
amene munapanga mapiri ndi mphamvu zanu,
    mutadziveka nokha ndi mphamvu.
Amene munakhalitsa bata nyanja
    kukokoma kwa mafunde ake,
    ndi phokoso la anthu a mitundu ina.
Iwo amene akukhala kutali amaopa zizindikiro zozizwitsa zanu;
    kumene dzuwa limatulukira ndi kumene dzuwa limalowera.
    Inu mumafuna nyimbo zachimwemwe.

Inu mumasamalira dziko lapansi ndi kulithirira;
    Inuyo mumalilemeretsa kwambiri.
Mtsinje wa Mulungu ndi wodzaza ndi madzi
    kuti upereke tirigu kwa anthu,
    pakuti Inu munakhazikitsa zimenezi.
10 Mwadzaza nthaka yake ndi madzi ndi kusalaza migula yake,
    mwayifewetsa ndi mvula yamawawa ndi kudalitsa mbewu zake.
11 Inu mumaveka chaka ndi zinthu zochuluka,
    ndipo ngolo zanu zimasefukira ndi zinthu zochuluka.
12 Malo a udzu a mʼchipululu amasefukira;
    mapiri avekedwa ndi chisangalalo.
13 Madambo akutidwa ndi zoweta
    ndi zigwa zavekedwa ndi tirigu;
    izo pamodzi zikufuwula ndi kuyimba mwachimwemwe.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo.

66 Fuwulani kwa Mulungu ndi chimwemwe, dziko lonse lapansi!
    Imbani ulemerero wa dzina lake;
    kumutamanda kwake kukhale kwaulemerero.
Nenani kwa Mulungu, “Ntchito zanu ndi zoopsa ndithu!
    Mphamvu yanu ndi yayikulu kwambiri
    kotero kuti adani anu amawerama pamaso panu.
Dziko lonse lapansi limaweramira inu;
    limayimba matamando kwa Inu;
    limayimba matamando pa dzina lanu.”
            Sela.

Bwerani mudzaone zimene Mulungu wachita,
    ntchito zanu ndi zoopsa ndithu pakati pa anthu.
Iye anasandutsa nyanja kukhala malo owuma,
    iwo anawoloka pa madzi ndi mapazi.
    Bwerani, tiyeni tikondwere mwa Iye.
Iye amalamulira ndi mphamvu zake mpaka muyaya,
    maso ake amayangʼanira anthu a mitundu ina.
    Anthu owukira asadzitukumule.

Tamandani Mulungu wathu, inu mitundu ya anthu,
    mulole kuti mawu a matamando ake amveke;
Iye watchinjiriza miyoyo yathu
    ndi kusunga mapazi athu kuti angaterereke.
10 Pakuti Inu Mulungu munatiyesa;
    munatiyenga ngati siliva.
11 Inu mwatilowetsa mʼndende
    ndi kutisenzetsa zolemera pa misana yathu.
12 Inu munalola kuti anthu akwere pa mitu yathu;
    ife tinadutsa mʼmoto ndi mʼmadzi,
    koma Inu munatibweretsa ku malo a zinthu zochuluka.

13 Ine ndidzabwera ku Nyumba yanu ndi nsembe zopsereza
    ndi kukwaniritsa malumbiro anga.
14 Malumbiro amene milomo yanga inalonjeza
    ndi pakamwa panga panayankhula pamene ndinali pa mavuto.
15 Ndidzapereka nsembe nyama zonenepa kwa Inu
    ndi chopereka cha nkhosa zazimuna;
    ndidzapereka ngʼombe zamphongo ndi mbuzi.
            Sela

16 Bwerani ndipo mudzamve inu nonse amene mumaopa Mulungu.
    Ndidzakuwuzani zimene Iyeyo wandichitira.
17 Ndinafuwula kwa Iye ndi pakamwa panga,
    matamando ake anali pa lilime panga.
18 Ndikanasekerera tchimo mu mtima mwanga
    Ambuye sakanamvera;
19 koma ndithu Mulungu wamvetsera
    ndipo watchera khutu ku mawu a kupempha kwanga.
20 Matamando akhale kwa Mulungu
    amene sanakane pemphero langa
    kapena kuletsa chikondi chake pa ine!

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Salimo.

67 Yehova atikomere mtima ndi kutidalitsa,
    achititse kuti nkhope yake itiwalire.
Kuti njira zanu zidziwike pa dziko lapansi,
    chipulumutso chanu pakati pa mitundu yonse.

Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu;
    mitundu yonse ya anthu ikutamandeni.
Mitundu yonse ya anthu isangalale ndi kuyimba mwachimwemwe,
    pakuti inu mumaweruza mitundu ya anthu mwachilungamo
    ndi kutsogolera mitundu ya anthu a dziko lapansi.
Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu;
    mitundu yonse ya anthu ikutamandeni.

Nthaka yabereka zokolola zake;
    tidalitseni Mulungu wathu.
Mulungu atidalitse
    kuti pamenepo malekezero onse a dziko lapansi apembedze Iyeyo.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

68 Adzuke Mulungu, adani ake amwazikane;
    adani ake athawe pamaso pake.
Monga momwe mphepo imachotsera utsi; Inu muwawulutsire kutali.
    Monga phula limasungunukira pa moto,
    oyipa awonongeke pamaso pa Mulungu.
Koma olungama asangalale
    ndi kukondwera pamaso pa Mulungu;
    iwo akondwere ndi kusangalala.

Imbirani Mulungu imbirani dzina lake matamando,
    mukwezeni Iye amene amakwera pa mitambo;
    dzina lake ndi Yehova ndipo sangalalani pamaso pake.
Atate wa ana amasiye, mtetezi wa akazi amasiye,
    ndiye Mulungu amene amakhala mʼmalo oyera.
Mulungu amakhazikitsa mtima pansi osungulumwa mʼmabanja,
    amatsogolera amʼndende ndi kuyimba;
    koma anthu osamvera amakhala ku malo owuma a dziko lapansi.

Pamene munatuluka kutsogolera anthu anu, Inu Mulungu,
    pamene munayenda kudutsa chipululu,
dziko lapansi linagwedezeka, miyamba inakhuthula pansi mvula,
    pamaso pa Mulungu, Mmodzi uja wa ku Sinai.
    Pamaso pa Mulungu, Mulungu wa Israeli.
Munapereka mivumbi yochuluka, Inu Mulungu;
    munatsitsimutsa cholowa chanu cholefuka.
10 Anthu anu anakhala mʼmenemo
    ndipo munapatsa anthu osauka zimene zinkawasowa chifukwa cha ubwino wanu Mulungu.

11 Ambuye analengeza mawu,
    ndipo gulu linali lalikulu la iwo amene anapita kukawafalitsa;
12 “Mafumu ndi ankhondo anathawa mwaliwiro;
    mʼmisasa anthu anagawana zolanda pa nkhondo.
13 Ngakhale mukugona pakati pa makola a ziweto,
    mapiko a nkhunda akutidwa ndi siliva,
    nthenga zake ndi golide wonyezimira.”
14 Pamene Wamphamvuzonse anabalalitsa mafumu mʼdziko,
    zinali ngati matalala akugwa pa Zalimoni.

15 Mapiri a Basani ndi mapiri aulemerero;
    mapiri a Basani, ndi mapiri a msonga zambiri.
16 Muyangʼaniranji mwansanje inu mapiri a msonga zambiri,
    pa phiri limene Mulungu analisankha kuti azilamulira,
    kumene Yehova mwini adzakhalako kwamuyaya?
17 Magaleta a Mulungu ndi osawerengeka,
    ndi miyandamiyanda;
    Ambuye wabwera kuchokera ku Sinai, walowa mʼmalo ake opatulika.
18 Pamene Inu munakwera mmwamba,
    munatsogolera a mʼndende ambiri;
    munalandira mphatso kuchokera kwa anthu,
ngakhale kuchokera kwa owukira,
    kuti Inu Mulungu, mukhale kumeneko.

19 Matamando akhale kwa Ambuye, kwa Mulungu Mpulumutsi wathu
    amene tsiku ndi tsiku amasenza zolemetsa zathu.
20 Mulungu wathu ndi Mulungu amene amapulumutsa;
    Ambuye Wamphamvuzonse ndiye amene amatipulumutsa ku imfa.

21 Ndithu Mulungu adzaphwanya mitu ya adani ake,
    zipewa za ubweya za iwo amene amapitiriza kuchita machimo awo.
22 Ambuye akunena kuti, “Ndidzawabweretsa kuchokera ku Basani;
    ndidzawabweretsa kuchokera ku nyanja zozama.
23 Kuti muviyike mapazi anu mʼmagazi a adani anu,
    pamene malilime a agalu anu akudyapo gawo lawo.”

24 Mayendedwe aulemu a anthu anu aonekera poyera, Inu Mulungu;
    mayendedwe olemekeza Mulungu wanga ndi Mfumu yanga yokalowa mʼmalo opatulika.
25 Patsogolo pali oyimba nyimbo pakamwa, pambuyo pawo oyimba nyimbo ndi zipangizo;
    pamodzi ndi iwo pali atsikana akuyimba matambolini.
26 Tamandani Mulungu mu msonkhano waukulu;
    tamandani Yehova mu msonkhano wa Israeli.
27 Pali fuko lalingʼono la Benjamini, kuwatsogolera,
    pali gulu lalikulu la ana a mafumu a Yuda,
    ndiponso pali ana a mafumu a Zebuloni ndi Nafutali.

28 Kungani mphamvu zanu Mulungu;
    tionetseni nyonga zanu, Inu Mulungu, monga munachitira poyamba.
29 Chifukwa cha Nyumba yanu ku Yerusalemu,
    mafumu adzabweretsa kwa Inu mphatso.
30 Dzudzulani chirombo pakati pa mabango,
    gulu la ngʼombe zazimuna pakati pa ana angʼombe a mitundu ya anthu.
Mochititsidwa manyazi, abweretse mitanda ya siliva.
    Balalitsani anthu a mitundu ina amene amasangalatsidwa ndi nkhondo.
31 Nthumwi zidzachokera ku Igupto;
    Kusi adzadzipereka yekha kwa Mulungu.

32 Imbirani Mulungu Inu mafumu a dziko lapansi
    imbirani Ambuye matamando.
            Sela
33 Kwa Iye amene amakwera pa mitambo yakalekale ya mmwamba
    amene amabangula ndi mawu amphamvu.
34 Lengezani za mphamvu za Mulungu,
    amene ulemerero wake uli pa Israeli
    amene mphamvu zake zili mʼmitambo.
35 Ndinu woopsa, Inu Mulungu mʼmalo anu opatulika;
    Mulungu wa Israeli amapereka mphamvu ndi nyonga kwa anthu ake.

Matamando akhale kwa Mulungu!

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Potsata mayimbidwe a “Akakombo.”

69 Pulumutseni Inu Mulungu,
    pakuti madzi afika mʼkhosi
Ine ndikumira mʼthope lozama
    mʼmene mulibe popondapo.
Ndalowa mʼmadzi ozama;
    mafunde andimiza.
Ndafowoka ndikupempha chithandizo;
    kummero kwanga kwawuma gwaa,
mʼmaso mwanga mwada
    kuyembekezera Mulungu wanga.
Iwo amene amadana nane popanda chifukwa
    ndi ochuluka kuposa tsitsi la kumutu kwanga;
ambiri ndi adani anga popanda chifukwa,
    iwo amene akufunafuna kundiwononga.
Ndikukakamizidwa kubwezera
    zomwe sindinabe.

Mukudziwa uchitsiru wanga, Inu Mulungu,
    kulakwa kwanga sikuli kobisika kwa Inu.

Iwo amene amadalira Inu
    asanyozedwe chifukwa cha ine,
    Inu Ambuye Wamphamvuzonse.
Iwo amene amafunafuna Inu
    asachititsidwe manyazi chifukwa cha ine,
    Inu Mulungu wa Israeli.
Pakuti ndimapirira kunyozedwa chifukwa cha Inu,
    ndipo manyazi amaphimba nkhope yanga.
Ndine mlendo kwa abale anga,
    munthu wakudza kwa ana aamuna a amayi anga;
pakuti changu chochitira nyumba yanu chandiphetsa
    ndipo chipongwe cha iwo amene amanyoza Inu chandigwera.
10 Pamene ndikulira ndi kusala kudya,
    ndiyenera kupirira kunyozedwa;
11 pomwe ndavala chiguduli,
    anthu amandiseweretsa.
12 Iwo amene amakhala pa chipata amandinena,
    ndipo ine ndine nyimbo ya zidakwa.

13 Koma ndikupempha kwa Inu Ambuye,
    pa nthawi yanu yondikomera mtima;
mwa chikondi chanu chachikulu
    Inu Mulungu, mundiyankhe pondipulumutsa.
14 Mundilanditse kuchoka mʼmatope,
    musalole kuti ndimire,
pulumutseni ine kwa iwo
    amene amadana nane, kuchoka mʼmadzi ozama.
15 Musalole kuti chigumula chindimeze,
    kuya kusandimeze
    ndipo dzenje lisatseke pakamwa pake kundimiza.
16 Ndiyankheni Inu Yehova mwa ubwino wanu wa chikondi chanu;
    mwa chifundo chanu chachikulu tembenukirani kwa ine.
17 Musabisire nkhope yanu mtumiki wanu,
    ndiyankheni msanga, pakuti ndili pa mavuto.
18 Bwerani pafupi ndi kundilanditsa;
    ndiwomboleni chifukwa cha adani anga.

19 Inu mukudziwa momwe ndanyozedwera,
    kunyozedwa ndi kuchititsidwa manyazi; adani anga onse ali pamaso panu.
20 Mnyozo waswa mtima wanga
    ndipo wandisiya wopanda thandizo lililonse;
ndinafunafuna ena woti andichitire chisoni,
    koma panalibe ndi mmodzi yemwe woti anditonthoze, sindinapeze ndi mmodzi yemwe.
21 Iwo anayika ndulu mʼchakudya changa
    ndi kundipatsa vinyo wosasa chifukwa cha ludzu.

22 Chakudya chomwe chayikidwa patsogolo pawo chikhale msampha;
    chikhale chobwezera chilango ndiponso khwekhwe.
23 Maso awo adetsedwe kotero kuti asaonenso
    ndipo misana yawo ipindike mpaka kalekale.
24 Khuthulirani ukali wanu pa iwo;
    mkwiyo wanu woyaka moto uwathe mphamvu.
25 Malo awo akhale wopanda anthu
    pasapezeke ndi mmodzi yemwe wokhala mʼmatenti awo.
26 Pakuti iwo amazunza amene inu munamuvulaza
    ndi kuyankhula zowawa kwa amene munawapweteka.
27 Awonjezereni kulakwa pa kulakwa kwawo,
    musalole kuti akhale ndi gawo pa chipulumutso chanu.
28 Iwo afufutidwe mʼbuku la amoyo
    ndipo asalembedwe pamodzi ndi olungama.

29 Ndikumva zowawa ndi kuzunzika;
    lolani chipulumutso chanu, Inu Mulungu, chinditeteze.

30 Ine ndidzatamanda dzina la Mulungu mʼnyimbo,
    ndidzalemekeza Iye ndi chiyamiko.
31 Izi zidzakondweretsa Yehova kupambana ngʼombe,
    kupambananso ngʼombe yayimuna, pamodzi ndi nyanga ndi ziboda zake.
32 Wosauka adzaona ndipo adzasangalala,
    Inu amene mumafunafuna Mulungu, mitima yanu ikhale ndi moyo!
33 Yehova amamvera anthu osowa
    ndipo sanyoza anthu ake omangidwa.

34 Kumwamba ndi dziko lapansi zitamanda Iye,
    nyanja ndi zonse zomwe zimayenda mʼmenemo,
35 pakuti Mulungu adzapulumutsa Ziyoni
    ndi kumanganso mizinda ya Yuda,
anthu adzakhala kumeneko ndipo dzikolo lidzakhala lawo;
36     ana atumiki ake adzalitenga kukhala cholowa chawo,
    ndipo iwo amene amakonda dzina lake adzakhala kumeneko.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Pempho.

70 Fulumirani Mulungu kundipulumutsa;
    Yehova bwerani msanga kudzandithandiza.
Iwo amene akufunafuna moyo wanga
    achititsidwe manyazi ndi kusokonezedwa;
onse amene akukhumba chiwonongeko changa
    abwezedwe mopanda ulemu.
Onse amene akunena kwa ine kuti, “Aha, aha,”
    abwerere chifukwa cha manyazi awo.
Koma onse amene akufunafuna Inu
    akondwere ndi kusangalala mwa Inu;
iwo amene amakonda chipulumutso chanu
    nthawi zonse anene kuti, “Mulungu akuzike!”

Koma ine ndine wosauka ndi wosowa;
    bwerani msanga kwa ine Inu Mulungu.
Inu ndinu thandizo langa ndi momboli wanga;
    Inu Yehova musachedwe.
71 Mwa Inu Yehova ine ndathawiramo;
    musalole kuti ndichititsidwe manyazi.
Mundilanditse ndi kundipulumutsa mwa chilungamo chanu,
    mutchere khutu lanu ndi kundipulumutsa.
Mukhale thanthwe langa lothawirapo,
    kumene ine nditha kupita nthawi zonse;
lamulani kuti ndipulumuke,
    pakuti Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa.
Landitseni Inu Mulungu wanga, kuchoka mʼdzanja la oyipa,
    kuchoka mʼdzanja la oyipa ndi anthu ankhanza.

Pakuti Inu mwakhala chiyembekezo changa, Inu Ambuye Wamphamvuzonse,
    chilimbikitso changa kuyambira ndili mwana.
Kuyambira pamene ndinabadwa, ndakhala ndikudalira Inu;
    Inu munanditulutsa mʼmimba mwa amayi anga,
    ndipo ndidzakupembedzani nthawi zonse.
Ine ndakhala chinthu chodabwitsa kwa anthu ambiri
    koma Inu ndinu wonditchinjiriza wamphamvu.
Pakamwa panga padzaza ndi matamando anu,
    kulengeza ulemerero wanu tsiku lonse.

Musanditaye pamene ndakalamba;
    musandisiye pamene mphamvu zanga zatha.
10 Pakuti adani anga ayankhula motsutsana nane;
    iwo amene amadikira kuti andiphe amapangana pamodzi.
11 Iwo amati, “Mulungu wamusiya;
    mutsatireni ndi kumugwira,
    pakuti palibe amene adzamupulumutse.”
12 Musakhale kutali ndi ine Inu Mulungu,
    bwerani msanga, Inu Mulungu wanga; thandizeni.
13 Ondineneza anga awonongeke mwa manyazi,
    iwo amene akufuna kundipweteka
    avale chitonzo ndi manyazi.

14 Koma ine ndidzakhala ndi chiyembekezo mwa Inu nthawi zonse,
    ndidzakutamandani mowirikizawirikiza.
15 Pakamwa panga padzafotokoza za chilungamo chanu,
    za chipulumutso chanu tsiku lonse,
    ngakhale sindikudziwa muyeso wake.
16 Ndidzabwera ndi kulengeza za machitidwe amphamvu zanu Inu Ambuye Wamphamvuzonse.
    Ndidzalengeza chilungamo chanu, chanu chokha.
17 Kuyambira ubwana wanga, Inu Mulungu mwakhala mukundiphunzitsa,
    ndipo mpaka lero ine ndikulengeza za ntchito zanu zodabwitsa
18 Ngakhale pamene ndakalamba ndipo imvi zili mbuu
    musanditaye Inu Mulungu,
mpaka nditalengeza mphamvu zanu
    kwa mibado yonse yakutsogolo.

19 Mphamvu zanu ndi kulungama kwanu zimafika mpaka kumwambamwamba.
    Ndani wofanana nanu Inu Mulungu,
    amene mwachita zazikulu?
20 Ngakhale mwandionetsa mavuto
    ambiri owawa,
mudzabwezeretsanso moyo wanga;
    kuchokera kunsi kwa dziko lapansi,
    mudzandiukitsanso.
21 Inu mudzachulukitsa ulemu wanga
    ndi kunditonthozanso.

22 Ndidzakutamandani ndi zeze
    chifukwa cha kukhulupirika kwanu Mulungu,
ndidzayimba matamando kwa Inu ndi pangwe,
    Inu Woyera wa Israeli.
23 Milomo yanga idzafuwula ndi chimwemwe
    pamene ndidzayimba matamando kwa Inu
    amene mwandiwombola.
24 Lilime langa lidzafotokoza za ntchito zanu zachilungamo
    tsiku lonse,
pakuti iwo amene amafuna kundipweteka
    achititsidwa manyazi ndi kusokonezedwa.

Salimo la Solomoni.

72 Patsani mwana wa mfumu nzeru zanu zoweruzira mwa chilungamo,
    Inu Mulungu mupatseni mwana wa mfumu chilungamo chanu.
Iye adzaweruza anthu anu mwachilungamo,
    anthu anu ozunzika mosakondera.
Mapiri adzabweretsa chuma kwa anthu anu,
    timapiri tidzabweretsa zipatso zachilungamo.
Iye adzateteza ozunzika pakati pa anthu
    ndi kupulumutsa ana a anthu osowa;
    adzaphwanya ozunza anzawo.

Adzakhala ndi moyo pa mibado yonse,
    nthawi zonse pamene dzuwa ndi mwezi zikuwala.
Iye adzakhala kugwa kwa mvula pa minda yolimidwa
    ngati mivumbi yothirira dziko lapansi.
Mʼmasiku a munthu wolungama adzakhazikika;
    chuma chidzachuluka mpaka mwezi utaleka kuwala.

Iye adzalamulira kuchokera ku nyanja ina mpaka ku nyanja ina
    ndiponso kuchokera ku mtsinje mpaka ku malekezero a dziko lapansi.
Mafuko a mʼchipululu adzawerama pamaso pake
    ndipo adani ake adzanyambita fumbi.
10 Mafumu a ku Tarisisi ndi a ku zilumba zakutali
    adzabweretsa mitulo kwa iye,
mafumu a ku Seba ndi Seba
    adzapereka mphatso kwa iyeyo.
11 Mafumu onse adzamuweramira
    ndipo mitundu yonse idzamutumikira.

12 Pakuti iye adzawombola wosowa amene akulira,
    wozunzika amene alibe wina womuthandiza.
13 Iye adzachitira chifundo anthu ofowoka ndi anthu osowa
    ndi kupulumutsa osowa ku imfa.
14 Iye adzalanditsa iwo ku mazunzo ndi chiwawa
    pakuti magazi awo ndi amtengo wapatali pamaso pake.

15 Iye akhale ndi moyo wautali;
    golide ochokera ku Seba apatsidwe kwa iye.
Anthu amupempherere nthawi zonse
    ndi kumudalitsa tsiku lonse.
16 Mulole kuti tirigu achuluke mʼdziko lonse;
    pamwamba pa mapiri pakhale tirigu.
Zipatso zake zichuluke ngati za ku Lebanoni;
    zichuluke ngati udzu wakuthengo
17 Dzina lake likhazikike kwamuyaya,
    lipitirire kukhala monga momwe limakhalira dzuwa.

Mitundu yonse idzadalitsika kudzera mwa iye
    ndipo iwo adzamutcha iye wodala.

18 Matamando akhale kwa Yehova Mulungu, Mulungu wa Israeli
    amene Iye yekha amachita ntchito zodabwitsa.
19 Matamando akhale ku dzina lake laulemerero kwamuyaya
    dziko lonse lapansi lidzaze ndi ulemerero wake.
            Ameni ndi Ameni.

20 Uku ndiko kumaliza kwa mapemphero a Davide mwana wa Yese.